Ndingatani Makolo Anga Akamaledzera Kapena Kumwa Mankhwala Osokoneza Bongo?
Mutu 23
Ndingatani Makolo Anga Akamaledzera Kapena Kumwa Mankhwala Osokoneza Bongo?
“Tsiku lina bambo anga anangoti akukakonza galimoto, koma sanabwereko mpaka madzulo. Mayi anga anayesetsa kuwaimbira foni koma sanayankhe. Patapita kanthawi, mayi anaoneka kuti ayamba kuda nkhawa ndipo anakonzeka kuti awatsatire. Iwo anandiuza kuti, ‘Ndikupita kukawayang’ana.’
“Kenako iwo anabwerako ali okha. Ndinawafunsa kuti, ‘Kodi mwawapeza kokonza galimoto kuja?’ ‘Ayi, kulibeko,’ anandiyankha choncho.
“Nditamva zimenezi, ndinadziwa kuti bambo ayambiranso khalidwe lawo lakale, logwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Ndipo nthawi imene ankafika kunyumba n’kuti ine ndi mayi titakhumudwa kwambiri. Ndinangowanyalanyaza mpaka tsiku lotsatira. Panopa, ndimaona kuti ndinalakwa kwambiri kuchita zimenezi.”—Anatero Karen, wazaka 14.
TSIKU ndi tsiku, achinyamata ambiri amakumana ndi mavuto chifukwa choti bambo kapena mayi awo amakonda kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kapena kumwa mowa mwauchidakwa. N’kutheka kuti mumachita manyazi kapena kukhumudwa ngati bambo kapena mayi anu ali ndi khalidwe lotereli.
Mwachitsanzo, bambo a Mary ankaoneka kuti ndi munthu wabwino kwambiri akakhala pagulu. Koma akakhala kwaokha, ankakonda kuledzera ndipo ankachitira nkhanza komanso kutukwana mkazi ndi ana awo. Mary ananena modandaula kuti: “Anthu ankatiuza kuti tili ndi mwayi chifukwa bambo athu ndi munthu wabwino kwambiri.” *
Kodi mungatani ngati bambo kapena mayi anu amakonda kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kapena kumwa mowa mwauchidakwa?
Kodi Chimayambitsa Vutoli N’chiyani?
Choyamba, kudziwa zinthu zina zokhudza vuto lawolo kungakuthandizeni kwambiri. Lemba la Miyambo 1:5 limati: ‘Wozindikira amafikira kuuphungu.’ Choncho, ndi bwino kudziwa zimene zimayambitsa vutoli komanso kuti ndi anthu otani amene angakhale nalo.
Mwachitsanzo, chidakwa si munthu yemwe amangoledzera mwa apo ndi apo, koma ndi munthu yemwe wakhala ndi vuto loledzera kwanthawi yaitali ndipo zikuoneka kuti sangathenso kusiya khalidwe lakelo. * Nthawi zonse amangoganizira za mowa moti akayamba kumwa safuna kusiya. Khalidweli limayambitsa mavuto aakulu m’banja mwake ndi kuntchito ndipo iye angathenso kudwala nalo.
Ngakhale kuti anthu ena amakhala zidakwa chifukwa choti poyamba ankangokonda kuledzera basi, ena vutoli limayambira m’maganizo mwawo. Ndipotu anthu ambiri amayamba kumwa Miyambo 14:13) Komanso ena mwa iwo analeredwa ndi makolo omwe anali zidakwa. Anthu ngati amenewa angayambe kumwa mowa kuti aiwale mavuto amene ankakumana nawo ali ana. Ena amayamba kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo pazifukwa ngati zomwezi.
mowa mwauchidakwa chifukwa choti sasangalala komanso alibe chiyembekezo chilichonse m’moyo. (Komabe, kumwa mowa kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo kumangowonjezera mavuto, chifukwa chakuti kumasokoneza maganizo kwambiri. N’chifukwa chake bambo kapena mayi anuwo akufunika kuthandizidwa ndi dokotala kuti asiye khalidwe limeneli.
Onani Zinthu M’njira Yoyenera
N’zoona kuti kudziwa zimene zinachititsa bambo kapena mayi anu kuti akhale chidakwa kapena kuti azigwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, sikungathetse vutolo. Komabe, zimenezi zingakuthandizeni kuti muziwamvera chisoni chifukwa cha vuto lawolo.
Tiyerekezere kuti bambo kapena mayi anu atchoka mwendo. Kodi mukuganiza kuti mungasewere nawo mpira wamiyendo? Kodi mungamve bwanji mutadziwa kuti iwo anavulala chifukwa chochita zinthu mosasamala? N’zodziwikiratu kuti mungakhumudwe kwambiri. Komabe, mungadziwe kuti iwo sangathe
kusewera nanu mpira mpaka atachira. Kumvetsa mfundo imeneyi kungakuthandizeni kuti muziona zinthu moyenera.Mofanana ndi zimenezi, bambo kapena mayi omwe amamwa mowa mwauchidakwa kapena amakonda kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, amakhala osokonezeka maganizo. N’zoona kuti mavutowo anawaputa okha ndipo mwina inuyo mumadana ndi khalidwe lawo loipalo. Komabe, iwo sangathe kukusamalirani bwinobwino mpaka atathandizidwa kuti asiye khalidwelo. Choncho, ndi bwino kuwaona ngati munthu wovulala, chifukwa zingakuthandizeni kuti musamayembekezere kuti azikuchitirani chilichonse chimene mukufuna.
