Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mawu kwa Osonkhana

Mawu kwa Osonkhana

UBATIZO Akulu a mumpingo wanu akonza dongosolo labwino mogwirizana ndi mmene zinthu zilili m’dera lanu kuti anthu amene akufuna kubatizidwa, abatizidwe Loweruka chigawo cha m’mawa chikatha.

ZOPEREKA Msonkhanowu wamasuliridwa m’zilankhulo zoposa 400. Ndalama zimene mumapereka mwa kufuna kwanu ndi zimene zimathandiza pa ntchitoyi yomwe ikuchitika padziko lonse. Mungapereke ndalama kudzera pa intaneti pogwiritsa ntchito donate.pr418.com. Timayamikira kwambiri zopereka zanu, ndipo Bungwe Lolamulira likukuyamikirani chifukwa chothandiza ndi mtima wonse pa ntchito ya Ufumu.

SUKULU YA AKHRISTU OLALIKIRA ZA UFUMU Apainiya azaka zapakati pa 23 ndi 65 amene akufuna kuwonjezera utumiki wawo, akupemphedwa kuti auze mlembi wa mpingo wawo komanso alembe fomu ya pa intaneti yofunsira Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu.

Wokonzedwa ndi Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova

© 2021 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania