Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

SIERRA LEONE NDI GUINEA

Kuyambira mu 1945 mpaka 1990 ‘Kuthandiza Anthu Ambiri Kukhala Olungama’—Dan. 12:3. (Gawo 2)

Kuyambira mu 1945 mpaka 1990 ‘Kuthandiza Anthu Ambiri Kukhala Olungama’—Dan. 12:3. (Gawo 2)

Kulemekeza Mphatso Yochokera kwa Mulungu

M’bale William Nushy atafika, anapeza kuti ofalitsa ena sankaona ukwati mmene Yehova amauonera. Ena ankangokhalira limodzi popanda kulembetsa ukwati wawo kuboma. Ena ankatsatira mwambo woti banja limayamba pokhapokha ngati mkazi ali woyembekezera. Ankatero posafuna kukhala m’banja lopanda ana.

Ndiyeno mu May 1953, ofesi ya nthambi inalemba kalata yopita kumipingo yonse yofotokoza zimene Baibulo limanena pa nkhani ya ukwati. (Gen. 2:24; Aroma 13:1; Aheb. 13:4) Mabanja ambiri anauzidwa kuti akalembetse ukwati wawo ndipo ngati salembetsa pofika nthawi inayake, adzachotsedwa mumpingo.—1 Akor. 5:11, 13.

Abale ndi alongo ambiri anasangalala ndi zimenezi. Koma panali ena amene ankachita makani. Anthu oposa hafu ya ofalitsa a mipingo iwiri anasiya kusonkhana. Koma anthu ena anapitiriza kulalikira mwakhama ndipo Yehova anawadalitsa chifukwa cha kukhulupirika kwawo.

Abale anayesetsa kupempha kuboma kuti Nyumba ya Ufumu ya ku Freetown ikhale malo omangitsira ukwati mwalamulo ndipo zinatheka. Ukwati woyamba unamangitsidwa m’Nyumba ya Ufumuyi pa September 3, 1954.  Kenako boma linapereka mabuku a mitchatho kwa abale ena m’maboma 7 a ku Sierra Leone. Izi zinathandiza kuti anthu ambiri amene anayamba kuphunzira, alembetse maukwati awo n’kuyenerera kukhala ofalitsa.

Ukwati umene unachitika pa Nyumba ya Ufumu

Anthu ena amene anali amitala anatsatiranso malangizo a m’Malembawa. Samuel Cooper amene panopa  akukhala ku Bonthe anati: “Mu 1957, ine limodzi ndi akazi anga awiri tinayamba kusonkhana ndipo ndinalembetsa mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Tsiku lina anandipatsa nkhani yonena za ukwati wovomerezeka. Pofufuza nkhaniyi, ndinazindikira kuti ndiyenera kuthetsa banja ndi mkazi wamng’ono. Nditauza abale anga nkhaniyi, onse anandiukira. Vuto linali lakuti mkazi wamng’onoyo ndi amene anandiberekera mwana. Koma ndinatsimikiza kuti nditsatira mfundo za m’Baibulo. Ndinadabwa kwambiri kuona kuti nditangothetsa banjalo, mkazi wanga wamkulu anayamba kubereka. Pano ndabereka naye ana okwana 5.”

Munthu wina amene ankaphunzira Baibulo, dzina lake Honoré Kamano, yemwe ankakhala ku Guinea, anali ndi akazi atatu. Atathetsa banja ndi akazi awiri aang’ono, mkazi wake wamkulu anasangalala kwambiri ndipo anayamba kulemekeza kwambiri mfundo za m’Baibulo. Mkazi wina wamng’ono anakhumudwa kwambiri koma anachita chidwi ndi kulimba mtima kwake potsatira mfundo za m’Baibulo. Kenako anapempha kuti aziphunzira Baibulo ndipo anabatizidwa.

Anthu amadziwa kuti a Mboni za Yehova amalemekeza ukwati

Masiku ano, anthu a ku Sierra Leone ndi Guinea amadziwa kuti a Mboni za Yehova amalemekeza ukwati. Popeza amakhulupirika m’banja, uthenga wawo umamveka bwino ndipo izi zimalemekeza kwambiri Mulungu amene anayambitsa ukwati.—Mat. 19:4-6; Tito 2:10.

Ku Freetown Kunayambika Mpatuko

Mu 1956, amishonale awiri, Charles ndi Reva Chappell, anafika ku Freetown. Iwo akupita kunyumba ya amishonale  anadabwa kuona chikwangwani choitanira anthu kuti akamvetsere nkhani ya Baibulo ku Wilberforce Memorial Hall. M’bale Chappell anati: “Pachikwangwanipo analemba kuti nkhaniyo idzakambidwa ndi C.N.D. Jones, woimira ‘Ekeleziya wa Mboni za Yehova.’”

