Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

1

Dzina la Mulungu M’Malemba Achiheberi

Dzina la Mulungu M’Malemba Achiheberi

Dzina la Mulungu m’zilembo zakale zachiheberi zomwe zinkagwiritsidwa ntchito Ayuda asanapite ku ukapolo ku Babulo

Dzina la Mulungu m’zilembo zachiheberi zomwe zinkagwiritsidwa ntchito Ayuda atabwerera kuchoka ku ukapolo ku Babulo

Dzina la Mulungu lolembedwa m’zilembo zinayi zachiheberi, limapezeka pafupifupi nthawi 7,000 m’Malemba Achiheberi. M’Baibulo la Dziko Latsopano, zilembo zinayizo zamasuliridwa kuti “Yehova.” Dzina limeneli ndi lomwe limapezeka kwambiri m’Baibulo kuposa dzina lililonse. Ngakhale kuti anthu omwe anauziridwa kulemba Baibulo anagwiritsa ntchito mayina ena aulemu monga akuti “Wamphamvuyonse,” “Wam’mwambamwamba” komanso “Ambuye,” iwo ankalemba zilembo zinayizi akafuna kutchula dzina lenileni la Mulungu.

Yehova Mulungu ndi amene anatsogolera anthu olemba Baibulo kuti azigwiritsa ntchito dzina lake. Mwachitsanzo, anatsogolera mneneri Yoweli kulemba kuti: “Aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” (Yoweli 2:32) Ndiponso, Mulungu anachititsa wolemba Masalimo wina kulemba kuti: “Anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova, inu nokha ndinu Wam’mwambamwamba, wolamulira dziko lonse lapansi.” (Salimo 83:18) Ndipotu dzina la Mulunguli limapezeka nthawi 700 m’buku la Masalimo lokha, lomwe ndi buku la ndakatulo ndiponso nyimbo zomwe anthu a Mulungu ankaimba komanso kuziloweza. Ndiyeno n’chifukwa chiyani dzina la Mulungu silipezeka m’Mabaibulo ambiri? N’chifukwa chiyani omasulira Baibulo la Dziko Latsopano anasankha kulemba dzina la Mulungu kuti “Yehova”? Nanga dzina la Mulungu loti Yehova, limatanthauza chiyani?

Mbali ina ya buku la Masalimo yomwe ili mu Mpukutu wa ku Nyanja Yakufa wopezeka m’nthawi ya Yesu. Mawu ena alembedwa m’njira imene Chiheberi ankachilembera Ayuda atabwera kuchokera ku ukapolo ku Babulo, koma zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu zalembedwa m’Chiheberi chakale

N’chifukwa chiyani dzinali silipezeka m’Mabaibulo ambiri? Pali zifukwa zosiyanasiyana. Anthu ena amaona kuti Mulungu Wamphamvuyonse safunika kukhala ndi dzina lapadera lomutchulira. Ena anatengera mwambo wachiyuda wosafuna kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu, mwina chifukwa choopa kuti angapeputse dzinalo. Pomwe enanso amaganiza kuti popeza katchulidwe kenikeni ka dzina la Mulungu sikakudziwika, ndi bwino kumagwiritsa ntchito mayina aulemu monga “Ambuye” kapena “Mulungu.” Koma zifukwa zonsezi n’zosamveka tikaganizira mfundo zotsatirazi:

  • Anthu amene amanena kuti Mulungu Wamphamvuyonse safunikira kukhala ndi dzina lake lenileni, ayenera kudziwanso mfundo yakuti m’Mabaibulo amene analipo ngakhale Khristu asanabwere, mumapezeka dzina lenileni la Mulungu. Monga mmene taonera kale, Mulungu anatsogolera anthu kuti alembe dzinali m’Mawu ake nthawi pafupifupi 7,000. Choncho zikusonyezeratu kuti Mulungu amafuna kuti tidziwe dzina lake ndi kuligwiritsa ntchito.

