Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 SIERRA LEONE NDI GUINEA

Kuyambira mu 1915 mpaka 1947 Kale (Gawo 3)

Kuyambira mu 1915 mpaka 1947 Kale (Gawo 3)

Ankalalikira M’madera Osiyanasiyana

Abale ndi alongo a mumpingo wa ku Freetown anali a khama ndipo “anatanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira mawu a Mulungu.” (Mac. 18:5) Alfred Joseph ananena kuti: “Nthawi zambiri ndinkamangirira katoni ya mabuku pa njinga yanga yamoto n’kukweza M’bale Thomas kapena Sylvester Grant. Tikatero tinkapita kukalalikira kumidzi ndiponso m’matauni ang’onoang’ono a mu Freetown.”

Abale ndi alongo ankalalikira ku Freetown m’dera lotchedwa The Colony mpaka mu 1927. Koma kuyambira mu 1928, chaka chilichonse nyengo ya mvula isanafike, abalewa ankachita hayala basi n’kupita kukalalikira kumadera ena. Amene sakanakwanitsa kupita nawo pa ulendowu ankathandiza popereka ndalama. Amene ankatsogolera maulendowa anali Melbourne Garber. Abalewa ankalalikira m’matauni ndi m’midzi ya kum’mawa mpaka kukafika kutauni ya Kailahun komanso kum’mwera mpaka kukafika pafupi ndi malire a dziko la Liberia. Lamlungu loyamba la mwezi uliwonse, ankabwereranso kukalimbikitsa anthu omwe anasonyeza chidwi.

Nthawi ina M’bale Brown anapita ku West Indies ndipo anabwera ndi galimoto, yomwe inali imodzi mwa magalimoto  oyambirira kulowa m’dziko la Sierra Leone. Galimotoyi inali ndi zipangizo zamphamvu zokuzira mawu zothandiza pa ntchito yolalikira. M’bale Brown ankaimika galimotoyi pamene pali anthu ambiri ndiye ankaika nyimbo zosangalatsa kuti anthu abwere. Kenako ankakamba nkhani yachidule kapena ankangoika tepi yankhaniyo. Ndiyeno ankauza anthuwo kuti alandire mabuku ofotokoza za m’Baibulo. Anthu akaona galimotoyi ankachita nayo chidwi kwambiri moti anaipatsa dzina lakuti galimoto yolankhula. Choncho ikafika m’dera lawo anthu ambiri ankapita kukamvetsera nyimbo komanso nkhani.

Akulalikira molimba mtima

Kenako M’bale Brown anayamba kuganizira za madera ena amene kunkakhala anthu olankhula Chingelezi ku West Africa, kumene uthenga wabwino unali usanafike. Pamene chaka cha 1930 chinkayandikira, iye anayamba  maulendo okalalikira ku Gambia, Ghana, Liberia ndi Nigeria. M’bale Brown anapeza anthu achidwi m’mayiko onsewa koma ku Nigeria n’kumene anapeza anthu ambiri achidwi. Mu 1930, iye ndi banja lake anasamuka ku Freetown kupita ku Lagos. Ali kumeneko, anapitiriza kuyang’anira ntchito yolalikira ku West Africa.

Panopa ku West Africa kuli abale ndi alongo oposa 500,000 amene akutumikira Yehova

Mu 1950, M’bale Brown anabwerera ku Jamaica chifukwa chodwaladwala koma anasiya mbiri yosaiwalika. Kwa zaka zoposa 27, iye ndi mkazi wake anaona chiwerengero cha Mboni ku West Africa chikuwonjezeka kuchokera pa 2 kufika pa Mboni zoposa 11,000. Iwo anaona kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesaya wonena kuti: “Wamng’ono adzasanduka anthu 1,000, ndipo wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu.” (Yes. 60:22) Panopa padutsa zaka zoposa 60, ndipo ku West Africa kuli “mtundu wamphamvu” wa abale ndi alongo oposa 500,000, omwe akutumikira Yehova.

