Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingasangalale Ngakhale Kuti Ndikuleredwa ndi Bambo Kapena Mayi Okha?

Kodi Ndingasangalale Ngakhale Kuti Ndikuleredwa ndi Bambo Kapena Mayi Okha?

Mutu 25

Kodi Ndingasangalale Ngakhale Kuti Ndikuleredwa ndi Bambo Kapena Mayi Okha?

“Mwana amene akuleredwa ndi makolo onse awiri amagona m’chipinda chakechake ndiponso amam’gulira zovala zatsopano. Koma ine ndilibe chipinda chandekha ndipo mayi anga nthawi zambiri sakwanitsa kundigulira zovala zomwe ndimafuna. Ndimangokhala ngati wantchito chifukwa choti ndimagwira ntchito zambiri zapakhomo, amayi ali kuntchito. Ndimaona kuti sindikudyerera ubwana wanga, chifukwa ndilibe ufulu ngati ana ena.”—Anatero Shalonda, mtsikana wazaka 13.

PANYUMBA pamafunika pazikhala makolo onse awiri. Ana amene akuleredwa ndi makolo onse awiri angatsogoleredwe, kutetezedwa ndiponso kuthandizidwa bwino kwambiri. Baibulo limati: “Awiri amaposa mmodzi chifukwa akamachitira zinthu limodzi, zinthu zimayenda bwino.”—Mlaliki 4:9, Today’s English Version.

Ngakhale zili choncho, masiku ano mabanja amene ali ndi makolo onse awiri akucheperachepera. Mwachitsanzo, ana oposa theka pa ana onse ang’onoang’ono a m’dziko la United States, panthawi inayake asanakwanitse zaka 18, adzaleredwa ndi bambo kapena mayi awo okha.

Ngakhale kuti mabanja amene ali ndi makolo onse awiri akucheperachepera, achinyamata ena amachita manyazi chifukwa akuleredwa ndi bambo kapena mayi awo okha. Ndipo ena mwa achinyamata a m’mabanja oterewa amaona kuti ndi opanikizika kwambiri chifukwa cha mavuto amene amakumana nawo. Ngati inuyo muli m’banja lotere, kodi mukukumana ndi mavuto otani? Lembani pamzere uli m’munsiwu vuto limene limakusowetsani mtendere kwambiri.

․․․․․

Ngati mukuleredwa ndi bambo kapena mayi anu okha, kodi zikutanthauza kuti simudzasangalalanso m’moyo wanu wonse? Ayi sichoncho, chifukwa chakuti kukhala wosangalala kapena wosasangalala kwenikweni kumadalira mmene munthu akuonera zinthu pamoyo wake, osati mmene zinthuzo zikumukhudzira. Lemba la Miyambo 15:15 limati: “Masiku onse a wosauka ali oipa; koma wokondwera mtima ali ndi phwando losatha.” Choncho, n’chiyani chingakuthandizeni kukhala “wokondwera mtima” ngakhale kuti mukuleredwa ndi bambo kapena mayi anu okha?

Mungathane ndi Maganizo Olakwika

Choyamba, musakhumudwe ndi zinthu zoipa zimene anthu ena anganene. Mwachitsanzo, aphunzitsi ena amanyoza ana asukulu omwe akuleredwa ndi bambo kapena mayi okha. Ana ena ochokera m’mabanja otere akachita chinthu chinachake choipa, aphunzitsi ena afika mpaka ponena kuti anawo achita zimenezo chifukwa cha mabanja amene akuchokera. Koma dzifunseni kuti: ‘Kodi anthu amene akunena zimenezi amandidziwa bwino komanso mmene banja lathu lilili? Kapena akungonena zimene anamvapo zokhudza mabanja amene muli bambo kapena mayi okha?’

Ndi bwino kudziwa kuti mawu akuti “mwana wamasiye” amapezeka kambirimbiri m’Baibulo ndipo sanawagwiritsepo ntchito monyoza. Ndipotu pafupifupi m’malo onsewo, Yehova anasonyeza kuti amadera nkhawa kwambiri ana amene akuleredwa ndi bambo kapena mayi okha. *

Komabe, palinso anthu ena amene angachite zinthu monyanyira pofuna kusonyeza kuti amakuderani nkhawa. Mwachitsanzo, akamalankhula nanu, angapewe kutchula mawu ngati akuti “bambo,” “ukwati,” “kutha kwa banja,” kapena “imfa,” poopa kukukhumudwitsani kapena kukuchititsani manyazi. Kodi zimenezi zimakusowetsani mtendere? Ngati zili choncho, asonyezeni bwinobwino kuti asamatero. Mwachitsanzo, mnyamata wina wazaka 14 dzina lake Tony, sadziwa bambo ake. Iye ananena kuti anthu ena akamalankhula naye amapewa kutchula mawu enaake. Koma Tony akamalankhula ndi anthu amenewo, amagwiritsa ntchito mawu omwewo, amene anthuwo amapewa. Iye anati: “Ndimafuna kuti adziwe kuti sindichita manyazi chifukwa chakuti ndikuleredwa ndi mayi anga okha.”

