Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 SIERRA LEONE NDI GUINEA

Kuyambira mu 1991 mpaka 2001 ‘Ng’anjo ya Masautso’—Yes. 48:10 (Gawo 2)

Kuyambira mu 1991 mpaka 2001 ‘Ng’anjo ya Masautso’—Yes. 48:10 (Gawo 2)

Anaphwanya Ofesi ya Nthambi

M’mwezi wa February chaka cha 1998, asilikali aboma ndi gulu la asilikali la Economic Community of West African States Monitoring Group (ECOMOG) anayamba kulimbana ndi zigawenga kuti zichoke ku Freetown. N’zomvetsa chisoni kuti m’bale wina anaphedwa ndi bomba pa nkhondo yoopsayi.

Ofalitsa okwana 150 anathawira kunyumba ya amishonale ya ku Kissy ndi ku Cockerill. M’bale Laddie Sandy yemwe ankagwira ntchito yolondera pa Beteli usiku, ananena kuti: “Tsiku lina usiku, ine ndi m’bale Philip Turay tikugwira ntchito, kunabwera zigawenga ziwiri za RUF zitanyamula mfuti n’kutiuza kuti titsegule zitseko zagalasi za pamalo ofikira alendo. Ine ndi Philip tinathawa n’kukabisala koma anayamba kuombera potsegulira chitseko kambirimbiri. Mwamwayi, chitsekochi sichinatseguke ndipo ngakhale kuti chinali chagalasi sanaganize zongochiswa. Atalephera kutsegula anachoka.

“Patadutsa masiku awiri zigawenga ziwiri zija zinabweranso zili ndi zigawenga zina 20, zitanyamula mfuti. Tinadziwitsa mwamsanga ena onse a m’banja la Beteli ndipo tinathawira kuchipinda china chapansi, chomwe tinakonza kuti tizithawiramo pakayambika zipolowe. Anthu okwana 7, abale 4 ndi alongo atatu, tinabisala kuseri kwa zimigolo ziwiri zikuluzikulu kwinaku tikunjenjemera. Zigawengazo zinawombera chitseko n’kuwotcha chotsegulira cha chitsekocho. Kenako tinamva chigawenga china chikufuula kuti, ‘Tiwasakesake a Mboni za Yehova amenewa ndipo tikawapeza tiwadule makosi.’ Tinangokhala chete titanyonyomala pamalo amene tinabisalapo kwa maola 7 pamene ankasakatulasakatula zinthu m’nyumbamo. Atawononga zinthu komanso kutenga zimene ankafuna ananyamuka n’kumapita.

“Kenako tinatenga katundu wathu wofunikira n’kuthawira kunyumba ya amishonale ya ku Cockerill, yomwe inali chapafupi yomwenso poyamba inali nyumba ya Beteli. Koma tili m’njira tinakumana ndi gulu lina la zigawenga zomwe zinatilanda  katundu. Tinafika kunyumba ya amishonaleko tili ndi mantha kwambiri koma tikuyamikira kuti tili ndi moyo. Tinakhalako kwa masiku ochepa kenako tinabwerera ku Beteli kuti tikakonzeko.”

Miyezi iwiri itadutsa, pambuyo poti gulu la ECOMOG lalamula kuti zigawenga zituluke mumzinda wa Freetown, amishonale omwe anathawira ku Guinea aja anaganiza zobwerera mumzindamo. Koma sanadziwe kuti adzangokhalamo kwa nthawi yochepa kwambiri.

Anakonza Zopha Anthu Onse

Patadutsa miyezi 8, mu December 1998, abale anali pa msonkhano wachigawo wakuti, “Njira ya Moyo ya Mulungu,” m’bwalo la masewera. Msonkhano uli mkati, abalewo anangomva bomba likuphulika kenako n’kuona utsi ukukwera m’mwamba kuchokera kumapiri. Zigawenga zija zinali zitabweranso mumzindawo.

M’masiku otsatira, chipwirikiti chinawonjezereka mumzinda wa Freetown. Komiti ya Nthambi inachita hayala ndege yaing’ono ndipo inanyamula amishonale 12, abale 8 ogwira ntchito pa Beteli ochokera kumayiko ena ndi abale 5 ogwira ntchito yomanga, n’kuwapititsa ku Guinea mumzinda wa Conakry. Patadutsa masiku atatu, pa January 6, 1999, gulu la zigawenga lija linayamba kampeni yawo yopha anthu onse. Zigawengazi zinayamba ziwawa mumzinda wa Freetown ndipo zinapha mwankhanza anthu okwana 6,000. Zinatcheranso mabomba amene anavulaza ndiponso kudula mikono ndi miyendo ya anthu ambirimbiri. Zinaba ana ambiri ndipo zinagwetsa nyumba masauzande ambiri.

N’zomvetsa chisoni kuti m’bale Edward Toby, yemwe anthu ankamukonda kwambiri, anaphedwa mwankhanza pa nthawi imeneyi. Ofalitsa oposa 200 amene anathawa, anawapezera malo okhala ku Beteli komanso kunyumba ya amishonale ku Cockerill. Koma ena anabisala m’nyumba zawo. Abale omwe ankakhala kunyumba ya amishonale ya ku Kissy, yomwe ili kum’mawa kwa tauniyo ankafunitsitsa thandizo la mankhwala. Komabe zinali zoopsa kwambiri kuyenda mumzindamo. Choncho panafunika anthu oti adzipereke kudutsa mumzindamo kuti akathandize  abale awo. M’bale Sandy ndi m’bale Turay omwe ankagwira ntchito yolondera pa Beteli aja ndi omwe anadzipereka kuti akathandize abale amenewa.

