Ntchito Yolalikira ndi Kuphunzitsa Padziko Lonse
PADZIKO LONSE
-
MAYIKO 240
-
OFALITSA 8,220,105
-
MAOLA ONSE AMENE TINATHERA MU UTUMIKI WAKUMUNDA 1,933,473,727
-
MAPHUNZIRO A BAIBULO 9,708,968
M'CHIGAWO ICHI
Africa
Kodi ndi njira zatsopano ziti zimene a Mboni za Yehova akugwiritsa ntchito polalikira uthenga wabwino?
North ndi South America
N’chifukwa chiyani mzimayi wina amachita kupita kumunda usiku kukaphunzira Baibulo atayatsa kandulo? N’chifukwa chiyani mfumu ina inkafuna kukumana ndi a Mboni? Nanga n’chiyani chinachititsa kuti munthu wina yemwe kale ankazunza a Mboni alire?
Ku Asia ndi ku Middle East
Zinthu ngati kumangidwa kapena kulumala sizilepheretsa anthu kulalikira za Ufumu.
Europe
Munthu woyankhula Chiromane, munthu yemwe ali m’ndende komanso mayi wina yemwe ankafuna kudzipha anasangalala atamva uthenga wabwino.
Oceania
Matebulo olalikirirapo, timashelefu tolalikirirapo, webusaiti ya jw.org komanso mavidiyo athu akuthandiza anthu ambiri kuti adziwe zimene Baiublo limaphunzitsa