Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingafotokoze Motani Zimene Ndimakhulupirira Zokhudza Mulungu?

Kodi Ndingafotokoze Motani Zimene Ndimakhulupirira Zokhudza Mulungu?

Mutu 36

Kodi Ndingafotokoze Motani Zimene Ndimakhulupirira Zokhudza Mulungu?

Kodi n’chiyani makamaka chimene chingakulepheretseni kufotokoza zinthu zokhudza chikhulupiriro chanu kwa mnzanu wa m’kalasi?

□ Kusadziwa zambiri za Baibulo

□ Kuopa kunyozedwa

□ Kusadziwa mmene mungayambire kukambirana naye

Kodi ndi njira iti yofotokozera za chikhulupiriro chanu imene siingakuvuteni?

□ Kulankhula ndi munthu wa m’kalasi mwanu ali yekha

□ Kufotokozera kalasi yonse pamodzi

□ Kulemba mfundo za m’Baibulo zimene mumakhulupirira m’chimangirizo

Tchulani munthu wa kusukulu kwanu amene mukuganiza kuti angasangalale kukambirana naye za Baibulo ngati mutadziwa mmene mungayambire kukambiranako.

N’ZODZIWIKIRATU kuti anzanu a kusukulu sakonda kukambirana nkhani zokhudza Mulungu. Iwo angasangalale kwambiri mutayambitsa nkhani zina monga zamasewera osiyanasiyana, zovala ndiponso zokhudza anyamata kapena atsikana. Koma mutati mutchule zokhudza Mulungu, palibe amene angakuyankheni.

Zimenezi sizikutanthauza kuti anzanuwo sakhulupirira Mulungu. Iwo amam’khulupirira ndithu, koma kungoti amachita manyazi kukambirana nkhani imeneyi. Mwina amaganiza kuti, ‘Imeneyi sinkhani yosangalatsa.’

Nanga Bwanji Inuyo?

Zingakhale zomveka ndithu ngati mumazengereza kuuza anthu a kusukulu kwanu nkhani zokhudza Mulungu. Palibe amene angasangalale kusalidwa ndi anzake, ndiponso kunyozedwa n’kopweteka kwambiri. Kodi zinthu ngati zimenezi zingakuchitikireni ngati mutauza anzanu za chikhulupiriro chanu? Inde, zingachitike. Komabe, mwina mungadabwe kudziwa kuti anzanu ambiri amafuna atadziwa mayankho a mafunso monga awa: Tsogolo la dzikoli n’lotani? ndiponso N’chifukwa chiyani pali mavuto ambiri? Iwo angakonde kukambirana nkhani ngati zimenezi ndi wachinyamata mnzawo kusiyana ndi munthu wachikulire.

Ngakhale zili choncho, kulankhula ndi achinyamata anzanu nkhani zokhudza chipembedzo kungaoneke ngati kovuta nthawi zina. Komabe, mukamalankhula nawo, musachite zinthu ngati kuti ndinu wodziwa zonse komanso musade nkhawa kuti mwina mungaphonyetseko zinthu zina. Kuuza ena zimene mumakhulupirira tingakuyerekezere ndi kuimba gitala. N’zodziwikiratu kuti pamene mukuphunzira kuimba gitala, zingaoneke zovuta ndithu. Koma mukachita khama, mukhoza kukwanitsa. Ndiyeno kodi mungatani kuti muyambe kukambirana nkhani zokhudza Mulungu?

Nthawi zambiri, n’zotheka kupeza nkhani imene simungavutike kukambirana. Mwachitsanzo, ngati kusukulu kwanu kuli nkhani inayake imene ili m’kamwam’kamwa, mukhoza kufotokozapo maganizo anu malinga ndi zimene Malemba amanena pankhaniyo. Mwinanso mungayese kulankhula ndi munthu mmodzi wa m’kalasi mwanu payekha. Njira inanso yosavuta ndi iyi: Achinyamata ena achikhristu amaika mabuku ofotokoza Baibulo padesiki pawo kuti aone amene angachite nawo chidwi. Ndipo nthawi zambiri amapezekadi ochita chidwi moti amayamba kukambirana nawo zokhudza Mulungu.

Panjira zimene tafotokozazi, ndi iti imene inuyo mukuona kuti mungaigwiritsire ntchito? ․․․․․

Kodi mungaganizire njira ina imene mungaigwiritsire ntchito kuti mufotokozere munthu wa m’kalasi mwanu zimene mumakhulupirira? Ngati ilipo, ilembeni m’munsimu.

