Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Sindifuna Kulakwitsa Chilichonse?

N’chifukwa Chiyani Sindifuna Kulakwitsa Chilichonse?

Mutu 27

N’chifukwa Chiyani Sindifuna Kulakwitsa Chilichonse?

Kodi mumakhumudwa mukakhala kuti simunakhoze zonse pamayeso?

□ Inde

□ Ayi

Kodi mumadziona kuti ndinu wolephera munthu wina akakudzudzulani?

□ Inde

□ Ayi

Kodi mumalephera kucheza ndi anzanu chifukwa mumawaona kuti ndi otsalira?

□ Inde

□ Ayi

NGATI mwayankha kuti inde funso limodzi kapena angapo, ndiye kuti mwina muli ndi vuto losafuna kulakwitsa chilichonse. Koma mungafunse kuti, ‘Kodi kukhala ndi mtima wofuna kuchita zinthu mosalakwitsa n’kulakwa?’ Ayi sikulakwa, ndipotu Baibulo limayamikira munthu “waluso pantchito yake.” (Miyambo 22:29, NW) Komabe munthu amene ali ndi vuto losafuna kulakwitsa chilichonse, amachita zinthu mowonjeza.

Mwachitsanzo, mnyamata wina wazaka 19, dzina lake Jason, anati: “Nditatsala pang’ono kumaliza sukulu, ndinkaona kuti ngati sindikhoza zonse pamayeso, ndiye kuti ndine mbuli. Panthawiyi ndinkaphunziranso kuimba piyano ndipo ndinkafuna kuti ndiziimba ngati katswiri ngakhale kuti ndinali nditangoyamba kumene.”

Nthawi zambiri anthu amene safuna kulakwitsa zinthu sapita patsogolo pazinthu zauzimu. Mwachitsanzo, taganizirani za wachinyamata amene nthawi zonse anthu amamuyamikira kuti amachita bwino zinthu. Iye angamayesetse kuti asalakwitse chilichonse. N’zoona kuti wachinyamata akakhala chitsanzo chabwino, achinyamata ena ndiponso achikulire mumpingo amapindula. Komabe, kuyesetsa kuchita zinthu mosalakwitsa kungachititse wachinyamata kuti asamatumikire Mulungu mosangalala. Wachinyamata wotere ayenera kuthandizidwa. Koma mwina iye sangapemphe thandizo chifukwa choopa kuti akhumudwitsa anthu amene amamuyamikira. Mwinanso anganyanyale chifukwa choganiza kuti, ‘Palibe chifukwa chopitirizira, chifukwa ndikungolephera chilichonse.’

Mmene Mungathetsere Vutoli

Anthu amene safuna kulakwitsa chilichonse, amaganiza kuti munthu safunika kulakwitsa ngakhale pang’ono. Koma maganizo amenewa si olondola. Baibulo limanena momveka bwino kuti: ‘Anthu onse ndi ochimwa ndipo ndi operewera pa ulemerero wa Mulungu.’ (Aroma 3:23) Choncho, n’zosatheka kuti munthu achite zinthu mosalakwitsa kalikonse. Ndiponso munthu amene amaganiza kuti angachite zinthu mosalakwitsa ali ngati munthu amene amaganiza kuti angathe kungodumpha m’mwamba n’kuyamba kuuluka. Izi n’zosatheka ngakhale munthu atazikhulupirira chotani.

Kodi mungatani ngati muli ndi vuto lofuna kuchita zinthu molakwitsa? Gwiritsani ntchito mfundo zotsatirazi:

Pewani mpikisano. Kuyesetsa kuti muzichita zinthu kuposa wina aliyense ndi kungodzivuta. Baibulo limati kuchita zimenezi ndi “kungosautsa mtima.” (Mlaliki 4:4) Mfundo ndi yakuti, kupikisana ndi ena kulibe phindu. Ndipo ngakhale munthu atachitadi zinthu zoposa ena, sipapita nthawi yaitali pasanapezeke munthu winanso wom’posa. Munthu amene amachita bwino zinthu, sapikisana ndi ena koma amangoyesetsa kuchita zimene angathe.Agalatiya 6:4.

Musalimbane ndi zinthu zosatheka. Muzidziwa zinthu zimene mungathe kuchita ndi zimene simungathe ndipo muzilimbikira kuchita zimene mungathezo. Munthu amene amalimbikira kuchita zimene sangathe, tingati ndi wodzitukumula kapena wonyada. Mtumwi Paulo anapereka malangizo abwino kwambiri pankhani imeneyi. Iye anati: “Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire koposa mmene muyenera kudziganizira.” (Aroma 12:3) Choncho musamalimbane ndi zinthu zosatheka. Ganiziraninso bwino zinthu zimene mungathe kuchita. Kenako chitani zonse zimene mungathe ndipo musadandaule ngati mukulakwitsa pena ndi pena.

