INDONESIA
Amakondana Ngakhale pa Nthawi ya Mavuto
M’DZIKO la Indonesia, zinthu monga zivomezi, kusefukira kwa madzi komanso kuphulika kwa mapiri zimachitika kawirikawiri. Zimenezi zikachitika, atumiki a Yehova amathandiza mwamsanga anzawo amene akumana ndi mavutowa, makamaka abale awo auzimu. Mwachitsanzo, m’chaka cha 2005, chivomezi champhamvu chinawononga nyumba zambiri m’tauni ya Gunungsitoli, yomwe ndi tauni yaikulu pachilumba cha Nias ku North Sumatra. Abale a m’mipingo ya pachilumba cha Sumatra chomwe chili pafupi ndi chilumba cha Nias komanso a ku ofesi ya nthambi, anatumiza mwamsanga katundu kwa abale amene anakumana ndi vutoli. Woyang’anira dera komanso m’bale woimira ofesi ya nthambi anapita kuchilumbachi kuti akalimbikitse abale ndi alongo. M’bale Yuniman Harefa, yemwe ndi mkulu pachilumba cha Nias ananena kuti: “Chivomezichi chitachitika, anthu anachita mantha kwambiri. Koma zimene gulu la Mulungu linachita zinatithandiza kudziwa kuti sitili tokha.”