Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Abusa Amene Amachitira Zabwino Anthu a Yehova

Abusa Amene Amachitira Zabwino Anthu a Yehova

Anthu ambiri amaona molakwika anthu amene ali ndi udindo. Chifukwa chiyani? Chifukwa kuyambira kalekale, anthu akhala akugwiritsa ntchito udindo pofuna kudzipindulitsa okha. (Mik 7:3) Koma timayamikira kwambiri kuti akulu amaphunzitsidwa kuti azigwiritsa ntchito udindo wawo pochitira zabwino anthu a Yehova.—Est 10:3; Mt 20:​25, 26.

Mosiyana ndi anthu audindo a m’dzikoli, akulu amagwira bwino ntchito yawo yoyang’anira chifukwa amakonda Yehova ndi anthu ake. (Yoh 21:16; 1Pe 5:​1-3) Motsogoleredwa ndi Yesu, abusawa amathandiza wofalitsa aliyense kuti azikhala womasuka mumpingo wa Chikhristu ndi kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Amakhala okonzeka kupereka thandizo lauzimu kwa nkhosa za Yehova, amathandiza wofalitsa akadwala mwadzidzidzi komanso amathandiza kukachitika ngozi zam’chilengedwe kapena zoyambitsidwa ndi anthu. Ngati mukufunikira thandizo, lankhulani ndi akulu a mumpingo mwanu ndipo adzakuthandizani.—Yak 5:14.

ONERANI VIDIYO YAKUTI ABUSA AMENE AMASAMALIRA GULU LA NKHOSA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi thandizo lomwe akulu anapereka kwa Mariana linamulimbikitsa bwanji?

  • Kodi thandizo lomwe akulu anapereka kwa Elias linamulimbikitsa bwanji?

  • Kodi zimene mwaona muvidiyoyi, zakhudza bwanji mmene mumaonera ntchito imene akulu amagwira?