Kabuku Kothandiza Kuphunzira Mawu a Mulungu
Dzina la Mulungu M’Malemba Achiheberi
Kodi Mabaibulo ena anamasulira bwanji dzina la Mulungu kuchokera M’chiheberi? Kodi n’koyenera kutchula dzinali kuti “Yehova”? Kodi dzina la Mulungu limatanthauza chiyani?
Dzina la Mulungu M’Malemba Achigiriki
Onani umboni wamphamvu wosonyeza kuti dzina la Mulungu linkapezeka m’mipukutu yoyambirira ya Chigiriki.
Tchati: Aneneri Komanso Mafumu a Yuda ndi Isiraeli (Gawo 1)
Onani tchati chosonyeza mbiri ya m’Baibulo kuchokera mu 997 B.C.E. mpaka mu 800 B.C.E.
Tchati: Aneneri Komanso Mafumu a Yuda ndi Isiraeli (Gawo 2)
Onani tchati chosonyeza mbiri ya m’Baibulo kuchokera mu 800 B.C.E. mpaka mu 607 B.C.E.
Main Events of Jesus’ Earthly Life—Leading Up to Jesus’ Ministry
Onani tchati ndi mapu osonyeza zomwe zinachitika kuchokera mu 3 B.C.E. mpaka mu 29 C.E.
Zochitika Zikuluzikulu m’Moyo wa Yesu Padziko Lapansi—Chiyambi cha Utumiki wa Yesu
Onani tchati ndi mapu osonyeza zimene zinachitika kuchokera mu 29 C.E. mpaka pa Pasika wa mu 30 C.E.
Zochitika Zikuluzikulu M’moyo wa Yesu Padziko Lapansi—Utumiki Waukulu wa Yesu M’Galileya (Gawo 1)
Onani tchati ndi mapu osonyeza zimene zinachitika kuchokera mu 30 C.E. mpaka pa Pasika mu 31 C.E.
Zochitika Zikuluzikulu M’moyo wa Yesu Padziko Lapansi—Utumiki Waukulu wa Yesu M’Galileya (Gawo 2)
Onani tchati ndi mapu osonyeza zochitika kuchokera mu 31 C.E. mpaka pambuyo pa Pasika, mu 32 C.E.
Zochitika Zikuluzikulu M’moyo wa Yesu Padziko Lapansi—Utumiki Waukulu wa Yesu M’Galileya (Gawo 3) ndi ku Yudeya
Onani zochitika zimene zinachitika mu 32 C.E. pa nthawi ya Chikondwerero cha Pasika ndi chikondwerero chopereka kachisi kwa Mulungu.
Zochitika Zikuluzikulu M’moyo wa Yesu Padziko Lapansi—Utumiki wa Yesu Wakumapeto Kum’mawa kwa Yorodano
Onani tchati ndi mapu osonyeza zochitika mu 32 C.E. pambuyo pa Chikondwerero Chopereka Kachisi kwa Mulungu.
Zochitika Zikuluzikulu M’moyo wa Yesu Padziko Lapansi—Utumiki Womaliza wa Yesu M’Yerusalemu (Gawo 1)
Onani tchati ndi mapu osonyeza zimene zinachitika kuyambira pa Nisani 8 mpaka pa Nisani 14, mu 33 C.E.
Zochitika Zikuluzikulu M’moyo wa Yesu Padziko Lapansi—Utumiki Womaliza wa Yesu M’Yerusalemu (Gawo 2)
Onani tchati ndi mapu osonyeza zochitika kuyambira pa Nisani 14 mpaka pa Iyari 25, mu 33 C.E.
Uthenga wa M’Baibulo
Baibulo lili ndi uthenga wosavuta komanso wogwirizana kuyambira ku Genesis mpaka Chivumbulutso. Kodi uthenga wake ndi wotani?
Chiyambi Komanso Maulendo a Atumiki Akale
Onani mapu a malo otchulidwa m’buku la Genesis.
Ulendo Wochoka ku Iguputo
Onani njira imene Aisiraeli anadutsa popita ku Dziko Lolonjezedwa.
Kugonjetsa Malo M’Dziko Lolonjezedwa
Onani pa mapu njira zomwe Aisiraeli ankadutsa popita ku nkhondo.
Chihema Chopatulika Komanso Mkulu wa Ansembe
Onani chithunzi cha chihema ndi zovala za mkulu wa ansembe wachiisiraeli.
Magawo a Mafuko a Isiraeli M’Dziko Lolonjezedwa
Onani mapu osonyeza madera amene mafuko a Isiraeli anapatsidwa ndi malo amene oweruza ankalamulira kuyambira Otiniyeli mpaka Samisoni.
Ufumu wa Davide ndi Solomo
Onani mapu a dziko la ana a Isiraeli pamene unali mtundu wamphamvu.
Kachisi Womangidwa ndi Solomo
Onani chithunzi cha kachisi chosonyeza malo ndi zinthu zosiyanasiyana zokwana 14.
Maulamuliro Amphamvu Padziko Lonse Oloseredwa ndi Danieli
Onani chifaniziro choopsa chomwe mfumu inalota cha mu Danieli chaputala 2 komanso mmene zimenezi zinakwaniritsidwira.
Dziko la Isiraeli M’nthawi ya Yesu
Onani mizinda ya Aroma yomwe inali mu Isiraeli komanso yozungulira Isiraeli.
Kachisi wa Paphiri M’nthawi ya Atumwi
Onani chithunzi chosonyeza mmene zinthu zinalili m’kachisi, m’nthawi ya Yesu.
Wiki Yomaliza ya Moyo wa Yesu Padziko Lapansi (Gawo 1)
Onani mapu a Yerusalemu ndi madera ozungulira, komanso tchati chosonyeza zimene zinachitika kuyambira pa Nisani 8 mpaka pa Nisani 11, 33 C.E.
Wiki Yomaliza ya Moyo wa Yesu Padziko Lapansi (Gawo 2)
Onani zimene zinachitika kuyambira pa Nisani 12 mpaka Nisani 16, 33 C.E.
Kufalikira kwa Chikhristu
Onani mapu osonyeza madera amene Paulo anafika polalikira uthenga wabwino komanso mizinda yotchulidwa m’buku la Chivumbulutso.
Miyezo ya Zinthu Ndiponso Malonda
Onani chithunzi kuti muone miyezo ya zinthu zamadzi, zomwe si zamadzi ndi miyezo yoyezera mtunda yotchulidwa m’Baibulo.
Ndalama ndi Kulemera kwa Zinthu
Onani chithunzi kuti muone ndalama ndi kulemera kwa zinthu kotchulidwa m’Baibulo.
Kalendala Yachiheberi
Yerekezerani kalendala ya m’Baibulo yotsatira tsiku limene mwezi waoneka ndi kalendala ya masiku ano, kuti muone nthawi ya zochitika za chaka ndi chaka.