ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI
Gulu la Yehova Likupita Patsogolo
Lachisanu, pa July 5, 2013, banja la Beteli ku United States linasangalala kwambiri ndi chilengezo chimene Anthony Morris wa m’Bungwe Lolamulira anapereka. Chilengezochi chinali chakuti: “Lachinayi pa July 4, 2013, tagwirizana kuti tigulitse nyumba zathu zokwana 6, zomwe zili ku 117 Adams Street ndi ku 90 Sands Street ku Brooklyn. Kuti tigulitse nyumba nambala 1 mpaka 5 tikufunika kuti tisamuke m’nyumbazi pofika mkatikati mwa mwezi wa August chaka chino.”
M’bale Morris anafotokoza kuti Dipatimenti Yochapa Zovala imene ili m’nyumba nambala 3, ikhalabe momwemo mpaka m’katikati mwa chaka cha 2014. M’baleyu ananena kuti: “Zikuoneka kuti tidzasamuka m’nyumba ya ku 90 Sands Street m’chaka cha 2017.”
Nyumba zikuluzikulu 6 zimenezi zikugulitsidwa chifukwa chakuti likulu la Mboni za Yehova likusamutsidwa kuchoka ku New York City kupita ku Warwick m’chigawo cha New York, komwe kuli malo okwana maekala 253. Koma zinali zosatheka kuyamba kukumba pamalowa pokonzekera ntchito yomangayi tisanapatsidwe chilolezo.
Choncho banja la Beteli ku United States linamvetsera mwatcheru chilengezo chimene M’bale Mark Sanderson wa m’Bungwe Lolamulira anapereka Lachinayi pa July 18. Chilengezochi chinali choti: “Ndife osangalala kulengeza kuti Lachitatu madzulo, pa July 17, bungwe loona mapulani a nyumba ku Warwick lavomereza pulani yathu ya likulu latsopano la Mboni za Yehova. Timayembekezera kuvomereza komaliza kumeneku kuti tiyambe kupempha zilolezo zina zoti tiyambe ntchito yomanga ku Warwick. N’zochititsa chidwi kuti ativomereza patatha zaka 4 ndendende kuchokera pamene tinamalizitsa kupereka ndalama zogulira malo a ku Warwick. Kuwonjezera pamenepo, zimene zachitika masiku angapo apitawa kuti pulani yathu ivomerezedwe, zikusonyeza kuti Yehova akudalitsa ntchito yathu.” M’bale Sanderson anathokoza banja lonse chifukwa cha khama lawo komanso chifukwa chopempherera mochokera pansi pa mtima ntchito yofunikayi. Kenako iye anati: “Koposa zonse, tikutamanda komanso kuthokoza Yehova potithandiza pa ntchito yathu yosamutsa likulu lathu kupita ku Warwick.”
Lachisanu, pa July 26, M’bale Morris anakumana ndi antchito odzipereka okwana 1,000 a ku Beteli komanso a m’Komiti Yomanga Yachigawo (RBC). Abale ndi alongowa anasonkhana m’chipinda chatsopano chodyera ku Tuxedo, m’chigawo cha New York, kufupi ndi ku Warwick. Atawalimbikitsa mwauzimu, anawauza kuti ali ndi chilengezo. M’bale Morris ananena kuti: “M’manjamu ndili ndi fomu imene ndalandira, ndipo ndikufuna kuti ndikuwerengereni. Pamwamba pa fomuyi pali mawu akuti: ‘Chilolezo cha Ntchito Yomanga.’” Atangowerenga mawu amenewa, antchito odziperekawo anawombera m’manja mosangalala kwambiri. Kenako M’bale Morris anapitiriza kuwerenga ndime zina za chilolezochi ndipo onse anasangalala zedi. Chilolezochi chinali choyamba ndipo chinaperekedwa ndi akuluakulu a mzinda wa Warwick, moti apa n’kuti patangotha maola atatu kuchokera pamene anachilandira.
Kodi ku Wallkill, ku Warwick ndi ku Tuxedo Kukuchitika Zotani?
