SIERRA LEONE NDI GUINEA
Kuyambira mu 1945 mpaka 1990 ‘Kuthandiza Anthu Kukhala Olungama’—Dan. 12:3. (Gawo 1)
Amishonale Anafika
Mu June 1947, amishonale atatu amene anamaliza maphunziro awo ku Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo anafika ku Freetown. Amishonalewa anali Charles Fitzpatrick, George Richardson ndi Hubert Gresham. Abalewa anali amishonale oyamba koma patapita nthawi, kunabwera enanso ambiri.
Amishonalewa anaona kuti abale ndi alongo kumeneko ankakonda kulalikira, koma ankafunika kuwathandiza kuti aziphunzitsa mwaluso. (Mat. 28:20) Choncho amishonalewo anayamba kuphunzitsa abalewo mmene angachitire maulendo obwereza komanso maphunziro a Baibulo. Ankapatsanso abalewo malangizo atsopano okhudza misonkhano ya mpingo komanso mmene zinthu ziyenera kuyendera m’gulu la Mulungu. Ndiyeno ku Wilberforce Memorial Hall kunachitika msonkhano waukulu. Kumsonkhanowu kunafika anthu 450, ndipo amishonalewo anasangalala kwambiri. Kenako amishonalewo anakhazikitsa tsiku logawira magazini mlungu uliwonse. Zimenezi zinalimbikitsa kwambiri mpingo ndipo zinachititsa kuti ukule.
Vuto linali lakuti amishonalewo ankavutika ndi kutentha. Lipoti la chaka cha 1948 lochokera kunthambi, linati: “Nyengo ku Sierra Leone kuno ndi yovuta kwambiri. Kumagwa mvula yamphamvu kwa miyezi 6. Nthawi zina imagwa kwa milungu iwiri osakata. Nyengo yamvula ikatha kumatentha koopsa.” Anthu a ku Ulaya amene anali oyamba kufika m’dzikoli analipatsa dzina loti manda a azungu. Anthu kumeneko amadwaladwala malungo, ntchofu ndi matenda ena. Mmodzi ndi mmodzi, amishonalewa anayamba kudwala ndipo anabwerera kwawo.
Zimenezi zinadetsa nkhawa kwambiri abale a kumeneko, koma sanafooke. Kuchokera mu 1947 mpaka 1952, chiwerengero cha ofalitsa chinakwera kuchoka pa 38 kufika pa 73. Apainiya ena akhama anathandiza kukhazikitsa mpingo m’tauni ya Waterloo, imene ili pafupi ndi mzinda wa Freetown. Komanso ku Kissy ndi ku Wellington kunakhazikitsidwa magulu a anthu ophunzira Baibulo. Zinkaoneka kuti ku Sierra Leone kuli anthu ambiri ofuna kuphunzira choonadi. Kodi zikanatheka bwanji kuphunzitsa anthu onsewo?
Ulendo Wolimbikitsa
Mu November 1952, m’bale wina wochepa thupi wochokera ku America, wazaka za m’ma 30, anatsika sitima ku Freetown n’kulowa mumzindawo. M’baleyu anali Milton G. Henschel ndipo ankachokera kulikulu lathu. M’baleyu anati: “Ndinadabwa kwambiri kuona kuti mzindawu unali waukhondo kwambiri kuposa mizinda ina yambiri. . . . Kunali misewu yokongola, mashopu, magalimoto atsopano komanso anthu anali piringupiringu.”
M’bale Henschel anapita kunyumba ya amishonale imene inali pafupi ndi mtengo wotchuka wa kotoni uja. Atafika anauza abale kuti gulu likufuna kuthandiza kwambiri ofalitsa a ku Sierra Leone pa ntchito yolalikira. Lamlungu lotsatira, anthu okwana 253 anasonkhana mu Wilberforce Memorial Hall kuti amvetsere zilengezo zosangalatsa. Zilengezo zake zinali zakuti: Ku Sierra Leone kukhala ofesi ya nthambi, woyang’anira dera komanso kuzichitika misonkhano yadera. Analengezanso kuti ku Kissy kukhazikitsidwa mpingo watsopano komanso ntchito yolalikira iwonjezeka m’madera onse. Anthuwo anasangalala kwambiri atamva zimenezi.
M’bale Henschel anati: “Anthuwo ankanena mobwerezabwereza kuti kusheh, kutanthauza kuti ‘zili bwino.’ Iwo anasangalala kwambiri. Anachoka kuholoko kunja kutayamba mdima, . . . ndipo ena ankaimba nyimbo.”
William Nushy, mmishonale yemwe anali atangofika kumene, ndi amene anali woyang’anira ofesi ya nthambi yatsopano. M’bale William Nushy poyamba ankagwira ntchito yochititsa juga m’makasino osiyanasiyana ku United States. Ataphunzira choonadi, anasiya ntchito yakeyo ndipo ankayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo pa zonse zimene ankachita. Zimenezi zinachititsa kuti abale onse a ku Sierra Leone azimukonda ndiponso kumulemekeza.