Jones, yemwe ankati ndi wodzozedwa, ankatsogolera gulu limene linapatuka mumpingo wa ku Freetown zaka zingapo m’mbuyomo. Iye ankati gulu lakelo ndi limene linali la mboni zenizeni za Yehova. Ankanenanso kuti amishonale ndiponso anthu amene anali okhulupirika kwa oyang’anira m’gulu anali mboni zabodza komanso “olisha ng’ombe ochokera ku Giliyadi.”

Zinthu zinafika povuta pamene Jones ndi anzake ena anachotsedwa mumpingo. M’bale Chappell anati: “Chilengezochi chitaperekedwa, abale ena amene ankalekerera mpatuko anadabwa kwambiri. Ena ankalankhula zinthu zosonyeza kuti akudana nazo. Anthu amenewa komanso anthu ena anapitiriza kucheza ndi ampatukowo ndipo ankasokoneza misonkhano ndi utumiki wakumunda. Iwo ankafika pa misonkhano n’kukhala pamalo amene ankati ndi a otsutsa. Ambiri mwa anthu amenewa anasiya choonadi koma ena anazindikira n’kuyambanso kutumikira Mulungu mwakhama.”

Zimene anthu ena okhulupirika anachita zinathandiza kuti mzimu wa Mulungu uzigwira bwino ntchito m’gulu la Yehova. Chaka chotsatira, M’bale Harry Arnott, yemwe anafika m’dzikoli kudzayendera nthambi anati: “Chiwerengero cha ofalitsa ku Sierra Leone chakwera kwambiri kuposa zaka za m’mbuyomu. Zikuonekeratu kuti zinthu ziyenda bwino kwambiri m’tsogolomu.”

Kuphunzitsa Anthu a Mtundu wa Kisi

Patangopita nthawi yochepa M’bale Arnott atachoka, M’bale Chappell analandira kalata yochokera kwa m’bale  wina wa ku Liberia. Iye ankafuna kuyamba kulalikira kwa anthu a mtundu wake a ku Sierra Leone. M’baleyu anali wa mtundu wa Kisi ndipo anthu amenewa anali m’malire a mayiko a Sierra Leone, Liberia ndi Guinea. Iye ankaona kuti anthu ambiri a mtundu umenewu ankafuna kuphunzira Baibulo.

Koma anthu ambiri a mtunduwu anali osaphunzira. Choncho anayambitsa makalasi ophunzitsa kuwerenga ndi kulemba ku Koindu n’cholinga choti anthuwo aphunzire mfundo za m’Baibulo. Anthu ambirimbiri analembetsa sukuluyi. M’bale Chappell anati: “Pa nthawi yochepa chabe, anthu 5 anakhala ofalitsa, kenako anakwana 10, kenako 15, kenako 20. Anthu ambiri anakhala ofalitsa mwamsanga moti ndinkakayikira ngati anasankhadi zimenezi ndi mtima wonse. Koma ndinadabwa kuona kuti ambiri anali okhulupirika komanso akhama.”

Abale atsopanowa analalikira m’tauni yonse ya Koindu ndi madera ozungulira mpaka kukafika m’dziko la Guinea. Iwo ankayenda maola ambiri m’madera ovuta n’kumalalikira m’mafamu ndi m’midzi. M’bale Eleazar Onwudiwe, yemwe anali woyang’anira dera, anati: “Pankatha milungu ingapo mwinanso miyezi osamva kulira kwa galimoto.”

Apa tingati abale ndi alongo a mtundu wa Kisi ankabzala ndi kuthirira ndipo Mulungu ankakulitsa. (1 Akor. 3:7) Munthu wina wakhungu ataphunzira choonadi, analoweza kabuku ka masamba 32 konena za uthenga wabwino wa Ufumu. Ndiyeno ankalakatula ndime zake polalikira kapena kuchititsa maphunziro ndipo anthu ankadabwa kwambiri. Mayi wina wovutika kumva ataphunzira Baibulo, anasintha kwambiri khalidwe lake. Mlamu wake ataona zimenezi anayamba kusonkhana  moti ankayenda mtunda wa makilomita 10 kuti akapezeke pa misonkhano.

Ntchito yolalikira kwa anthu a mtundu wa Kisi inkayenda bwino kwambiri. Mpingo wina unakhazikitsidwa kenako winanso. Ofalitsa pafupifupi 30 anayamba upainiya wokhazikika. Amfumu ena a m’tauni ya Koindu anachita chidwi kwambiri ndi mfundo za m’Baibulo moti anapereka malo oti abale amangepo Nyumba ya Ufumu. Anthu oposa 500 anapezeka pa msonkhano wadera ku Kailahun ndipo zitatero kunakhazikitsidwanso mpingo. Anthu a mtundu wa Kisi anali ochepa kwambiri koma pasanapite nthawi, hafu ya abale ndi alongo ku Sierra Leone anali a mtunduwu.

Komatu anthu ena, makamaka atsogoleri achipembedzo a mtunduwu, sanasangalale ndi zimenezi. Iwo ankaona kuti anthu awo akutha, choncho anayesetsa kuchita zonse zimene angathe kuti asokoneze ntchito yathu. Kodi anachita bwanji zimenezi?