․․․․․

Nthawi zina phunziro linalake m’kalasi mwanu lingakupatseni mwayi wofotokoza zimene mumakhulupirira. Mwachitsanzo, kodi mungatani ngati mukukambirana nkhani yoti zinthu zamoyo zinakhalako mwa kuchita kusanduka kuchokera ku zinthu zina? Kodi mungafotokoze bwanji chikhulupiriro chanu choti zinthu zinachita kulengedwa?

Mmene Mungafotokozere Kuti Zinthu Zinachita Kulengedwa

Mnyamata wina dzina lake Ryan anati: “Kusukulu kwathu, nkhani yoti zamoyo zinakhalako mwa kuchita kusanduka, anatiphunzitsa ngati ndi yoona. Zimenezi zinandisokoneza maganizo chifukwa zinali zotsutsana kwambiri ndi zimene ndinali nditaphunzira m’Baibulo.” Mtsikana wina dzina lake Raquel anafotokoza maganizo ofanana ndi amenewa. Iye anati: “Ndinachita mantha kwambiri aphunzitsi athu a sayansi atanena kuti phunziro lathu lotsatira lidzakhala lakuti zamoyo zinakhalako mwa kuchita kusanduka. Ndinadziwiratu kuti ndidzafunika kufotokoza m’kalasi zimene ndimakhulupirira pa nkhani yovutayi.”

Kodi inuyo mumamva bwanji mukamaphunzira m’kalasi mwanu nkhani yakuti zamoyo zinakhalako mwa kuchita kusanduka? Mosakayikira, inu mumakhulupirira kuti Mulungu ‘analenga zinthu zonse.’ (Chivumbulutso 4:11) Paliponse mumaona umboni wakuti zinthu zinachita kulengedwa. Koma mabuku a sayansi ndiponso aphunzitsi anu amati zamoyo zinakhalako mwa kuchita kusanduka. Choncho mungaganize kuti simuyenera kutsutsa zimene mabuku ndiponso aphunzitsi anu amanena.

Koma dziwani kuti si inu nokha amene simukhulupirira chiphunzitso chakuti zamoyo zinakhalako mwa kuchita kusanduka. Ngakhale asayansi ena komanso aphunzitsi ndi ana asukulu ambiri sakhulupirira zimenezi.

Komabe, kuti mufotokoze zimene mumakhulupirira, zoti zinthu zinachita kulengedwa, mufunika kudziwa zimene Baibulo limaphunzitsadi pankhaniyi. Palibe chifukwa choti muzitsutsira nkhani zimene Baibulo silifotokoza mwachindunji. Taonani zitsanzo izi:

Buku langa la sayansi limati dziko lapansili, mapulaneti ena ndi dzuwa zakhalako kwa zaka mabiliyoni ambiri. Baibulo limanena kuti tsiku loyamba la kulenga lisanayambe, dziko lapansili, mapulaneti ena ndi dzuwa zinali ziliko kale. Choncho zinthu zimenezi ziyenera kuti zakhalapo kwa zaka mabiliyoni ambiri.—Genesis 1:1.

Aphunzitsi anga amati n’zosatheka kuti dziko lapansili linalengedwa masiku 6 okha. Baibulo silinena kuti tsiku lililonse la masiku 6 a kulenga linali la maola 24 enieni.

M’kalasi mwathu tinaphunzira zitsanzo zingapo zosonyeza mmene nyama ndi anthu asinthira m’kupita kwanthawi. Baibulo limati Mulungu analenga zinthu zamoyo “mwa mitundu yawo.” (Genesis 1:20, 21) Siligwirizana ndi mfundo yoti moyo unachokera ku zinthu zopanda moyo, komanso yoti Mulungu anayambitsa moyo kuchokera ku selo imodzi yokha imene m’kupita kwa nthawi inasintha n’kukhala zamoyo zosiyanasiyana. Komabe, zinthu za mu “mtundu” uliwonse zikhoza kusintha kwambiri. Choncho, zimene Baibulo limanena zikugwirizana ndi mfundo yoti kusintha kukhoza kuchitika pakati pa zinthu za mu “mtundu” umodzi.

Malinga ndi zimene taona m’nkhaniyi, fotokozani zimene munganene ngati aphunzitsi kapena munthu wa m’kalasi mwanu atanena kuti:

“Sayansi imasonyeza kuti anthufe tinachita kusanduka kuchokera ku zamoyo zina.” ․․․․․

