Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

September 16-22

MASALIMO 85-87

September 16-22

Nyimbo Na. 41 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Pemphero Limatithandiza Kupirira

(10 min.)

Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala wosangalala (Sl 86:4)

Muzipempha Yehova kuti akuthandizeni kukhalabe wokhulupirika (Sl 86:​11, 12; w12 5/15 25 ¶10)

Muzikhulupirira kuti Yehova ayankha mapemphero anu (Sl 86:​6, 7; w23.05 13 ¶17-18)


DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndimawonjezera nthawi imene ndimakhala ndikupemphera ndikakumana ndi mayesero?’—Sl 86:3.

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 86:11—Kodi pemphero la Davideli limatiuza chiyani zokhudza mtima wa munthu? (it-1 1058 ¶5)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 3 mfundo 5)

5. Ulendo Wobwereza

(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Pemphani kuti muziphunzira Baibulo ndi munthu amene m’mbuyomu anakufotokozerani kuti akuda nkhawa ndi zinthu zimene zinali zitangochitika kumene. (lmd phunziro 7 mfundo 4)

6. Kuphunzitsa Anthu

(5 min.) lff phunziro 15 mfundo 5. Konzani zoti wophunzira wanuyo adzaphunzire mlungu wotsatira ngakhale kuti inu mukuchokapo. (lmd phunziro 10 mfundo 4)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 83

7. Musafooke

(5 min.) Nkhani yokambirana.

Onerani VIDIYO. Kenako funsani mafunso awa:

  • N’chifukwa chiyani nthawi zina timafooka tikakhala mu utumiki?

  • N’chifukwa chiyani sitiyenera kufooka?

8. Pitirizani Kuyambitsa Maphunziro a Baibulo

(10 min.) Nkhani yokambirana.

Kodi mwayambitsako phunziro la Baibulo pogwiritsa ntchito kabuku kakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, pa ntchito yapadera imene tikugwira mwezi uno? Ngati ndi choncho, muyenera kuti mukusangalala kwambiri. Ndipo sitikukayikira kuti anthu ena akulimbikitsidwa ndi zimene mwachitazi. Komabe ngati simunayambitse phunziro la Baibulo mukhoza kuyamba kudzifunsa ngati khama limene mukuchita likuthandizadi. Kodi mungatani ngati mwafooka chifukwa choti simunayambitsebe phunziro la Baibulo?

Onerani VIDIYO yakuti ‘Timasonyeza Kuti Ndife Atumiki a Mulungu . . . mwa Kukhala Oleza Mtima’—Tikamalalikira. Kenako funsani mafunso awa:

  • Kodi lemba la 2 Akorinto 6:​4, 6 lingatithandize bwanji ngati tayamba kuona utumiki wathu uli ngati “dzenje lakuya kwambiri”?

  • Kodi mungafunike kusintha zinthu ziti ngati mwaona kuti zimene mwakhala mukuyesetsa kuchita kuti muyambitse maphunziro a Baibulo sizikuthandiza?

Tizikumbukira kuti sitikhala osangalala chifukwa cha maphunziro a Baibulo amene tayambitsa kapena amene timachititsa. M’malomwake timasangalala chifukwa chodziwa kuti Yehova akusangalala ndi zomwe tikuyesetsa kuchita. (Lu 10:​17-20) Choncho pitirizani kugwira nawo ntchito yapaderayi ndi mtima wonse chifukwa “zonse zimene mukuchita pa ntchito ya Ambuye sizidzapita pachabe.”—1Ak 15:58.

9. Phunziro la Baibulo la Mpingo

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 39 ndi Pemphero