Kuyambira mu August 2009, pamene ntchito yowonjezera nyumba zina inayambika ku Wallkill, abale ndi alongo pafupifupi 2,800 ongodzipereka akhala akutumikira kumeneko. Abale ndi alongowa akumanga nyumba yogona yatsopano, malo osungira magalimoto ndiponso maofesi. Nyumba ina yogona akuikonzanso, ndipo akusintha zina ndi zina m’nyumba yosindikizira mabuku, m’nyumba yochapiramo zovala, muholo, pofikira alendo ndi malo ena. Tikuyembekezera kuti ntchito imeneyi ipitirizabe mpaka kumapeto kwa chaka cha 2015.
Panopa ntchito ili mkati kumalo amene tikufuna kuti kudzakhale likulu lathu lapadziko lonse ku Warwick. Kwa miyezi yochepa imene ntchitoyi yakhala ikuchitika, akumba pamalowa n’kuika mapaipi ndi zinthu zina zofunika kuzikwirira pansi. Chakumapeto kwa chaka cha 2013, ntchito yomanga nyumba zitatu zoyambirira, inayambika. Nyumba ina ndi yokonzeramo magalimoto, ina yosungiramo magalimoto a alendo ndipo ina ndi ya Dipatimenti Yokonzetsa Zinthu. Nyumba zimenezi n’zofunika kwambiri pa ntchito yokonzetsa zinthu zogwirira ntchito pamalowo pa nthawi yomangayi komanso ntchitoyo ikadzatha. Akamaliza nyumba zimenezi adzayamba kumanga nyumba zogona ndi maofesi ndipo akonza zoti ntchito imeneyi idzayambe mu 2014.
Ku Tuxedo kulinso malo athu a maekala 50 ndipo ali pa mtunda wa makilomita 10 kumpoto kwa Warwick. M’bale Kenneth Chernish amene ali m’Komiti Yoyang’anira Zomangamanga ananena kuti: “Cholinga cha malo amenewa n’choti azithandizira pa ntchito zina zimene zikuchitika ku Warwick. Antchito ena odzipereka azigona kumeneko, kulandirira chakudya komanso azisungirako zipangizo zina.” Pofuna kuti ntchito ya ku Tuxedo ithe mofulumira, anasankha makomiti ena omanga a kum’mawa kwa United States kuti akathandize ntchito zina.
Antchito ambiri odzipereka amene akutumikira m’Makomiti Omanga Achigawo m’dzikoli akufunitsitsa kuti nawonso apatsidwe mwayi wokathandiza ntchito yomanga likulu lathuli. Abale ndi alongo amene amadziwa ntchito zosiyanasiyana adzipereka kale ndipo akuthandiza pa ntchito imeneyi. Mwachitsanzo, Leslie Blondeau limodzi ndi mwamuna wake Peter, amene akugwira ntchito m’dipatimenti yolumikiza mapaipi ananena kuti: “Tikukondana kwambiri chifukwa chogwirira ntchito limodzi ndipo zimene tikuchitazi sitidzaziiwala.”
Mlongo wina dzina lake Mallory Rushmore ananena kuti: “Panopa ndikugwira ntchito limodzi ndi abale amene akulumikiza mawaya amagetsi ku Tuxedo kuno. Tsiku lililonse limakhala losangalatsa, makamaka kuona anthu onse kuno komanso antchito odzipereka akugwira ntchito limodzi.”
M’bale Quincy Dotson ananena kuti: “Kugwira nawo ntchito imeneyi ndi mwayi waukulu kwambiri. Ndinkaganiza kuti abale apindula kwambiri ndi thandizo langa, koma kwenikweni ineyo ndi amene ndikupindula kwambiri.”
M’bale Chernish ananena kuti: “N’zosangalatsa kwambiri kugwira nawo ntchito imeneyi. Abale ndi alongo akugwira ntchitoyi mofulumira kwambiri ndipo akuigwira mwaluso, komanso akusangalala kwabasi.”