Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 SIERRA LEONE NDI GUINEA

Kuyambira mu 1915 mpaka 1947 Kale (Gawo 1)

Kuyambira mu 1915 mpaka 1947 Kale (Gawo 1)

 Mmene Choonadi Chinafikira

Uthenga wabwino unafika ku Sierra Leone m’chaka cha 1915. Anthu a m’dzikoli amene anali ku England anabwera ndi mabuku ofotokoza Baibulo. Mu July 1915, Alfred Joseph, yemwe anali Mboni yobatizidwa anafika ku Freetown. Iye anali ndi zaka 31, ndipo kwawo kunali ku Guyana ku South America. Iye anabatizidwa m’chaka chomwechi m’dziko la Barbados ku West Indies ndipo anabwera ku Freetown kudzagwira ntchito yoyendetsa sitima. Alfred ankakhala m’tauni ya Cline, komwe kunali nyumba za anthu ogwira ntchito ku kampani yawoyo. Malowa anali pa mtunda wa makilomita oposa atatu kuchokera ku mtengo wa ku Freetown uja. Iye anayamba kufotokozera anzake uthenga wa m’Baibulo.

M’chaka chotsatira, Alfred anakumana ndi Leonard Blackman, yemwe ankagwira naye ntchito ku Barbados. Mayi ake a Leonard, a Elvira Hewitt, ndi amene anaphunzitsa Alfred choonadi. Leonard ankakhala moyandikana ndi Alfred, choncho nthawi zambiri ankakambirana mfundo za m’Baibulo. Iwo ankagawiranso mabuku ofotokoza za m’Baibulo kwa anzawo ndi anthu ena achidwi.

Alfred ndi Leonard anaona kuti m’munda wa ku Freetown “mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.” (Yoh. 4:35) Mu 1923, Alfred analembera kalata kulikulu ku New York, yonena kuti: “Anthu ambiri kuno akufuna kuphunzira Baibulo. Kodi mungatitumizire munthu woti adzatithandize pa ntchito yolalikira kuno ku Sierra Leone?” Abale kulikuluko anamuyankha kuti: “Titumiza munthu.”

William “Baibulo” Brown ndi mkazi wake, Antonia

 Alfred anati: “Loweruka lina usiku, patadutsa miyezi ingapo, ndinalandira foni.”

“Munthu yemwe anaimba foniyo anati: ‘Kodi ndinu amene munalembera kalata ku Watch Tower Society kupempha anthu oti adzakuthandizeni kulalikira?’

“Ndinayankha kuti, ‘Inde.’

“Munthuyo anati, ‘Ndiyetu anditumiza ineyo.’

“Munthuyu anali William R. Brown. Iye anafikira kuhotelo ya Gainford, limodzi ndi mkazi wake Antonia ndi mwana wawo wamkazi.

“Tsiku lotsatira, ineyo ndi Leonard tikukambirana mfundo za m’Baibulo, tinangoona chimunthu chojintcha chitaima pakhomo. Dzina lake anali William R. Brown. Anali wakhama kwambiri moti ankafuna kukamba nkhani mawa lake. Mwamsanga tinapempha malo ku Wilberforce Memorial Hall, yomwe inali holo yaikulu kwambiri mu Freetown. Tinapempha kuti akambe nkhaniyo Lachinayi, ndipo iyi inali nkhani yoyamba pa nkhani 4 zimene anakamba.

 “Kagulu kathu kanayamba kuuza anthu kuti adzamvetsere nkhaniyi. Tinkagwiritsanso ntchito nyuzipepala ndi timapepala poitana anthuwo. Sitinkadziwa kuti anthuwo angabweredi. Koma anthu pafupifupi 500 anabwera kuphatikizapo atsogoleri a zipembedzo a ku Freetown. Zinali zosangalatsa kwambiri.”

Nkhaniyo inatenga ola lathunthu ndipo M’bale Brown ankagwiritsa ntchito kwambiri Malemba. Ankagwiritsanso ntchito pulojekita kuti anthu aziona mavesi. Ankakonda kunena kuti, “Baibulo likutero, osati Brown.” Anthu anadabwa kwambiri ndipo ankawombera m’manja mfundo iliyonse. Sikuti anthu ankakopeka ndi mawu ake amphamvu koma mfundo za m’Malemba zimene ankafotokoza. Mnyamata wina yemwe ankaphunzira zaubusa anati, “Komatu a Brown amalidziwa bwino Baibulo.”

1924

Mzinda wonse unagwedezeka ndi nkhani za M’bale Brown moti anthu ambiri ankabwera kudzamvetsera nkhanizi. Lamlungu lotsatira, kunabweranso anthu ambiri kudzamvetsera nkhani yofotokoza zimene zimachitika munthu akamwalira. Anthu odalirika m’Matchalitchi osiyanasiyana atamva mfundo zogwira mtima zimene M’bale Brown anakamba usiku umenewo, anachoka m’zipembedzo zawozo.

Khamu la anthu linasonkhana kudzamvetsera nkhani yachinayi, yomwenso inali yomaliza, yamutu wakuti “Anthu Mamiliyoni Ambiri Amene Ali ndi Moyo Sadzafa.” Patapita nthawi, munthu wina wa ku Freetown ananena kuti, “M’matchalitchi ena, mapemphero amadzulo analephereka chifukwa chakuti anthu onse anapita kukamvetsera nkhani ya M’bale Brown.”

Popeza kuti M’bale William R. Brown nthawi zonse ankagwiritsa ntchito Baibulo pofotokoza mfundo zake, anthu anam’patsa dzina lakuti “Baibulo” Brown. M’baleyu ankadziwika ndi dzina limeneli ku West Africa konse ndipo ankalikonda mpaka pamene anamaliza utumiki wake padziko lapansi.