“Sindikhulupirira kuti kuli Mulungu chifukwa chakuti saoneka.” ․․․․․

Khalani Otsimikiza pa Zimene Mumakhulupirira

Ngati mukuleredwa ndi makolo achikhristu, mwina mumakhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa chifukwa chakuti ndi zimene iwo akhala akukuphunzitsani. Koma tsopano popeza mukukula, mufunika kumalambira Mulungu “mwa kugwiritsa ntchito luntha la kulingalira,” zimene zimafuna kukhala wotsimikiza pa zimene mumakhulupirira. (Aroma 12:1) Poganizira zimenezi dzifunseni kuti, ‘N’chiyani chimandikhutiritsa ineyo kuti kuli Mlengi?’ Mnyamata wina wazaka 14 dzina lake Sam, akamatsimikizira kuti zinthu zinachita kulengedwa amagwiritsa ntchito chitsanzo cha thupi la munthu. Iye amati: “Thupi la munthu lili ndi ziwalo zambirimbiri zovuta kuzimvetsa, ndipo zonse zimagwira ntchito mogwirizana. N’zosamveka kunena kuti linangosintha kuchokera ku zinthu zina.” Mtsikana wina wazaka 16 dzina lake Holly, anafotokoza maganizo ogwirizana ndi mfundo imeneyi. Iye anati: “Kuyambira pamene anandipeza ndi matenda a shuga, ndaphunzira zambiri zokhudza mmene thupi limagwirira ntchito. Mwachitsanzo, n’zochititsa chidwi kuti kapamba, kachiwalo kakang’ono komwe kali kuseri kwa chifu, amagwira ntchito yaikulu kwambiri pothandiza magazi ndi ziwalo zina kugwira ntchito bwino.”

Lembani zinthu zitatu pamizere yotsatirayi zimene zimakukhutiritsani inuyo kuti kuli Mlengi.

1. ․․․․․

2. ․․․․․

3. ․․․․․

Palibe chifukwa chochitira manyazi ndi chikhulupiriro chanu chakuti kuli Mulungu ndiponso kuti zinthu zinachita kulengedwa. Malinga ndi maumboni amene alipo, n’zosakayikitsa kuti anthufe tinachita kulengedwa.

Mfundo zonse zimene akatswiri asayansi amaphunzitsa zosonyeza kuti zamoyo zinakhalako mwa kuchita kusanduka, n’zopanda umboni. Koma pali umboni wochuluka wakuti zinthu zinachita kulengedwa. Mukaiganizira nkhani imeneyi mofatsa mwa kugwiritsa ntchito luntha lanu la kulingalira, mudzakhala wotsimikiza kufotokozera ena zimene mumakhulupirira zokhudza Mulungu.

M’MUTU WOTSATIRA

Nthawi zambiri mumaona achinyamata anzanu akubatizidwa. Kodi inuyo ndinu wokonzeka kubatizidwa?

LEMBA LOFUNIKA

“Sindichita nawo manyazi uthenga wabwino. Kunena zoona, uthengawo ndiwo mphamvu ya chipulumutso imene Mulungu amaipereka kwa aliyense amene ali ndi chikhulupiriro.”—Aroma 1:16.

MFUNDO YOTHANDIZA

Musamakayikire kapena kuchita manyazi mukamauza anzanu a kusukulu zimene mumakhulupirira chifukwa mukamatero, zingapangitse kuti anzanuwo azikunyozani. Koma iwo angamakumvetsereni mwaulemu ngati mukulankhula nawo motsimikiza, ngati mmene iwowo angalankhulire zimene amakhulupirira.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Nthawi zina aphunzitsi akapemphedwa kupereka umboni wotsimikizira kuti zamoyo zinachita kusanduka, amalephera kutero ndipo amazindikira kuti iwo amakhulupirira zimenezi chifukwa chongoti ndi zimene anaphunzira.

ZOTI NDICHITE

Kuti ndiyambe kukambirana ndi munthu wa m’kalasi mwathu za Baibulo, ndingachite izi: ․․․․․

Nditafunsidwa chifukwa chake ndimakhulupirira kuti kuli Mlengi, ndinganene izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

● N’chifukwa chiyani m’pofunika kuti muzifotokozera ena zimene mumakhulupirira?

● Kodi ndi njira zina ziti zimene zingakuthandizeni kuti kusukulu kwanu muzifotokoza momasuka zimene mumakhulupirira?

● Kodi mungasonyeze motani kuti mumayamikira amene analenga zinthu zonse?—Machitidwe 17:26, 27.

[Mawu Otsindika patsamba 299]

“Kusukulu ndi gawo lolalikira limene ana asukulu tokhafe ndi amene tingafikeko.”—Anatero Iraida

[Chithunzi patsamba 298]

Mofanana ndi kuimba gitala, kuuza ena zimene mumakhulupirira kumafuna luso ndipo mungakhale waluso kwambiri mukamayesetsa nthawi zonse kuchita zimenezi

[Chithunzi pamasamba 300, 301]

N’zotheka kulimba mtima n’kufotokozera anthu ena zimene mumakhulupirira