Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

September 2-8

MASALIMO 79-81

September 2-8

Nyimbo Na. 29 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Tizikonda Dzina la Yehova Laulemerero

(10 min.)

Tizipewa makhalidwe amene amanyozetsa dzina la Yehova (Sl 79:9; w17.02 9 ¶5)

Tizitamanda dzina la Yehova (Sl 80:18; (ijwbv 3 ¶4-5)

Yehova amadalitsa anthu omwe ndi omvera amene amasonyeza kuti amakonda dzina lake (Sl 81:​13, 16)

Kuti zochita zathu zizisonyeza kuti timaimira Yehova, tizizidziwikitsa kuti ndife a Mboni za Yehova

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 80:1—N’chifukwa chiyani dzina la Yosefe nthawi zina linkagwiritsidwa ntchito pofotokoza za mafuko onse a Isiraeli? (it-2 111)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(1 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 4 mfundo 4)

5. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 4 mfundo 3)

6. Ulendo Woyamba

(2 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 3 mfundo 3)

7. Ulendo Wobwereza

(5 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pemphani munthu amene anakanapo kuphunzira Baibulo m’mbuyomu kuti muziphunzira naye. (lmd phunziro 8 mfundo 3)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 10

8. “Iwo Adzayeretsa Dzina Langa”

(15 min.) Nkhani yokambirana.

Satana anayamba kunyoza dzina la Yehova m’munda wa Edeni. Kungoyambira nthawi imeneyo, kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova kwakhala nkhani yaikulu kwambiri kwa zolengedwa zonse zanzeru.

Tangoganizirani zitsanzo zochepa chabe za mabodza oipa kwambiri amene Satana wakhala akufalitsa okhudza Yehova. Iye amanena kuti Mulungu ndi wolamulira wankhanza komanso wopanda chikondi. (Ge 3:​1-6; Yob 4:​18, 19) Amanenanso kuti anthu amene amalambira Yehova samamukonda ndi mtima wonse. (Yob 2:​4, 5) Iye wachititsanso anthu mamiliyoni ambiri kuyamba kukhulupirira kuti Yehova si amene analenga dziko lokongolali.—Aro 1:​20, 21.

Kodi mumamva bwanji mukaganizira mabodza amenewa? Mosakayikira, mumafuna kuchitapo kanthu ndi kuteteza dzina la Yehova. Iye anadziwa kuti anthu ake adzakhala ofunitsitsa kumuthandiza kuyeretsa dzina lake. (Yerekezerani ndi Yesaya 29:23.) Kodi mungathandize bwanji?

  • Muzithandiza ena kuti adziwe Yehova komanso kuyamba kumukonda. (Yoh 17:​25, 26) Muzikhala okonzeka kufotokoza umboni woti iye alipodi komanso kuphunzitsa ena za makhalidwe ake ochititsa chidwi.—Yes 63:7

  • Muzikonda Yehova ndi mtima wanu wonse. (Mt 22:​37, 38) Muzimvera malamulo onse a Yehova, ngakhale amene samakusangalatsani, ndipo muzichita zimenezi chifukwa choti mumafuna kumusangalatsa.—Miy 27:11

Onerani VIDIYO yakuti Chikondi Chanu Chisathe Ngakhale Kuti . . . Mukukumana ndi Mavuto Kusukulu. Kenako funsani mafunso awa:

  • Kodi Ariel ndi Diego anateteza bwanji dzina la Yehova?

  • Kodi n’chiyani chinawalimbikitsa kuti ateteze dzina la Yehova?

  • Kodi mungatsanzire bwanji chitsanzo chawo?

9. Phunziro la Baibulo la Mpingo

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 90 ndi Pemphero