Zimene Mungachite
Dziwani kuti, panopa muzivutikabe ndi khalidwe lawolo, pokhapokha iwo atalisiya. Ndiyeno panopa mungachite chiyani?
Musawachirikize pakhalidwe lawolo. Lemba la Agalatiya 6:5 limati: “Aliyense ayenera kunyamula katundu wakewake.” Choncho, bambo kapena mayi anuwo akufunika kunyamula okha katundu wa zimene akuchitazo. Si udindo wanu kuwathetsera vutolo kapena kuwateteza ku mavuto amene angabwere chifukwa cha zochita zawozo. Mwachitsanzo, bambo kapena mayi anuwo akalephera kupita kuntchito chifukwa choledzera, simufunika kuwathandizira ponamiza abwana awo, ndiponso akaledzera kwambiri n’kumangogona paliponse, muzingowasiya.
Alimbikitseni kuti apeze anthu oti awathandize. N’kutheka kuti vuto lalikulu limene bambo kapena mayi anuwo ali nalo ndilo kulephera kuvomereza kuti ali ndi vuto. Ngati bambo anu ndi amene ali chidakwa, mwina zingathandize kuti mayi anu pamodzi ndi achibale anu akuluakulu awafotokozere mmene mukuvutikira ndi khalidwe lawolo. Angawafotokozerenso zimene angachite kuti athetse vutolo. Bambo angachitenso zimenezi ngati mayi ndi amene ali chidakwa.
Komanso, bambo kapena mayi anu amene ali ndi vutoli angachite bwino kuyankha mafunso otsatirawa: Kodi n’chiyani chingachitikire ineyo komanso banja langa ndikapitiriza khalidweli? Nanga n’chiyani chingachitike nditasiya? Kodi ndichite chiyani kuti anthu ena andithandize?
Ngati mukuona kuti zinthu ziipa, chokanipo. Lemba la Miyambo 17:14 limati: “Kupikisana kusanayambe tasiya makani.” Choncho, pewani kukangana nawo. Ngati n’kotheka, pitani ku chipinda kwanu kapena kunyumba kwa mnzanu. Mukaona kuti pangachitike zachiwawa, mungachite bwino kupempha anthu ena kuti akuthandizeni.
Musadziimbe mlandu. Achinyamata ena amadziimba mlandu chifukwa chakuti sagwirizana ndi bambo kapena mayi awo amene amaledzera kapena kumwa mankhwala osokoneza bongo. Sizachilendo kuganiza choncho, makamaka ngati khalidwe lawolo likuwalepheretsa kukukondani komanso kukusamalirani. Aefeso 6:2, 3) Koma mawu akuti ‘kulemekeza’ akutanthauza kuwapatsa ulemu chifukwa cha udindo wawo, ngati mmene mungalemekezere wapolisi kapena woweruza milandu. Sakutanthauza kuti muzisangalala ndi khalidwe lawolo. (Aroma 12:9) Ndiponso, ngati mukudana ndi khalidwelo, sizingatanthauze kuti ndinu munthu woipa, ndipotu palibe amene angasangalale ndi chidakwa kapena munthu amene amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo.—Miyambo 23:29-35.
N’zoona kuti Baibulo limati muzilemekeza makolo. (Muzicheza ndi anthu amene angakulimbikitseni. Panyumba panu pakakhala mavuto, mungaiwale mmene moyo uyenera kukhalira. Choncho, ndi bwino kuti muzicheza ndi anthu akhalidwe labwino komanso amene amakonda zinthu zauzimu. Abale ndi alongo anu achikhristu angakulimbikitseni ndiponso angakuthandizeni kuti mupezeko mpumulo. (Miyambo 17:17) Kucheza ndi mabanja achikhristu kungakuthandizeni kukhala ndi chithunzi chabwino cha mmene banja liyenera kukhalira.
Nanunso pemphani anthu ena kuti akuthandizeni. Kucheza ndi munthu wamkulu wodalirika amene mungamuuze zakukhosi Yesaya 32:2) Choncho, musawaope kapena kuchita nawo manyazi mukafuna kuti akulimbikitseni ndiponso kuti akupatseni malangizo.
kwanu kungakuthandizeni kwambiri. Akulu mumpingo wachikhristu ndi ofunitsitsa kukuthandizani. Baibulo limati iwo ali ngati “pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.” (Pamfundo 6 zimene takambiranazi, lembani pamzere uwu mfundo imodzi imene mukufuna kuigwiritsa ntchito koyamba. ․․․․․
Mwina zochita zanu sizingathandize kusintha zinthu kuti zikhale bwino kunyumba kwanu, koma mungachite zinthu zimene zingathandize kuti musasowe mtendere kwambiri. M’malo moyesa kuletsa bambo kapena mayi anu kumwa mowa mwauchidakwa kapena kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, yesetsani kuchita zinthu zimene zingakuthandizeni inuyo. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pitirizani kukonza chipulumutso chanu.” (Afilipi 2:12) Kuchita zimenezi kungakuthandizeni kuti musamadandaule kwambiri ndipo mwina kungalimbikitse bambo kapena mayi anuwo kupempha anthu ena kuti awathandize kusiya khalidwe lawolo.