Pewani Kuda Nkhawa Kwambiri

Mwachibadwa, mungapwetekedwe mtima chifukwa cha kutha kwa banja la makolo anu kapena imfa ya bambo kapena mayi anu. Komabe, m’kupita kwanthawi muyenera kuvomereza mmene zinthu zilili pamoyo wanu. Ndipo Baibulo limapereka malangizo awa: “Usanene, Kodi bwanji masiku akale anapambana ano?” (Mlaliki 7:10) Pamfundoyi, mtsikana wina wazaka 13 dzina lake Sarah, ndipo banja la makolo ake linatha iye ali ndi zaka 10 anati: “Pewani kuda nkhawa kwambiri ndi zimene zachitikazo. Ndi bwinonso kupewa kuganiza kuti mukukumana ndi mavuto chifukwa chakuti mukuleredwa ndi bambo kapena mayi anu okha, kapena kuganiza kuti ana amene akuleredwa ndi makolo onse awiri ali ndi moyo wopanda mavuto.” Awatu ndi malangizo abwino kwambiri chifukwa nawonso ana amene akuleredwa ndi makolo onse awiri, amakumana ndi mavuto.

Tingayerekezere banja ndi bwato lopalasa. Kuti bwato lotere liyende bwino, pamafunika anthu okwanira olipalasa. Ngati banja lilibe bambo kapena mayi, ndiye kuti lili ngati bwato limene likuperewera munthu mmodzi. Choncho, anthu enawo angafunike kupalasa mwakhama kwambiri kuti bwatolo liyende bwino. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti banja lotere ndi lolephera? Ayi. Ngati anthu enawo atapalasa bwatolo mogwirizana, akhoza kukafika kumene akupita.

Kodi Mukuchitapo Mbali Yanu?

Kodi mungatani kuti muzichita mbali yanu m’banjamo? Taonani mfundo zitatu zotsatirazi:

Phunzirani kugwiritsa ntchito zinthu mosamala. Vuto lalikulu limene limakhalapo m’mabanja ambiri amene alibe bambo kapena mayi ndi lokhudza ndalama. Kodi inuyo mungatani? Tony, yemwe tam’tchula kale uja anati: “Anzanga kusukulu kwathu amauza makolo awo kuti awagulire zovala ndiponso nsapato zapamwamba. Ndipo amakana kupita ku sukulu akapanda kuwagulira. Ine ndilibe zovala zapamwamba, komabe ndimavala zovala zaukhondo ndipo ndimazisamalira bwino. Mayi anga akuyesetsa kundisamalira ndipo sindifuna kuti azivutika kwambiri chifukwa cha ine.” Yesetsani kutsanzira mtumwi Paulo yemwe anati: “Ndaphunzira kukhala wokhutira ndi zimene ndili nazo . . . , m’zinthu zonse ndi m’mikhalidwe yonse.”—Afilipi 4:11, 12.

Mungachitenso bwino kuonetsetsa kuti simukuwononga zinthu zimene muli nazo. (Yohane 6:12) Mnyamata wina dzina lake Rodney anati: “Ndimayesetsa kuti ndisamawononge kapena kuphwanya zinthu, ndiponso sindisiya zinthu paliponse. Ndimachita zimenezi chifukwa chakuti pamafunika ndalama zambiri kukonzetsa zinthu zimene zawonongeka kapena kugulanso zina. Ndipo ndimayesetsa kuthimitsa magetsi ndiponso zipangizo zina zamagetsi zimene sizikugwiritsidwa ntchito. Kuchita zimenezi kumathandiza kuti tisamakhale ndi bilu yaikulu ya magetsi.”

Yambani inuyo kuchitapo kanthu. Abambo kapena amayi ambiri omwe akulera okha ana safuna kuikira anawo malamulo kapena kuwagawira ntchito zapakhomo. Chifukwa chiyani? Ena amaganiza kuti ayenera kufewetsa kwambiri moyo wa ana awo n’cholinga choti asamaganizire za bambo kapena mayi awo amene palibewo. Iwo anganene kuti, ‘Sindikufuna kuti ana anga asamasangalale.’

