Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Lipoti la Milandu

Lipoti la Milandu

Mtumwi Paulo anauza Akhristu kuti: “Kumbukirani amene ali m’ndende ngati kuti mwamangidwa nawo limodzi.” (Aheb. 13:3) Monga atumiki a Yehova, timakumbukira abale ndi alongo athu okhulupirika ndipo timapempherera “anthu onse apamwamba, kuti tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendere, ndiponso kuti tikhale odzipereka kwa Mulungu mokwanira komanso tikhale oganiza bwino.”—1 Tim. 2:1, 2; Aef. 6:18.

M’munsimu muli milandu ina imene Mboni za Yehova zinali nayo chaka chathachi:

Abale athu ku Russia akupitiriza “mwakhama kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino” ngakhale kuti tchalitchi cha Orthodox komanso akuluakulu aboma akuyesetsa kuletsa ntchito yathu kumeneko. (Mac. 5:42) Akuluakulu  aboma ku Russia akupitiriza kugwiritsa ntchito molakwika lamulo lawo losamveka bwino lokhudza kuchita zinthu monyanyira, limene poyamba analikhazikitsa pofuna kuthana ndi uchigawenga. Iwo akugwiritsa ntchito lamuloli poletsa zofalitsa zathu komanso pozunza abale ena. Zimenezi zachititsa kuti makhoti agamule kuti zofalitsa zathu zokwana 70 zili ndi mfundo zolimbikitsa anthu kuchita zinthu monyanyira. Ndipo akuluakulu aboma aika zofalitsa zimenezi pa mndandanda wa mabuku oletsedwa m’dzikolo. Zimenezi zachititsa kuti akuluakulu ena aboma azilowa m’Nyumba za Ufumu ndiponso m’nyumba za abale athu kuti akafufuze mabukuwa amenewo. Apolisi amagwira komanso kujambula ndi kutenga zidindo za zala za anthu ambiri a Mboni chifukwa cholalikira ndipo kawirikawiri amawaopseza.

 Kuyambira mu May 2013, abale ndi alongo a mumzinda wa Taganrog anaimbidwa mlandu chifukwa chochita misonkhano ndiponso kulalikira. Aka n’koyamba kuchokera pamene boma la Soviet Union linagwa kuti a Mboni aimbidwe milandu chifukwa chochita zinthu zokhudza chikhulupiriro chawo. Akukuakulu aboma m’madera ena ku Russia komweko akukakamiza akhoti kuti agamule zoti mabuku athu amasokoneza anthu komanso kuti abale athu amalimbikitsa anthu kuti azidana chifukwa chosiyana zipembedzo.

Abale ndi alongo athu akuzunzidwabe ku Eritrea. Pofika mu July 2013, m’ndende za m’dzikoli munali abale ndi alongo athu okwana 52. Chiwerengero chimenechi chikuphatikizapo abale 8 a zaka 70 ndi alongo 6. Abale atatu omwe ndi Paulos Eyassu, Isaac Mogos ndi Negede Teklemariam, akhala m’ndende kuyambira pa September 24, 1994, chifukwa chokana kulowa usilikali.

Pa abale ndi alongo onse amene ali m’ndende m’dzikoli, ambiri ali kundende ya Meiter yomwe ili m’chipululu kumpoto kwa mzinda wa Asmara, womwe ndi likulu ladzikoli. Kuchokera mu October 2011 mpaka mu August 2012, akuluakulu aboma analanga abale athu okwana 25 powatsekera m’nyumba ya malata okhaokha. Hafu ya nyumba imeneyi inali m’nthaka ndipo hafu inayo inali pamtunda. M’miyezi yotentha, apolisi olondera akaidi amatulutsa akaidi m’ndendezi kuti asafe ndi kutentha. Komanso, akaidiwa sawapatsa chakudya chabwino ndi madzi okwanira moti abale athu amawonda ndiponso kufooka. Zomvetsa chisoni n’zakuti M’bale Yohannes Haile, wa zaka 68, anamwalira mu August 2012 chifukwa cha kuzunzidwaku, ndipo M’bale Misghina Gebretinsae anamwalira mu 2011.

Kyrgyzstan: Nyumba ya Ufumu iyi inawonongedwa kawiri ndi anthu a m’derali