Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Chikondi Chokhulupirika cha Mulungu Chimatiteteza ku Mabodza a Satana

Chikondi Chokhulupirika cha Mulungu Chimatiteteza ku Mabodza a Satana

Satana amafuna kuti anthu azikhulupirira kuti Yehova ndi amene amachititsa zinthu zoipa (Yob 8:4)

Amafunanso kuti tiziganiza kuti Yehova sizimamukhudza ngati tili okhulupirika kapena ayi (Yob 9:​20-22; w15 7/1 12 ¶3)

Chikondi chokhulupirika cha Yehova chimatithandiza kuti tisamapusitsike ndi mabodza a Satana komanso kuti tikhalabe wokhulupirika (Yob 10:12; Sl 32:​7, 10; w21.11 6 ¶14)

TAYESANI IZI: Kuti mulimbitse chikhulupiriro chanu, muzifufuza mmene Yehova akukusonyezerani chikondi chokhulupirika, muzilemba zomwe mwapezazo ndipo muziziwerenga mobwerezabwereza.