SIERRA LEONE NDI GUINEA
Ankafunitsitsa Kuionera
MU 1956, abale a ku Freetown anaonetsa filimu yakuti, The New World Society in Action. Abalewo anafotokoza kuti:
“Tinachita lendi holo ina yaikulu kwambiri mu Freetown ndipo tinagawira timapepala toitanira anthu tokwana 1,000. Sitinkadziwa kuti kubwera anthu angati. Patangotsala mphindi 30 kuti filimu iyambe, panali anthu 25 okha. Patapita mphindi zina 15, panafika anthu oposa 100. Pasanapite nthawi mipando yonse yokwana 500 inadzaza ndipo anthu 100 anangoimirira. Anthu enanso 500 anaima panja chifukwa mkati munalibe malo. Atafunsidwa ngati angayembekezere kuti alowe anzawowo akatuluka, anthuwo anavomera ngakhale kuti kunali mvula.”
Kwa zaka zambiri anthu oposa 80,000 a ku Sierra Leone ankaonera filimuyi komanso mafilimu ena.