Mwina inuyo mungasangalale kwambiri bambo kapena mayi anu akamakuchitirani zimenezi. Koma mukamatero, mungathe kungowawonjezera mavuto. Choncho, mungachite bwino kuyamba inuyo kuchitapo kanthu. Taonani zimene Tony ankachita. Iye anati: “Mayi anga amagwira ntchito kuchipatala ndipo yunifomu yawo imafunika kusita. Motero ndimawasitira.” Kodi imeneyi si ntchito ya munthu wamkazi? Tony anati: “Ndi mmenedi ena amaganizira, koma ndimawasitirabe chifukwa choti ndikatero ndimawachepetsera ntchito.”

Chitani zinthu zosonyeza kuti mumawayamikira. Kuwonjezera pa kuwathandiza ntchito zapakhomo, mungawalimbikitse kwambiri mwa kuchita zinthu zosonyeza kuti mumawayamikira. Mayi wina yemwe akulera yekha ana ake anati: “Ndikakhumudwa kwambiri ndi zochitika kuntchito, nthawi zambiri ndimakapeza mwana wanga wamkazi akukonza chakudya chamadzulo kunyumba.” Mayiyu ananenanso kuti: “Ndipo mwana wanga wamwamuna amandikumbatira.” Kodi zimenezi zimam’khudza bwanji mayiyu? Iye anati: “Mavuto onse akuntchito amachoka m’maganizo mwanga ndipo ndimakhalanso wosangalala.”

Pamfundo zitatu zimene taonazi, lembani pamzere uwu mfundo imene mukufuna kuigwiritsa ntchito kwambiri. ․․․․․

Kuleredwa ndi bambo kapena mayi anu okha kungakuthandizeni kuti mukhale munthu wachifundo, wosadzikonda ndiponso wodalirika. Ndipo Yesu anati: “Kupatsa kumabweretsa chisangalalo chochuluka kuposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Choncho, mungakhale munthu wosangalala kwambiri mukamadzipereka kuthandiza bambo kapena mayi anuwo.

N’zodziwikiratu kuti nthawi zina mungamalakelake mutakhala ndi makolo onse awiri. Komabe n’zotheka kukhala wosangalala ngakhale kuti mukuleredwa ndi bambo kapena mayi anu okha. Izi ndi zimene mtsikana wina dzina lake Nia anazindikira. Iye anati: “Bambo anga atamwalira, munthu wina anandiuza kuti, ‘chimene chingakuthandize kuti ukhale wosangalala, ndi mmene ukuonera zinthu pamoyo wako, osati mmene zinthuzo zikukukhudzira.’ Mawu amenewa sindiwaiwala ndipo amandithandiza kuti ndikhale wosangalala.” N’zotheka kuti nanunso mukhale ndi maganizo ngati amenewa. Kumbukirani, kuti mukhale wosangalala sizidalira mmene zinthu zilili pamoyo wanu, koma ndi mmene inuyo mumaonera zinthuzo ndiponso zimene mukuchita.

WERENGANI ZAMBIRI PANKHANIYI M’BUKU LOYAMBA, MUTU 4

[Mawu a M’munsi]

LEMBA LOFUNIKA

“Musasamale zofuna zanu zokha, koma musamalenso zofuna za ena.”—Afilipi 2:4.

MFUNDO YOTHANDIZA

Ngati mukuona kuti bambo kapena mayi anu amakupatsani ntchito zambiri zomwe zimakuvutani kuzikwanitsa, apempheni kuti achite izi:

Alembe ntchito zimene aliyense m’banjamo azichita.

Nthawi zina azigawiranso ena ntchito m’banjamo ngati pakufunika kutero.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Kusamalira zinthu komanso kugwira ntchito zapakhomo kungakuthandizeni kukhwima maganizo mwamsanga kusiyana ndi achinyamata amene akuleredwa ndi makolo onse awiri, omwe kawirikawiri sakhala ndi zochita zambiri pakhomo.

ZOTI NDICHITE

Ndingathane ndi maganizo olakwika mwa kuchita izi: ․․․․․

Anthu ena akamachita zinthu monyanyira poopa kundikhumudwitsa ndidzawauza izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa bambo kapena mayi anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

N’chifukwa chiyani anthu ena amanyoza ana amene akuleredwa ndi bambo kapena mayi awo okha?

N’chifukwa chiyani nthawi zina bambo kapena mayi anu sangakupempheni kuti muwathandize ntchito zapakhomo?

Kodi mungatani kuti musonyeze kuti mumayamikira bambo kapena mayi anu?

[Mawu Otsindika patsamba 211]

“Kuyambira pamene banja la makolo anga linatha, ine ndi mayi anga timapatula nthawi yocheza, ndipo timagwirizana kwambiri.”—Anatero Melanie

[Chithunzi pamasamba 210, 211]

Banja lomwe lilibe bambo kapena mayi, lili ngati bwato lopalasa lomwe likuperewera munthu mmodzi. Choncho, anthu enawo angafunike kupalasa mwakhama kuti bwatolo liyende bwino