  • Ngakhale kuti omasulira Baibulo ena anachotsa dzina la Mulungu pofuna kulemekeza mwambo wachiyuda, ayeneranso kudziwa mfundo ina yofunika kwambiri. N’zoona kuti alembi ena Achiyuda ankakana kutchula dzina la Mulungu koma sanalichotse m’Mabaibulo awo. M’mipukutu yakale yomwe inapezeka m’dera la Qumran, lomwe lili pafupi ndi Nyanja Yakufa, dzina la Mulungu limapezekamo kambirimbiri. Omasulira Baibulo ena amavomereza kuti dzina la Mulungu linkapezeka m’mipukutu yoyambirira koma m’malo onse amene linkapezekamo ankalichotsa n’kumaikamo dzina la ulemu lakuti “AMBUYE” m’zilembo zazikulu. Koma funso ndi lakuti, n’chifukwa chiyani omasulira Baibulo amenewa anachita zimenezi ngakhale ankadziwa kuti dzinali linkapezeka m’mipukutu ya Baibulo kambirimbiri? Kodi ndi ndani anawapatsa mphamvu yochotsa dzina la Mulungu m’Baibulo? Omasulira Baibulowa ndi amene angadziwe mayankho a mafunso amenewa.

  • N’zodabwitsa kuti anthu amene amanena kuti dzina la Mulungu siliyenera kugwiritsidwa ntchito chifukwa sitidziwa katchulidwe kake kenikeni, amatha kugwiritsa ntchito dzina la Yesu. Komatu ophunzira a Yesu ankatchula dzinali mosiyana kwambiri ndi mmene timatchulira masiku ano. Akhristu Achiyuda ankatchula dzina la Yesu kuti Ye·shuʹa‛. Ndipo dzina lakuti “Khristu,” ankalitchula kuti Ma·shiʹach, kapena “Mesiya.” Akhristu olankhula Chigiriki ankatchula dzinali kuti I·e·sousʹ Khri·stosʹ, ndipo olankhula Chilatini ankalitchula kuti Ieʹsus Chriʹstus. Koma motsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu, omasulira Malemba Achigiriki anaika dzinali m’Baibulo. Zimenezi zikusonyeza kuti Akhristu oyambirira ankatsatira mmene anthu ankatchulira dzinali pa nthawiyo m’chilankhulo chawo. Choncho Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano inaona kuti n’zomveka kutchula dzina la Mulungu kuti “Yehova” ngakhale kuti sitikudziwa bwinobwino mmene ankatchulira dzinali a m’Chiheberi.

N’chifukwa chiyani omasulira Baibulo la Dziko Latsopano anasankha kulemba dzina la Mulungu kuti “Yehova”? M’Chingelezi, zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu (יהוה) amazilemba kuti YHWH. Iwo analemba zilembo zoimira dzina la Mulungu m’njira imeneyi chifukwa mawu onse a m’Chiheberi chakale anali opanda mavawelo. Koma anthu ambiri atayamba kugwiritsa ntchito mawu achiheberi, owerenga anayamba kuikirira mavawelo.

Patadutsa zaka pafupifupi 1000 kuchokera pamene anamaliza kulemba Malemba Achiheberi, akatswiri a maphunziro Achiyuda anakonza njira yodziwira mmene angatchulire mawu Achiheberi komanso tizizindikiro towathandiza kudziwa mavawelo omwe angagwiritse ntchito powerenga Chiheberi. Pa nthawi imeneyi Ayuda ambiri ankaganiza kuti n’kulakwa kutchula dzina la Mulungu moti anapeza mawu ena oti aziwagwiritsa ntchito akafuna kutchula dzinalo. Choncho pamene anakopera zilembo zinayi zachiheberi zija anaphatikiza zilembozi ndi mavawelo a m’mawu omwe ankawagwiritsa ntchito akafuna kutchula dzina la Mulungu. Chotero, mavawelo amene anawaikawo satithandiza kudziwa bwinobwino mmene dzinali ankalitchulira poyambirira m’Chiheberi. Ena amanena kuti dzinali linkatchulidwa kuti “Yahweh,” pomwe ena amanena kuti linkatchulidwa m’njira zina. Mpukutu wina wa ku Nyanja Yakufa womwe uli ndi mbali ya buku la Levitiko m’Chigiriki unamasulira dzina la Mulungu kuti Iao. Kuwonjezera pa kalembedwe kameneka olemba Baibulo Achigiriki amanena kuti dzinali linkatchulidwanso kuti Iae, I·a·beʹ, komanso I·a·ou·eʹ. Komabe zoona zake n’zakuti sitidziwa mmene atumiki a Mulungu akale ankatchulira dzina limeneli m’Chiheberi. (Genesis 13:4; Ekisodo 3:15) Chomwe tikudziwa n’chakuti Mulungu ankagwiritsa ntchito dzina lake mobwerezabwereza polankhula ndi anthu ake, anthuwo ankamutchula ndi dzina lake komanso ankaligwiritsa ntchito akamauza ena za iye.—Ekisodo 6:2; 1 Mafumu 8:23; Salimo 99:9.

