Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangokhalira Kumvetsera Nyimbo?
Mutu 31
Kodi Ndingatani Kuti Ndisamangokhalira Kumvetsera Nyimbo?
Kodi kumvetsera nyimbo n’kofunika motani kwa inu?
□ Ndingathe kukhala osamvetsera nyimbo.
□ Sindingathe kukhala osamvetsera nyimbo.
Kodi mumamvetsera nyimbo nthawi yanji?
□ Ndikakhala paulendo
□ Powerenga
□ Nthawi zonse
Kodi mumakonda nyimbo zotani, ndipo n’chifukwa chiyani?
ANTHUFE mwachibadwa timakonda nyimbo. Ndipo achinyamata ambiri sangathe kukhala osamvetsera nyimbo. Mwachitsanzo, mtsikana wina wazaka 21, dzina lake Amber, anati: “Sindingathe kukhala osamvetsera nyimbo. Ndimamvetsera nyimbo pokonza m’nyumba, pophika, akandituma kwinakwake kapena powerenga.”
Sikuti nyimbo zimangosangalatsa kumvetsera koma zimakhudzanso mmene timaganizira. Baibulo limati: ‘Mawu a pa nthawi yake ndi abwino.’ (Miyambo 15:23) Choncho kumvetseranso nyimbo pa nthawi yoyenera kumakhazika mtima pansi. Mtsikana wina wazaka 16, dzina lake Jessica, anati: “Nthawi zina ndimaona kuti palibe amene akundimvetsa. Koma ndikangomvetsera nyimbo zimene ndimakonda, ndimadziwa kuti si ine ndekha amene ndimakhumudwa.”
Kodi Makolo Anu Amasangalala ndi Nyimbo Zimene Mumamvetsera?
N’kutheka kuti makolo anu sasangalala ndi nyimbo zimene mumamvetsera. Mnyamata wina anati: “Ndikamamvetsera nyimbo, bambo anga amandiuza kuti, ‘Tatseka nyimbo zakozo zikundiboola m’makutu.’” Chifukwa chotopa ndi kukalipidwa, mwina mungaone kuti makolo anu akukokomeza zinthu. Mtsikana wina anati: “Kodi iwowa ali ana, sankamvetseranso nyimbo zimene makolo awo ankadana nazo?” Mtsikana winanso wazaka 16, dzina lake Ingred, anati: “Akuluakulu amakakamira zinthu zakale. Zingakhale bwino atamadziwa kuti anafe tili ndi nyimbo zathu zimene timakonda.”
Apa Ingred sakunama. Kwazaka zambiri, achinyamata ndi akuluakulu akhala asakugwirizana chifukwa choti amakonda zinthu zosiyana. Koma zimenezi sizikupereka ufulu woti achinyamata ndi akuluakulu azikangana
chifukwa cha nyimbo. Kuti musamayambane ndi makolo anu pankhani ya nyimbo, muzisankha nyimbo zimene makolo anu sadana nazo. Ngati makolo anu amakonda Mulungu, ndiye kuti muli ndi mwayi waukulu. Zili choncho chifukwa chakuti Mawu a Mulungu angakuthandizeni inuyo ndiponso makolo anu kudziwa zinthu zoyenera ndiponso zosayenera. Kuti mudziwe nyimbo zoyenera, ganizirani mfundo ziwiri zofunika kwambiri izi: (1) Uthenga wa nyimbo zimene mukumvetsera ndiponso (2) kuchuluka kwa nthawi imene mukuthera pomvetsera nyimbo. Choyamba tiyeni tikambirane mfundo yotsatirayi.Uthenga wa Nyimbo Zimene Mumamvetsera
Nyimbo zili ngati chakudya. Chakudya chabwino mukachidya pa mlingo woyenerera, chingakuthandizeni. Koma chakudya choipa chingakuvulazeni ngakhale mutachidya pang’ono. Koma chodabwitsa n’chakuti nyimbo zoipa ndi zimene zimasangalatsa kwambiri. Mnyamata wina dzina lake Steve anati: “N’chifukwa chiyani nyimbo zonse zabwino zimakhala ndi mawu oipa?”
