Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chitsanzo Chabwino Anyamata a Chiheberi Atatu

Chitsanzo Chabwino Anyamata a Chiheberi Atatu

Chitsanzo Chabwino Anyamata a Chiheberi Atatu

Hananiya, Misael, ndi Azariya anakana kugwadira fano lalikulu limene linaimikidwa ku Dura, pafupi ndi mzinda wa Babulo. Anthu onse amene analipo, anagwadira fanolo koma anyamatawa sanagonje ngakhale kuti mfumu inkawawopseza komanso anthu ena ankawakakamiza kuti agwadire fanolo. Ndipo anauza Nebukadinezara mwaulemu koma molimba mtima kuti iwo sangasiye kutumikira Yehova.—Danieli 1:6; 3:17, 18.

Anyamata amenewa anatengedwera ku ukapolo ku Babulo ali aang’ono. Iwo anali okhulupirika kuyambira ali ana ndipo anakana kudya chakudya chomwe mwina chinali choletsedwa m’Chilamulo cha Mulungu. Ndipo zimenezi zinawathandiza kuti atakula apirire mayesero ena. (Danieli 1:6-20) Iwo anadziwa kuti kumvera Yehova n’kopindulitsa kwambiri. Kodi inunso mwatsimikiza kutsatira malangizo a Mulungu ngakhale anzanu atakukakamizani kuti muchite zoipa? Mukaphunzira kumvera Yehova pazinthu zazing’ono, mudzathanso kukhala okhulupirika pazinthu zazikulu.Miyambo 3:5, 6; Luka 16:10.