Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Ngati Sindikusangalala ndi Mmene Ndikuonekera?

Kodi Ndingatani Ngati Sindikusangalala ndi Mmene Ndikuonekera?

Mutu 7

Kodi Ndingatani Ngati Sindikusangalala ndi Mmene Ndikuonekera?

Kodi simusangalala ndi mmene mumaonekera?

□ Inde □ Ayi

Kodi mumasala chakudya n’cholinga choti muchepe thupi?

□ Inde □ Ayi

Kodi ndi zinthu ziti pa thupi lanu zimene mukanakonda kuti zisinthe? (Chongani zimene mwasankha.)

Msinkhu

Thupi

Khungu

Tsitsi

Mawu

MUSADANDAULE ngati mwayankha mafunso awiri oyambirira aja kuti “inde” komanso ngati mwachonga zinthu ziwiri kapena kuposerapo. Dziwani kuti anthu ena sakuonani kuti ndinu wosaoneka bwino. Achinyamata ambiri sasangalala ndi mmene amaonekera. Mwachitsanzo, ofufuza apeza kuti atsikana ambiri amaopa kunenepa kuposa mmene amaopera nkhondo, matenda a khansa kapena imfa ya makolo awo.

N’zoona kuti mumadziona mogwirizana ndi maonekedwe anu komanso mmene anthu ena amakuonerani. Mtsikana wina wazaka 19, dzina lake Maritz, anati: “Azikulu anga awiri anali okongola kwambiri, koma ineyo sindinkaoneka bwino chifukwa chonenepa. Kusukulu anzanga ankandinyoza kwambiri. Komanso azakhali anga anandipatsa dzina loti Chubs, kutanthauza kuti chiduntu. Dzinali linali la galu wawo yemwe anali wamng’ono koma wonenepa kwambiri. Nayenso Julie wazaka 16, anati: “Mtsikana wina kusukulu kwathu ankandigemula kuti ndili ndi ‘mano otuluka.’ Imeneyi si inali nkhani yaikulu, koma zinkandiwawa kwambiri ndipo mpaka pano ndimachitabe manyazi ndi mano anga.”

Kodi Mumadandaula Kwambiri?

Sikulakwa kuganizira kwambiri za mmene mumaonekera. Ndipotu Baibulo limati akazi ndi amuna ena monga Sara, Rakele, Yosefe, Davide, ndi Abigayeli anali ooneka bwino. Limatinso mtsikana wina wotchedwa Abisagi anali “wokongola” kwambiri.—1 Mafumu 1:4.

Komabe, achinyamata ambiri amaganizira kwambiri mmene akuonekera. Mwachitsanzo, atsikana ena amaganiza kuti munthu wokongola amafunika kukhala wochepa thupi, chifukwa atsikana ambiri a m’magazini otchuka amaoneka choncho. Dziwani kuti zithunzi za atsikana okongolawo amachita kuzikongoletsa pa kompyuta komanso atsikanawo amasala kwambiri chakudya kuti azioneka choncho. Mukamadziyerekezera ndi atsikana a m’magazini amenewo mukhoza kungodzivuta ndi mtima. Koma bwanji ngati mukuonadi kuti simuoneka bwino? Ngati mukuona choncho, ganiziraninso bwinobwino za maonekedwe anu.

Kodi Mumadziona Molakwika?

Pali magalasi ena amene amasintha kwambiri maonekedwe a munthu. Kodi munayamba mwadzionapo pagalasi lotere? Ngati munatero, n’zodziwikiratu kuti galasilo silinakuonetseni mmene mulili.

Achinyamata ambiri amadziona m’njira yolakwika imeneyi. Mwachitsanzo, ofufuza ena anapeza kuti atsikana 58 pa 100 alionse ankadziona kuti ndi onenepa kwambiri, koma zoona zake zinali zakuti ndi atsikana 17 okha pa 100 alionse amene analidi onenepa kwambiri. Ofufuza anapezanso kuti akazi 45 pa 100 alionse omwe anali ochepa thupi ankadziona kuti ndi onenepa kwambiri.