Ngati munthu umakonda nyimbo inayake, kodi uthenga wake uli ndi vuto lililonse? Kuti muyankhe funsoli dzifunseni kuti: ‘Ngati munthu wina atafuna kundiikira poizoni mu Yobu 12:11) Choncho m’malo mongomvetsera nyimbo chifukwa choti mumaikonda, ‘yesani mawu ake.’ Mungachite zimenezi mwa kuona mutu wa nyimboyo ndiponso uthenga wake. Izi n’zofunika chifukwa mawu a mu nyimboyo angathe kusintha khalidwe ndi maganizo anu.
chakudya, kodi angandiikire m’chakudya chokoma kapena chosakoma?’ Munthu wokhulupirika Yobu anafunsa kuti: ‘Kodi m’khutumu simuyesa mawu, monga m’kamwa mulawa chakudya chake?’ (N’zokhumudwitsa kuti masiku ano nyimbo zambiri zili ndi uthenga wonena za kugonana, chiwawa, ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Ngati mukuganiza kuti palibe vuto ndi kumvetsera nyimbo zotere ndiye kuti poizoni wayamba kale kugwira ntchito m’thupi mwanu.
Muzisankha Nokha Zochita
Anzanu angakukopeni kuti muzimvetsera nyimbo zoipa. Komanso anthu oimba angakukopeni kuti muzikonda nyimbo zawo. Mawailesi, Intaneti, ndi TV zachititsa kuti bizinesi ya nyimbo ikhale ya ndalama zambiri. Akatswiri azamalonda amalembedwa ntchito n’cholinga chakuti akope anthu kuti ayambe kumvetsera nyimbo zinazake.
Mukalola kuti anzanu kapena mawailesi, Intaneti, ndi TV zikulandeni ufulu wanu wosankha nyimbo zimene mukufuna kumvetsera, mumakhala ngati kapolo amene alibe ufulu wosankha yekha zochita. (Aroma 6:16) Baibulo limatichenjeza kuti tisamatengere nzeru za dongosolo lino. (Aroma 12:2) Choncho, muyenera kuphunzitsa ‘luntha lanu kuti muzisiyanitsa choyenera ndi cholakwika.’ (Aheberi 5:14) Kodi mungagwiritse ntchito bwanji luntha lanu posankha nyimbo? Onani mfundo zotsatirazi:
Werengani mawu a pachikuto. Mawu amene alembedwa pa chikuto cha nyimbo angakuthandizeni kudziwa ngati nyimboyo ndi yabwino kapena ayi. Ngati nyimbo ili ndi zachiwawa, zachiwerewere, kapena zamizimu pachikuto chake, ndiye kuti ndi yoipa.
Mvetserani mawu ake. Kodi mawu a m’nyimboyo ndi otani? Kodi mukufunadi kuti muzimvetsera mawu amenewo nthawi zonse? Kodi uthenga wa m’nyimboyo ndi wogwirizana ndi mfundo zachikhristu zimene mumatsatira?—Aefeso 5:3-5.
Onani mmene nyimboyo ikukukhudzirani. Wachinyamata wina dzina lake Philip, anati: “Ndinaona kuti nyimbo zambiri zimene ndinkamvetsera zinkandichititsa kuti ndikhale wokhumudwa.” N’zoona kuti nyimbo zingakhudze anthu mosiyanasiyana. Koma kodi nyimbo 1 Akorinto 15:33.
zimene mumamvetsera zimakukhudzani bwanji inuyo? Dzifunseni kuti: ‘Ndikamvetsera nyimbo inayake, kodi ndimayamba kuganizira zinthu zoipa? Kodi ndayamba kulankhula mawu ena osayenera a m’nyimboyo?’—Muziganizira ena. Kodi makolo anu amasangalala ndi nyimbo zimene mumamvetsera? Afunseni maganizo awo. Ganiziraninso ngati Akhristu anzanu angasangalale ndi nyimbozo. Kodi Akhristu ena angakhumudwe nazo? Kuchita zinthu moganizira ena, ndi umboni wakuti mukukula.—Aroma 15:1, 2.
Mafunso amene ali pamwambawa angakuthandizeni kusankha nyimbo zosangalatsa, zomwe sizingasokoneze moyo wanu wauzimu. Palinso mfundo ina yofunika kuiganizira.
