Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kusintha kwa Thupi

Kusintha kwa Thupi

Chigawo 2

Kusintha kwa Thupi

Kodi simukusangalala ndi mmene thupi lanu likusinthira?

□ Inde □ Ayi

Kuchokera pamene thupi lanu linayamba kusintha, kodi munayamba kusokonezeka maganizo, kuchita mantha kapena kumva kuti muli nokha?

□ Inde □ Ayi

Kodi tsiku lililonse mumatha nthawi yaitali mukuganizira za mnyamata kapena mtsikana winawake?

□ Inde □ Ayi

Musadandaule ngati pali funso limene mwayankha kuti “inde” pa mafunso amenewa, ndipo musaganize kuti muli ndi vuto. Dziwani kuti mukamakula, thupi lanu limasintha ndipo zimenezi zimachititsa kuti nthawi zina muzisangalala kwambiri kapena muzikhumudwa kwambiri. N’zodziwikiratu kuti muli mwana munkafuna mutakhala wamkulu, koma panopo mukuchita mantha ndi mmene thupi lanu likusinthira. Mitu 6 mpaka 8 ikuthandizani kudziwa zochita pankhaniyi.

[Chithunzi chachikulu pamasamba 56, 57]