Ofufuza ena anapezanso kuti atsikana ambiri amene amaona kuti ndi onenepa kwambiri amakhala kuti si onenepa n’komwe. Komabe zingakuvuteni kukhulupirira zimenezi ngati muli wojintcha. Kodi n’chiyani chinachititsa kuti mukhale wojintcha choncho?

Nthawi zambiri chimakhala chibadwa. Anthu ena amangokhala ochepa thupi mwachibadwa basi. Koma ngati mwachibadwa muli wojintcha ndiye kuti sizingatheke kukhala wochepa thupi. Ngakhale atakuuzani mfundo imeneyi kuchipatala, mutha kumadzionabe kuti ndinu wonenepa. N’zoona kuti masewera olimbitsa thupi ndiponso zakudya zopatsa thanzi zingakuthandizeni kuti musanenepe kwambiri, komabe dziwani kuti n’zovuta kusintha chibadwa chanu.

Nthawi zina chimakhala chifukwa cha kukula. Mtsikana akamakula, thupi lake limayamba kunenepa pafupifupi kuwirikiza katatu. Koma nthawi zambiri zimenezi sizipitirira. Mtsikana wazaka mwina 11 kapena 12 amene amaoneka kuti ndi wonenepa amatha kukhala wochepa thupi akadutsa msinkhu umenewu. Komabe kodi mungatani ngati simuoneka bwino chifukwa choti simudya mokwanira kapena simuchita masewera olimbitsa thupi? Nanga mungatani ngati dokotala wakuuzani kuti muchepetseko thupi chifukwa cha thanzi lanu?

Kudziona Moyenerera

Baibulo limatilimbikitsa kuti tikhale “odziletsa m’zizolowezi” zathu. (1 Timoteyo 3:11) Choncho musamadzimane chakudya. Njira yabwino kwambiri yochepetsera thupi ndiyo kudya zakudya zopatsa thanzi ndi kuchita masewera olimbitsa thupi.

Musavutike ndi kugwiritsa ntchito njira zamakono zochepetsera thupi. Mwachitsanzo, n’zoona kuti mapilisi owondetsa angakuchititseni kuti musamafune kudya, koma pakapita nthawi, thupi lanu limawazolowera ndipo mumayambanso kudya kwambiri. Komanso mapilisiwo angasokoneze kayendedwe ka chakudya m’thupi ndipo munganenepe kwambiri. Mapilisiwa amachititsanso anthu ena chizungulire, vuto la kuthamanga magazi, ndiponso kuvutika maganizo. Nthawi zinanso munthu akayamba kumwa mapilisiwa amavutika kuti asiye. Pewaninso mapilisi amtunduwu amene amachititsa kuti chakudya chizigayika msanga m’thupi kapena amene amachititsa kuti m’thupi muzikhala madzi ochepa.

Kudya zakudya zopatsa thanzi ndiponso kuchita masewera olimbitsa thupi nthawi zonse, kungakuthandizeni kuti muzioneka bwino komanso kuti muzidzimva bwino. Kuchita masewera othamangitsa magazi kangapo pa mlungu, kungakuthandizeni kwambiri kukhala ndi thanzi labwino. Nthawi zina kuyenda mongowongola miyendo n’kokwanira.

Chenjerani ndi Vuto Lodana ndi Chakudya

Pofuna kuchepetsa thupi, achinyamata ena amapezeka kuti ayamba kudana ndi chakudya. Vutoli ndi loopsa ndipo limayamba ngati munthu wayamba kusala chakudya. Msungwana wina dzina lake Masami, atalandira thandizo la vutoli kwa miyezi inayi, anati: “Panopa munthu akandiuza kuti ‘wayamba kuoneka bwino,’ pansi pamtima ndimangoti, ‘ndiye kuti ndikunenepa.’ Nthawi zina ndimalira ndipo ndimangoti, ‘bola ndikanakhala ngati mmene ndinalili miyezi inayi yapitayo.”