M’bale Turay ananena kuti: “Mumzinda monse munali chipwirikiti. Zigawengazi zinakhazikitsa malodibuloko m’malo osiyanasiyana ndipo zinkaimitsa anthu n’kumawavutitsa. Panali patakhazikitsidwa lamulo loti pasapezeke munthu akuyenda kuyambira m’ma 3 koloko masana mpaka m’ma 10 koloko m’mawa, zomwe zinachititsa kuti kuyenda kuzikhala kovuta. Titayenda kwa masiku awiri, tinafika kunyumba ya amishonale ya ku Kissy. Koma tinapeza kuti zigawengazo zaba katundu yense ndi kuyatsa nyumbayo.

“Titazungulira pamalowo tinapeza m’bale Andrew Caulker, ndipo anali ndi mabala aakulu m’mutu. Zigawenga zinali zitam’manga manja n’kumukhapa ndi nkhwangwa m’mutu. Mwamwayi m’baleyu sanamwalire ndipo anakwanitsa kuthawa.  Tinathamanga naye kuchipatala ndipo patapita nthawi anayamba kupeza bwino. M’baleyu anadzakhala mpainiya wokhazikika.”

(Kuchokera kumanzere) Laddie Sandy, Andrew Caulker ndi Philip Turay

Mboni zina sizinaphedwe kapena kuvulazidwa chifukwa chodziwika kuti sizilowerera ndale. M’bale wina ananena kuti: “Nthawi ina zigawenga zinatilamula kuti aliyense amange kansalu koyera kumutu n’kumavina m’misewu posonyeza kuti tili kumbali yawo. Zinatiuza kuti, ‘Ngati simukufuna, tikudulani mkono, mwendo kapena kukuphani.’ Ine ndi mkazi wanga tinachita mantha kwambiri ndipo tinangoima pambali n’kupemphera kuti Yehova atithandize. Ataona kuti tili ndi mantha, bambo wina yemwe anali m’gulu lomwelo yemwenso ankakhala kufupi ndi kwathu anauza mtsogoleri wa zigawengazo kuti: “Ameneyutu ndi m’bale wathu. Salowerera ndale, ndiye tivina m’malo mwake.’ Kenako mtsogoleri wawo uja anangotisiya, ndipo mwamsanga tinapita kunyumba.”

Kwa kanthawi mumzindamo munakhala bata. Choncho abale anayambiranso kulalikira ndi kupanga misonkhano koma ankachita zimenezi mosamala kwambiri. Ofalitsa ankavala mabaji a msonkhano wachigawo n’cholinga choti asamavutike pamalo amene apolisi ankasecha katundu amene munthu wanyamula. Komanso pakakhala mizera yaitali abale ankapezanso mwayi woyamba kukambirana za Baibulo.

Nkhondo imeneyi inachititsa kuti mumzinda wa Freetown muyambike vuto la kuperewera kwa chakudya ndi zinthu zina. Choncho ofesi ya nthambi ya ku Britain, inatumiza makatoni okwana 200 a zinthu zothandizira abalewa. M’bale Billie Cowan ndi M’bale Alan Jones anayenda ulendo wa pa ndege kuchokera mumzinda wa Conakry kupita ku Freetown kuti akaone ngati katunduyo wadutsa bwinobwino malodibuloko onse. Ndipo mwamwayi katunduyo anafika nthawi imene inakhazikitsidwa kuti anthu asiye kuyenda ija isanakwane. M’bale James Koroma ndi amene ankapita ku Conakry kukatenga mabuku ndi zinthu zina zofunikira. China mwa chakudya chauzimu chimenechi chinkapititsidwa kwa abale a ku Bo ndi ku Kenema.

Ndege yonyamula chithandizo ikufika ku Freetown

Pa August 9, 1999, amishonale omwe anathawira ku Conakry aja anayamba kubwerera ku Freetown. Chaka chotsatira asilikali aboma  la Britain anathamangitsa gulu la zigawenga lija mumzinda wa Freetown. Komabe nkhondoyi inkachitikabe mwa apo ndi apo, koma mu January 2002, analengeza kuti yatha. Nkhondoyi inatha zaka 11 ndipo anthu pafupifupi 50,000 anaphedwa, 20,000 analumala, nyumba 300,000 zinagwetsedwa ndipo anthu 1.2 miliyoni anathawa kwawo.

Nanga kodi gulu la Yehova linkachita zotani pa nthawi imeneyi? N’zodziwikiratu kuti Yehova anateteza ndi kudalitsa gulu lake. Pa nthawi ya nkhondo anthu pafupifupi 700 anabatizidwa. Komanso ngakhale kuti Mboni zambirimbiri zinali zitathawa, chiwerengero cha ofalitsa ku Sierra Leone chinawonjezereka ndi 50 peresenti. Nakonso ku Guinea, chiwerengero cha ofalitsa chinawonjezereka ndi 300 peresenti. Ndipo chofunika kwambiri n’choti anthu a Mulungu anakhalabe okhulupirika pa nthawi yonseyi. Pa nthawi imene anali “m’ng’anjo ya masautso,” Akhristu anasonyeza kuti anali okondana kwambiri komanso ogwirizana ndipo “anapitiriza mwakhama kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino.”—Yes. 48:10; Mac. 5:42.