October 28–November 3
MASALIMO 103-104
Nyimbo Na. 30 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. “Amakumbukira Kuti Ndife Fumbi”
(10 min.)
Chifundo chachikulu cha Yehova chimamuchititsa kukhala wololera (Sl 103:8; w23.07 21 ¶5)
Iye satitaya tikalakwitsa zinazake (Sl 103:9, 10; w23.09 6-7 ¶16-18)
Sayembekezera kuti tizichita zimene sitingathe (Sl 103:14; w23.05 26 ¶2)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi zimene ndimachitira anthu ena zimasonyeza kuti ndine wololera mofanana ndi Yehova?’
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
-
Sl 104:24—Kodi vesili likutiphunzitsa chiyani zokhudza luso la Yehova lolenga zinthu? (cl 55 ¶18)
-
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Sl 104:1-24 (th phunziro 11)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. (lmd phunziro 3 mfundo 4)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Kambiranani vidiyo yakuti Sangalalani Pophunzira Baibulo ndi munthu amene anavomera kuphunzira Baibulo. (th phunziro 9)
6. Nkhani
(5 min.) lmd zakumapeto A mfundo 6—Mutu: Mwamuna Ayenera ‘Kukonda Mkazi Wake Ngati Mmene Amadzikondera Yekha.’ (th phunziro 1)
Nyimbo Na. 44
7. Kodi Mumadziwa Zimene Simungakwanitse Kuchita?
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Yehova amasangalala tikamachita zonse zomwe tingathe pomutumikira, komanso ifeyo timasangalala. (Sl 73:28) Komabe ndi bwino kuti tikamachita zonse zomwe tingathe, tiziganiziranso zomwe sitingakwanitse kuchita. Zimenezi zingatithandize kuti tisamakhale ndi nkhawa komanso tisamakhumudwe.
Onerani VIDIYO yakuti Tingachite Zambiri Potumikira Yehova Tikamachita Zomwe Tingakwanitse. Kenako funsani mafunso awa:
-
Kodi Yehova amayembekezera kuti tizichita chiyani? (Mik 6:8)
-
N’chiyani chinathandiza mlongoyu kuti asamadere nkhawa kwambiri za mmene angakwaniritsire cholinga chake?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 17 ¶8-12, bokosi patsamba 137