Kodi Ndizimvetsera Nyimbo Nthawi Yochuluka Bwanji?
Nyimbo zabwino zili ngati chakudya chabwino monga uchi. Komabe, mwambi wina umachenjeza kuti: “Wapeza uchi kodi? Idyapo wokwanira, kuti ungakukole, nusanze.” (Miyambo 25:16) Uchi ndi wabwino ndipo ena amanena kuti umachiritsa matenda. Komabe, kudya uchi wambiri kungakuvulazeni. Apa mfundo ndi yakuti, ngakhale chinthu chabwino chitha kutivulaza ngati titachichita mopitirira malire.
Komabe achinyamata ena amangokhalira kumvetsera nyimbo. Mwachitsanzo, Jessica yemwe tamutchula kale uja, anati: “Ndimamvetsera nyimbo nthawi zonse, ngakhale pamene ndikuwerenga Baibulo. Ndimawauza makolo anga kuti nyimbo zimandithandiza kumvetsa zimene ndikuwerenga. Koma iwo amatsutsa zimenezi.” Kodi inunso mumachita zimenezi?
Kodi mungadziwe bwanji kuti mukumvetsera nyimbo mopitirira malire? Dzifunseni mafunso otsatirawa:
Kodi patsiku ndimamvetsera nyimbo nthawi yochuluka bwanji? ․․․․․
Kodi pamwezi nyimbo zimandiwonongera ndalama zochuluka bwanji? ․․․․․
Kodi nyimbo zikundilepheretsa kucheza ndi anthu a m’banja lathu? Ngati ndi choncho, lembani pansipa zimene mungachite kuti muchepetse vutoli. ․․․․․
Chepetsani Nthawi Imene Mumamvetsera Nyimbo
Ngati kumvetsera nyimbo kukukuwonongerani nthawi yambiri, mungachite bwino kudziikira malire. Mwachitsanzo, mwina mungafunikire kusiya chizolowezi choika mahedifoni m’makutu tsiku lonse, kapena chizolowezi chotsegula nyimbo mukangofika panyumba.
Komanso, ndi bwino nthawi zina kungokhala duu osamvetsera chilichonse. Zimenezi zingakuthandizeni pa maphunziro anu. Steve amene tinamutchula uja, anati: “Ukamawerenga utatseka nyimbo umamvetsa zimene ukuwerengazo.” Kuti mutsimikizire zimenezi, yesani kuwerenga mutatseka nyimbo.
Mufunikiranso kukhala ndi nthawi yowerenga Baibulo ndi mabuku onena za Baibulo. Nthawi zina, Yesu Khristu Maliko 1:35) Kodi inunso mumawerengera pamalo aphee, opanda phokoso? Ngati simuchita zimenezi, n’zovuta kuti mukule mwauzimu.
ankakhala kumalo aphee kuti apemphere ndi kusinkhasinkha. (Muzisankha Mwanzeru
Nyimbo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, koma muyenera kusamala kuti zisakusokonezeni. Musakhale ngati mtsikana wina dzina lake Marlene, amene anati: “Ndili ndi nyimbo zimene ndikuona kuti ndiyenera kuzitaya, koma ndimazikonda kwambiri.” Dziwani kuti mtsikanayu akuwononga maganizo ake komanso makhalidwe ake chifukwa cha nyimbo zoipazi. Pewani zimenezi, ndipo musalole kuti nyimbo zikusokonezeni maganizo. Yesetsani kutsatira mfundo zachikhristu posankha nyimbo. Ndiponso muzipemphera kuti Mulungu akuthandizeni ndi kukutsogolerani. Ndipo muzicheza ndi anthu amene amakonda Mulungu ngati inuyo.
Nyimbo zingakukhazikeni mtima pansi. Zingakuthandizeninso ngati mukusowa munthu wocheza naye. Koma sizingathetse mavuto anu. Ndipotu nyimbo sizingalowe m’malo mwa anzanu. Choncho, musamangokhalira kumvetsera nyimbo. Kumvetsera nyimbo sikulakwa koma musamamvetsere mopitirira malire.
Nthawi zina mumafunika kusangalala. Kodi mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni bwanji kuti muzisangalala moyenerera?