Boma Litaletsa Mabuku Athu, Anapitiriza Kulalikira

Pamene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inayamba ku Africa, anthu a Yehova ku Sierra Leone sanalowerere nawo. (Mika 4:3; Yoh. 18:36) Choncho akuluakulu a boma ochokera ku Britain ananamizira Mboni za Yehova kuti anali anthu oukira boma. Ndiye anayamba kuwalondalonda ndipo analamula kuti munthu asapezekenso ndi mabuku awo. Akuluakulu a boma oona katundu wolowa m’dzikomo analanda mabuku awo amene ankalowa m’dzikolo n’kuwawotcha. Abale ena anamangidwa chifukwa chopezeka ndi mabuku koma pasanapite nthawi anamasulidwa. *

Ngakhale m’dzikoli munali lamulo loletsa mabuku athu, a Mboni anapitirizabe kulalikira. Pauline Cole ananena kuti:  “M’bale wina yemwe ankagwira ntchito mu sitima yomwe inkabwera kawirikawiri, ankatibweretsera magazini a Nsanja ya Olonda. Ndiyeno tinkakopera magaziniwa kuti tizikagwiritsa ntchito pa misonkhano. Tinkasindikizanso timapepala ta nkhani za m’Baibulo n’kumagawira anthu. Abale anapitiriza kukamba nkhani za onse komanso ankaika matepi a nkhani za M’bale Rutherford m’madera akumidzi.

Yehova anadalitsa khama lawoli. James Jarrett, yemwe anali mkulu komanso mpainiya wapadera kwa nthawi yaitali, anati: “Pa nthawi ya nkhondo, ndikugwira ntchito yosema miyala, mlongo wina anandipatsa kabuku konena za anthu othawa kwawo. Popeza kuti anthu ambiri othawa kwawo ankafika ku Freetown, ndinachita chidwi kwambiri ndi kabukuka. Choncho ndinakawerenga usiku wa tsiku limenelo ndipo nthawi yomweyo ndinazindikira kuti ndapeza chipembedzo choona. Tsiku lotsatira, ndinakumananso ndi mlongo uja ndipo ndinam’pempha timabuku tina kuti ndikapatse azichimwene anga atatu. Ine ndi azichimwene angawo tinayamba kuphunzira Baibulo.”

Pamene nkhondo inkafika kumapeto mu 1945, mpingo wa ku Freetown unali ndi ofalitsa 32. Ofalitsawa anapitiriza kutumikira Mulungu mokhulupirika ndipo sanabwerere m’mbuyo.

Kuitanira Anthu ku Misonkhano

Pa Msonkhano wa Utumiki wa pa August 29, 1945, abale ndi alongo mumpingo wa Freetown anakambirana za ntchito yatsopano imene inalengezedwa mu Utumiki Wathu wa Ufumu (pa nthawiyo unkatchedwa Informant) wa December 1944. Mpingo uliwonse unkafunika kuitanira anthu ku misonkhano 4, yomwe inkachitika mumzinda uliwonse, m’matauni komanso m’midzi. Pa msonkhano uliwonse, m’bale (wa zaka 18 kapena kuposerapo) yemwe anali ndi luso lokamba nkhani mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, ankakamba nkhani kwa ola limodzi. Pambuyo pa misonkhanoyi,  abale ankakhazikitsa magulu ophunzira Baibulo kuti athandize anthu achidwi m’dera lililonse.

Kodi ofalitsa anatani atauzidwa zimenezi? Taonani mfundo zimene anakambirana pa Msonkhano wa Utumiki mumpingo wa ku Freetown:

Tcheyamani: “Mukuganiza kuti tigwira bwanji ntchito imeneyi?”

M’bale Woyamba: “Tisayembekezere kuti ziyenda bwino ngati ku America. Anthu a kuno ndi osiyana ndi a kumeneko.”

M’bale Wachiwiri: “Zimenezi ndi zoona.”

M’bale Wachitatu: “Koma bwanji tiyese?”

M’bale Wachinayi: “Ine ndikuona kuti zivuta kwambiri.”

M’bale Wina: “Komabe tikufunika kutsatira malangizo a gulu la Yehova.”

M’bale Winanso: “Tikudziwa zimenezo koma kuno sizingayende.”

Mlongo Woyamba: “Komatu malangizo a mu Utumiki Wathu wa Ufumu ndi omveka bwino. Tiyeni tiyese.”

Choncho anayesadi kutsatira malangizowo. Abale ankachita misonkhano m’makalasi, m’misika komanso m’nyumba za anthu kuchokera m’mphepete mwa nyanja ku Freetown kukafika kumzinda wa Bo kum’mwera chakum’mawa, mpaka kumzinda wa Kabala womwe unali kumapiri chakumpoto. Zimenezi zinalimbikitsa mpingo ndipo “mawu a Yehova anapitiriza kukula ndi kufalikira.”—Mac. 12:24.

Komabe ofalitsawa ankafunika kuphunzitsidwa ndipo Yehova anawaphunzitsadi.

^ ndime 10 Lamulo loletsa mabuku athu linatha mu 1948.