Kodi mungatani ngati mumaona kuti makolo anu amangokhalira kukangana? Kodi mungachite chiyani kuti mupirire zimenezo?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 7 Ngati mukuzunzidwa ndi bambo kapena mayi amene amaledzera, mungachite bwino kuuza munthu wina wachikulire amene mumam’khulupirira kwambiri kuti akuthandizeni. Ngati ndinu wa Mboni za Yehova, mungauze mkulu mumpingo kapena Mkhristu wina wachikulire.
^ ndime 11 Akazinso angathe kukhala ndi vuto limeneli.
LEMBA LOFUNIKA
“Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo.”—Miyambo 19:11.
MFUNDO YOTHANDIZA
M’malo modana ndi bambo kapena mayi anuwo, yesetsani kudana ndi khalidwe lawo loipalo.—Miyambo 8:13; Yuda 23.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
M’Baibulo mawu akuti “lemekeza” angatanthauze kuzindikira udindo wa munthu wina. (Aefeso 6:1, 2) Choncho, kulemekeza makolo sikutanthauza kuti nthawi zonse muzigwirizana ndi khalidwe lawo.
ZOTI NDICHITE
Bambo kapena mayi anga akamalalata kapena kuchita ndewu, ndizichita izi: ․․․․․
Kuti ndilimbikitse bambo kapena mayi anga kupeza munthu woti awathandize, ndidzachita izi: ․․․․․
Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․
MUKUGANIZA BWANJI?
● N’chiyani chimachititsa anthu ena kukhala zidakwa kapena kuyamba kumwa mankhwala osokoneza bongo?
● N’chifukwa chiyani simuyenera kudziimba mlandu ngati bambo kapena mayi anu ali ndi khalidwe limeneli?
● Ngati bambo kapena mayi anu ali ndi khalidwe limeneli, kodi ndi mbali ziti zimene inuyo mungasinthe pamoyo wanu, ndipo mungasinthe motani?
[Mawu Otsindika patsamba 192]
“Sindikukayikira kuti makolo anga adzandichititsanso manyazi chifukwa cha khalidwe lawo, koma ndikudziwa kuti ndikadalira Yehova, iye adzandithandiza kupirira.”—Anatero Maxwell
[Bokosi patsamba 198]
Bambo Kapena Mayi Anu Akasiya Kutumikira Yehova
Kodi mungatani ngati bambo kapena mayi anu asiya kutsatira mfundo za m’Baibulo, mwinanso n’kufika ponena kuti sakufunanso kukhala wa Mboni za Yehova?
● Dziwani kuti Yehova sangakuimbeni mlandu wa zochita zawozo. Baibulo limati: “Aliyense wa ife adzadziyankhira yekha [mlandu] kwa Mulungu.”—Aroma 14:12.
● Musamadziyerekezere ndi achinyamata ena omwe zinthu zikuwayendera bwino pamoyo wawo. (Agalatiya 5:26) Mnyamata wina amene bambo ake anathawa banja lawo anati, “M’malo momangoganizira zimene zinachitikazo, zimakhala bwino kwambiri kuganizira zimene ungachite ndi vutolo.”
● Pitirizani kulemekeza bambo kapena mayi anu omwe asiya kutumikira Yehovawo, ndipo muziwamvera ngati zimene iwo akukuuzani kuti muchite sizikutsutsana ndi zofuna za Mulungu. Yehova amafuna kuti muzilemekeza makolo anu, kaya iwo amamutumikira kapena ayi. (Aefeso 6:1-3) Mukamalemekeza ndiponso kumvera makolo anu mosaganizira zolakwa zawo mumasonyeza kuti mumakonda Yehova.—1 Yohane 5:3.
● Muzisonkhana mokhazikika ndi mpingo wachikhristu ndiponso muzicheza kwambiri ndi abale ndi alongo. Zimenezi zingakulimbikitseni mwauzimu. (Maliko 10:30) Mnyamata wina dzina lake David ankaganiza kuti iye ndi abale ake azisalidwa ndi abale ndi alongo a mumpingo wachikhristu, chifukwa chakuti bambo ake anasiya kutumikira Yehova. Koma David anapeza kuti maganizo akewo sanali oona. Iye anati: “Anthu mumpingo sankationa ngati achabechabe. Zimenezi zinandithandiza kuona kuti amatikonda kwambiri.”
[Chithunzi patsamba 194]
Kuona bambo kapena mayi anuwo ngati munthu wovulala kungakuthandizeni kuti musamawayembekezere kuchita zinthu zimene sangathe