Vutoli lingayambe mosayembekezereka. Mtsikana angayambe kumadya pang’ono n’cholinga choti achepetseko thupi. Koma akatero sakhutitsidwabe ndi mmene akuonekera. Akadziyang’ana pagalasi anganene kuti: “Sindinasinthe kwenikweni.” Choncho angaganize zochepetsabe thupi. Ndipo atatero angafune kuchepetsakonso pang’ono, n’kumangopitirizabe. Pamenepa m’pamene pamayambira vutoli.

Ngati mwayamba kudana ndi chakudya, mukufunikira thandizo. Uzani makolo anu za vutoli kapena munthu aliyense wamkulu amene mumam’khulupirira. Baibulo limati: “Bwenzi limakonda nthawi zonse; ndipo m’bale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.”—Miyambo 17:17.

Kukongola Kwenikweni

Baibulo silinena kuti kukongola kwa munthu ndi maonekedwe ake okha ayi, koma amafunikanso kuti akhale ndi khalidwe labwino losangalatsa Mulungu.—Miyambo 11:20, 22.

Taganizirani za Abisalomu, mwana wa Mfumu Davide. Baibulo limati: “M’Isiraeli monse munalibe wina anthu anam’tama kwambiri chifukwa cha kukongola kwake monga Abisalomu; kuyambira ku mapazi kufikira pakati pa mutu wake mwa iye munalibe chilema.” (2 Samueli 14:25) Koma mnyamatayu anali ndi nsanje yoopsa. Chifukwa chodzitukumula, anafuna kulanda ufumu kwa mfumu yodzozedwa ndi Yehova. Choncho, Baibulo limati Abisalomu anali munthu wosakhulupirika ndiponso woipa mtima kwambiri.

Mfundo yofunika kuikumbukira ndi yakuti: ‘Yehova amayesa mitima’ osati kukongola kwa munthu. (Miyambo 21:2) Choncho, ngakhale kuti maonekedwe ndi ofunika, makhalidwe abwino ndi amene ali ofunika kwambiri. Ndipotu, makhalidwe auzimu ndi amene angakuchititseni kuti mukhale munthu wosiririka kwambiri.

WERENGANI ZAMBIRI PANKHANIYI M’BUKU LOYAMBA, MUTU 10

M’MUTU WOTSATIRA

Pali achinyamata ambiri amene ndi olumala kapena akuvutika ndi matenda aakulu. Ngati muli ndi mavuto amenewa, kodi mungatani?

LEMBA LOFUNIKA

“Munthu ayang’ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang’ana mumtima.”—1 Samueli 16:7.

MFUNDO ZOTHANDIZA

Mukafuna kuchepetsa thupi . . .

● Musamaphonye kudya chakudya cha m’mawa. Mukaphonya, mumamva njala ndipo mumafuna kudya kwambiri kuposa mmene mumadyera.

● Imwani madzi ambiri musanadye. Madziwo amachepetsa njala ndipo mumadya chakudya chochepa.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Akatswiri ena amati ngati munthu akusala zakudya n’cholinga choti awonde, thupi lake limagaya chakudya pang’onopang’ono ndipo amayambanso kunenepa.

ZOTI NDICHITE

Kuti ndikhale ndi thanzi labwino ndiyenera kuchita izi: ․․․․․

Ineyo ndizichita masewera olimbitsa thupi awa: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

Kodi mumasangalala ndi mmene mumaonekera?

Kodi mungachite chiyani kuti muyambe kuoneka bwino?

Kodi mungamuuze chiyani mnzanu amene ali ndi vuto lodana ndi zakudya?

Kodi mungam’thandize bwanji mng’ono wanu kuti azidziona moyenerera?

[Mawu Otsindika patsamba 69]

“Kwanthawi yaitali, anthu ankandigemula kuti ndili ndi maso akuluakulu. Koma ndinayamba kumaseka nawo akamandinena komanso ndinasiya kudandaula ndi mmene ndimaonekera. Ndimanyadiranso kuti ndili ndi makhalidwe abwino.”—Anatero Amber

[Chithunzi patsamba 68]

N’zotheka kumadziona molakwika ngati mmene munthu amaonekera pagalasi limene limasintha kwambiri maonekedwe a munthu