Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

September 23-29

MASALIMO 88-89

September 23-29

Nyimbo Na. 22 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Ulamuliro wa Yehova Ndi Wabwino Kwambiri

(10 min.)

Ulamuliro wa Yehova umalimbikitsa chilungamo chenicheni (Sl 89:14; w17.06 28 ¶5)

Ulamuliro wa Yehova umathandiza anthu kukhala ndi chisangalalo chenicheni (Sl 89:​15, 16; w17.06 29 ¶10-11)

Ulamuliro wa Yehova udzakhalapo mpaka kalekale (Sl 89:​34-37; w14 10/15 10 ¶14)

Kuganizira za ulamuliro wa Yehova womwe ndi wapamwamba kwambiri, kungatithandize kusakhala mbali ya dziko andale akamafalitsa mabodza

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 89:37—Kodi kukhulupirika n’kosiyana bwanji ndi kudalirika? (cl 281 ¶4-5)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Pemphani kuti muziphunzira Baibulo ndi munthu amene si Mkhristu. (lmd phunziro 5 mfundo 5)

5. Ulendo Wobwereza

(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. M’pempheni kuti mumusonyeze mmene phunziro la Baibulo limachitikira. (th phunziro 9)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

(5 min.) Nkhani. ijwbq 181—Mutu: Kodi m’Baibulo Muli Nkhani Zotani? (th phunziro 2)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 94

7. Mfundo za Yehova Ndi Zabwino Kwambiri

(10 min.) Nkhani yokambirana.

Anthu ambiri amaona kuti zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kugonana ndiponso ukwati ndi zopanikiza komanso zachikale. Kodi mumatsimikiza mumtima mwanu kuti kutsatira mfundo za Yehova nthawi zonse n’kwabwino kwa inuyo?—Yes 48:​17, 18; Aro 12:2.

Baibulo limaphunzitsa kuti anthu amene amanyalanyaza malamulo a Mulungu “sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu.” (1Ak 6:​9, 10) Koma kodi timatsatira mfundo za Mulungu pa chifukwa chokhachi basi?

Onerani VIDIYO yakuti Zifukwa Zokhalira ndi Chikhulupiriro—Kodi Ndizitsatira Mfundo za Mulungu Kapena Zanga? Kenako funsani funso ili:

  • Kodi mfundo zamakhalidwe abwino za Mulungu zimatiteteza bwanji?

8. Zofunika Pampingo

(5 min.)

9. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 15 ¶15-20

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 133 ndi Pemphero