Makolo Anu
Chigawo 6
Makolo Anu
Makolo anu amadziwa zambiri. Nawonso anakhalapo ana ndipo amadziwa mavuto amene amakhalapo panthawi yaunyamata. Choncho, iwo ndi amene angakupatseni malangizo abwino omwe angakuthandizeni pamene muli wachinyamata. Komabe, nthawi zina makolo angawonjezere mavuto m’malo mokuthandizani. Mwachitsanzo, mwina mungakumane ndi mavuto ngati awa:
□ Makolo anu amangokhalira kukudzudzulani.
□ Bambo kapena mayi anu amamwa mowa mwauchidakwa kapena amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.
□ Makolo anu amakangana nthawi zonse.
□ Makolo anu analekana.
M’Mitu 21 mpaka 25 muona zimene mungachite mukamakumana ndi mavuto amenewa.
[Chithunzi chachikulu pamasamba 172, 173]