Musamakhumudwe mukalakwitsa. Yesani kuchita zinthu zatsopano monga kuphunzira kugwiritsira ntchito zida zoimbira. Koma chifukwa chakuti mukuphunzira, simungalephere kulakwitsa ndipo musakhumudwe ndi zimenezi. Baibulo limati pali “mphindi yakuseka.” (Mlaliki 3:4) Choncho mungathe kumadziseka mukalakwitsa. Zimenezi zidzakuthandizani kumvetsa mfundo yakuti, munthu amaphunzira bwino akamalakwitsa. Komabe tikalakwitsa zinthu, mwachibadwa timakhumudwa. Motero, kuti musamakhumudwe kwambiri, muzipewa kumangoganizira za zolephera zanuzo.

Dziwani kuti Yehova sayembekezera kuti tizichita zinthu mosalakwitsa. Iye amangofuna kuti tikhale okhulupirika basi. (1 Akorinto 4:2) Mukamayesetsa kukhala wokhulupirika, mungathe kukhala wosangalala ndi zimene mukukwanitsa kuchita ngakhale kuti mungamalakwitse zinthu zina ndi zina.

M’MUTU WOTSATIRA

Masiku ano anthu ambiri amaganiza kuti kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha sikulakwa. Kodi mungapewe bwanji khalidwe limeneli? Nanga mungatani ngati mumalakalaka kugonana ndi mwamuna kapena mkazi mnzanu?

LEMBA LOFUNIKA

“Kulibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa.”—Mlaliki 7:20.

MFUNDO YOTHANDIZA

Ganizirani ntchito inayake imene munaisiyira panjira chifukwa choopa kuti simuikwanitsa. Ndiyeno dziikireni nthawi yoti mudzaimalizitse.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Yehova salakwitsa kalikonse, komabe iye sayembekezera kuti anthu azichita zinthu mosalakwitsa kalikonse. Iye amangofuna kuti tizichita zimene tingathe.

ZOTI NDICHITE

Ndikamangodziimba mlandu ndizichita izi: ․․․․․

Ndikamadandaula kwambiri chifukwa cha zimene ena alakwitsa ndizichita izi: ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․

MUKUGANIZA BWANJI?

● Kodi ndi zinthu ziti zimene mumafuna kuchita popanda kulakwitsa chilichonse?

● Kodi ndi malemba ati m’Baibulo amene amasonyeza kuti Yehova Mulungu sayembekezera kuti atumiki ake azichita zinthu popanda kulakwitsa kalikonse?

● Kodi mtima wosafuna kulakwitsa kalikonse ungachititse bwanji kuti anthu asamafune kucheza nanu?

● Kuyambira panopo, kodi muzichita chiyani mukalakwitsa zinazake?

[Mawu Otsindika patsamba 226]

“Munthu amene amayesetsa kuchita zinthu zimene angathe ndi wosiyana ndi munthu amene ali ndi vuto losafuna kulakwitsa zinthu.”—Anatero Megan

[Bokosi patsamba 228]

Mtima Wosafuna Kulakwitsa Ungakulepheretseni Kukhala ndi Anzanu

Kodi simufuna kucheza ndi anthu ena chifukwa choti sachita bwino zinthu mmene inuyo mumafunira? Kapena kodi anzanu ena safuna kucheza nanu chifukwa choti mumakhwimitsa zinthu? Baibulo limati: “Usapambanitse kukhala wolungama; usakhale wanzeru koposa; bwanji ufuna kudziwononga wekha?” (Mlaliki 7:16) Munthu amene amafuna kuchita chilichonse mosalakwitsa amadziwononga yekha posafuna kucheza ndi anthu omwe mwina angakhale anzake abwino. Mtsikana wina dzina lake Amber, anati: “Palibe amene angasangalale kucheza ndi anthu amene amakutenga ngati wachabechabe. Ndipo ndaonapo anthu ena osafuna kulakwitsa zinthu akudana ndi anzawo apamtima pazinthu zazing’ono.”

[Chithunzi patsamba 229]

Munthu amene ali ndi vuto losafuna kulakwitsa zinthu ali ngati munthu amene amaganiza kuti angathe kungodumpha m’mwamba n’kuuluka