Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Yehova Amapulumutsa Anthu Odzimvera Chisoni

Yehova Amapulumutsa Anthu Odzimvera Chisoni

Nthawi zina, tonsefe timakhumudwa. Koma kukhumudwa sikutanthauza kuti tayamba kufooka mwauzimu. Ndipotu ngakhale Yehova, nthawi zina amakhumudwa. (Ge 6:​5, 6) Koma bwanji ngati timakhala okhumudwa kwambiri nthawi zina kapenanso nthawi zonse?

Muzipemphera kwa Yehova kuti akuthandizeni. Yehova amachita chidwi ndi zimene tikuganiza komanso mmene tikumvera mumtima. Amadziwa ngati tikusangalala kapena ngati takhumudwa. Amamvetsa zimene zimatichititsa kuti tiziganiza kapena kumva mmene tikumvera. (Sl 7:9b) Koma chosangalatsa kwambiri n’chakuti, Yehova amatidera nkhawa ndipo angatithandize pamene takhumudwa kapena pamene tikudwala matenda ovutika maganizo.—Sl 34:18.

Muziteteza maganizo anu. Kukhala ndi maganizo olakwika kungachititse kuti tisamasangalale komanso kungasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova. Choncho tiyenera kumateteza mtima wathu kapena kuti umunthu wathu wamkati kuphatikizapo mmene timaganizira komanso mmene timamvera.—Miy 4:23.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MMENE ABALE ATHU AKUKHALIRA MWAMTENDERE NGAKHALE KUTI AKUVUTIKA MAGANIZO, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi Nikki anachita chiyani kuti apirire pamene ankavutika maganizo?

  • N’chifukwa chiyani Nikki anaona kuti akufunika thandizo lachipatala?—Mt 9:12

  • Kodi Nikki anasonyeza kuti amadalira Yehova m’njira ziti?