Ndiye n’chifukwa chiyani omasulira Baibulo la Dziko Latsopano analemba dzinali kuti “Yehova”? N’chifukwa chakuti m’Chingelezi akhala akugwiritsa ntchito kalembedwe ka dzina la Mulungu kameneka kwa nthawi yaitali.

Dzina la Mulungu pa Genesis 15:2 m’Baibulo limene William Tyndale anamasulira, mu 1530

William Tyndale ndi amene anayamba kugwiritsa ntchito dzina la Mulungu m’mabuku 5 oyambirira a Baibulo lachingelezi lomwe analimasulira m’chaka cha 1530. Iye anagwiritsa ntchito mawu akuti “Iehouah.” Patapita nthawi kalankhulidwe ka Chingelezi kanasintha zomwe zinachititsa kuti kalembedwe ka dzinalo kasinthe. Mwachitsanzo m’chaka cha 1612, womasulira Baibulo wina dzina lake, Henry Ainsworth anagwiritsa ntchito mawu akuti “Iehovah,” pomasulira buku la Masalimo. Kenako m’chaka cha 1639, pamene buku lake linakonzedwanso n’kusindikizidwa limodzi ndi mabuku 5 oyambirira a Baibulo, dzina lija lakuti “Iehouah,” linalowedwa m’malo ndi lakuti “Yehova.” Mu 1901, omasulira Baibulo la American Standard Version anagwiritsiranso ntchito dzina lakuti “Yehova” pamene pankapezeka dzinali m’Malemba Achiheberi.

Pofotokoza chifukwa chimene anagwiritsira ntchito dzina lakuti “Yehova” m’malo mwa “Yahweh,” katswiri wa maphunziro a Baibulo, dzina lake Joseph Bryant Rotherham ananena m’buku lake limene analemba mu 1911 kuti anasankha kutero “pofuna kugwiritsa ntchito mawu amene anthu owerenga Baibulo akuwadziwa.” (Studies in the Psalms) M’chaka cha 1930, katswiri winanso wamaphunziro a Baibulo dzina lake A. F. Kirkpatrick anafotokoza mfundo yofanana ndi imeneyi ponena za dzina lakuti “Yehova.” Iye anati: “Akatswiri a masiku ano oona za galamala amanena kuti dzinali linayenera kutchulidwa kuti Yahveh kapena Yahaveh; koma YEHOVA ndi katchulidwe kamene n’kodziwika kwambiri m’Chingelezi, ndipo chofunika kwambiri si katchulidwe kolondola ka dzinali koma chofunika n’kudziwa kuti ndi dzina la Mulungu lenileni osati laulemu ngati lakuti ‘Ambuye.’”

Zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu, YHWH: “Amachititsa Zinthu Kukhalapo”

Mneni HWH: “kukhala”

Kodi dzina loti Yehova limatanthauza chiyani? M’Chiheberi dzina lakuti Yehova linachokera ku mneni amene amatanthauza “kukhala,” ndipo akatswiri ambiri amaphunziro amaona kuti mawuwa m’Chiheberi amatanthauza chinthu chimene chimachititsa kuti chinachake chichitike. Choncho a m’Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano anaona kuti dzina la Mulungu limatanthauza kuti “Amachititsa Zinthu Kukhalapo.” Akatswiri amaphunziro ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani imeneyi. Komabe tanthauzo la dzina la Mulunguli ndi logwirizana ndi udindo wake monga Mlengi wa zinthu zonse komanso yemwe amakwaniritsa cholinga chake. Sikuti Mulungu anangolenga zinthu zakumwamba ndi dziko lapansi, koma iye akupitiriza kuchita zinthu pofuna kukwaniritsa cholinga chake ndiponso chifuniro chake.

Choncho tanthauzo la dzina loti Yehova silimangotanthauza zimene zili pa lemba la Ekisodo 3:14 zakuti: “Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala.” Mawu amenewa satanthauzira mokwanira dzina la Mulungu. M’malomwake akungosonyeza mmene Mulungu alili kuti amatha kukhala chilichonse chimene akufuna, kuti akwaniritse cholinga chake. Choncho ngakhale kuti imeneyi ndi mbali ina ya tanthauzo la dzina la Mulungu lakuti Yehova, sikuti limangotanthauza kukhala chilichonse chimene akufuna. Limatanthauzanso zimene amachita m’chilengedwe chakechi komanso zimene amachita pokwaniritsa cholinga chake.