LEMBA LOFUNIKA
‘Kodi m’khutumu simuyesa mawu, monga m’kamwa mulawa chakudya chake?’—Yobu 12:11.
MFUNDO YOTHANDIZA
Ngati mukufuna kuti makolo anu amvetse chifukwa chimene mumakondera nyimbo kapena gulu linalake loimba, yambani inuyo kukonda zina mwa nyimbo zimene iwowo amazikonda.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
Ngati simufuna kuti makolo anu amvetsere nyimbo zimene mumakonda, ndiye kuti nyimbozo si zabwino.
ZOTI NDICHITE
Kuti ndichepetse kumvetsera kwambiri nyimbo, ndizichita izi: ․․․․․
Anzanga akandiuza kuti ndimvetsere nyimbo zosayenera, ndiziwayankha izi: ․․․․․
Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: ․․․․․
MUKUGANIZA BWANJI?
● N’chifukwa chiyani muyenera kusamala ndi nyimbo zimene mumamvetsera?
● Kodi mungadziwe bwanji kuti nyimbo inayake ndi yabwino kapena ayi?
● Kodi mungatani kuti muzikonda nyimbo zosiyanasiyana?
[Mawu Otsindika patsamba 259]
“Nthawi zina ndimangopezeka kuti ndikumvetsera nyimbo zimene ndikuona kuti si zabwino. Ndipo nthawi yomweyo ndimazitseka. Ndikapanda kutseka, ndimayamba kuziona kuti ndi zabwino.”—Anatero Cameron
[Bokosi/Zithunzi patsamba 258]
Musamangomvetsera Nyimbo za Mtundu Umodzi
Kodi masiku ano mumakonda zakudya zosiyanasiyana kuposa zimene munkakonda muli wamng’ono? Munthu akamakula amayamba kukonda zakudya zosiyanasiyana. N’chimodzimodzinso ndi nyimbo. Musamangomvetsera nyimbo za mtundu umodzi. Yesani kumvetsera nyimbo zosiyanasiyana.
Kuti muchite zimenezi, phunzirani kugwiritsa ntchito zida zoimbira. Zimenezi n’zovuta koma ndi zopindulitsa chifukwa zingakuthandizeni kuti muzikonda nyimbo zosiyanasiyana. Kodi nthawi yochitira zimenezi mungaipeze kuti? Mungachepetse nthawi imene mumaonera TV kapena kuchita masewera a pakompyuta. Tamvani zimene achinyamata ena anena.
“Kugwiritsa ntchito zida zoimbira n’kosangalatsa kwambiri ndipo ndi njira yabwino yosonyeza zimene zili mumtima mwako. Kuphunzira kuimba nyimbo zatsopano kwandithandiza kuti ndiyambe kukonda nyimbo zosiyanasiyana.”—Anatero Brian, wazaka 18, yemwe amadziwa kuimba gitala, ng’oma ndi piyano.
“Kuti munthu aphunzire kuimba bwino chida chinachake, amafunikira kuchita khama. Nthawi zina kuphunzira sikusangalatsa. Koma ukakwanitsa kuimba bwino nyimbo inayake, umasangalala kwambiri.”—Anatero Jade, wa zaka 13, amene amadziwa kuimba gitala.
“Ndikakhumudwa kapena ndikakhala ndi vuto linalake, ndimaimba gitala ndipo ndimamva bwino. Ndikaimba nyimbo yabwino, ndimasangalala ndipo mtima wanga umakhala m’malo.”—Anatero Vanessa, wazaka 20, amene amadziwa kuimba gitala, piyano ndi chitoliro.
“Poyamba ndinkaganiza kuti sindingathe kuimba ngati mmene anthu ena amaimbira. Koma sindinasiye kuphunzira. Panopa ndimasangalala ndikaimba bwino nyimbo. Komanso ndimatha kuzindikira luso limene oimba ena ali nalo.”—Anatero Jacob, wazaka 20, amene amadziwa kuimba gitala.
[Chithunzi patsamba 255]
Nyimbo zili ngati chakudya. Chakudya chabwino mukachidya pa mlingo woyenerera, chingakuthandizeni. Koma chakudya choipa ngakhale mutachidya pang’ono, chingakuvulazeni