October 7-13
MASALIMO 92-95
Nyimbo Na. 84 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Kutumikira Yehova Ndi Kwabwino Kwambiri
(10 min.)
Yehova amafuna kuti tizimulambira (Sl 92:1, 4; w18.04 26 ¶5)
Iye amathandiza anthu ake kuti azisankha okha zochita zomwe anthuwo angamasangalale nazo (Sl 92:5; w18.11 20 ¶8)
Iye amasangalala ndi anthu amene amamutumikira ngakhale pamene akalamba (Sl 92:12-15; w20.01 19 ¶18)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi n’chiyani chikundilepheretsa kudzipereka kwa Yehova komanso kubatizidwa?’
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
-
Sl 92:5—Kodi mawu a palembali akufotokoza bwanji nzeru za Yehova? (cl 176 ¶18)
-
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Sl 94:1-23 (th phunziro 5)
4. Ulendo Woyamba
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Pamene mukucheza ndi munthuyo, pezani mpata woti mumufotokozere zoti mumaphunzira Baibulo ndi anthu. (lmd phunziro 5 mfundo 3)
5. Ulendo Wobwereza
(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Pemphani munthu amene anakanapo kuphunzira Baibulo m’mbuyomu kuti muziphunzira naye. (lmd phunziro 8 mfundo 4)
6. Kuphunzitsa Anthu
(5 min.) Kambiranani ndi wophunzira amene sakupita patsogolo. (lmd phunziro 12 mfundo 5)
Nyimbo Na. 5
7. Kodi Achinyamata Angatani Akapanikizika ndi Nkhawa?
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Anthu amene amatumikira Yehova nawonso amakhala ndi nkhawa. Mwachitsanzo, Davide nthawi zina ankakhala ndi nkhawa pa moyo wake ndipo ndi mmene zililinso ndi abale ndi alongo athu ambiri masiku ano. (Sl 13:2; 139:23) N’zomvetsa chisoni kuti ngakhale achinyamata nawonso amakhala ndi nkhawa. Nthawi zina, nkhawa zingachititse munthu kuona kuti zinthu zimene amachita nthawi zonse monga kupita ku sukulu kapena kumisonkhano, kukhala zopanikiza. Ena angafike mpaka povutika maganizo kapena kufuna kudzipha.
Achinyamata, mukaona kuti mwapanikizika ndi nkhawa muziuza makolo anu kapena munthu wina wamkulu. Komanso musamaiwale kuuza Yehova m’pemphero kuti akuthandizeni. (Afi 4:6) Iye adzakuthandizani. (Sl 94:17-19; Yes 41:10) Taganizirani chitsanzo cha Steing.
Onerani VIDIYO yakuti Yehova Anandisamalira. Kenako funsani mafunso awa:
• Kodi ndi vesi la m’Baibulo liti limene linathandiza Steing, nanga linamuthandiza bwanji?
• Kodi Yehova anamusamalira bwanji?
Makolo, mungathandize ana anu kuthana ndi nkhawa powamvetsera moleza mtima, kuwasonyeza kuti mumawakonda komanso kuwathandiza kuti azikhulupirira kuti Yehova amawakonda. (Tit 2:4; Yak 1:19) Muzidalira Yehova kuti akulimbikitseni komanso akupatseni mphamvu zomwe mungafunikire kuti muthandize ana anu.
Sitingadziwe ngati wina mumpingo akulimbana ndi nkhawa kapena kumvetsa mmene akumvera. Komabe tingathandize poyesetsa kukonda aliyense mumpingo komanso kuchititsa aliyense kuti azidziona kuti ndi wofunika.—Miy 12:25; Ahe 10:24.
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 16 ¶6-9, bokosi patsamba 132