Chitsanzo Chabwino—Timoteyo
Chitsanzo Chabwino—Timoteyo
Timoteyo ali ndi zaka pafupifupi 20 anali wokonzeka kuchoka pakhomo pa makolo ake, osati pothawa zochitika za pakhomopo, koma kuti azikagwira ntchito ya umishonale limodzi ndi mtumwi Paulo. Pa msinkhu umenewu n’kuti Timoteyo ali kale ndi udindo chifukwa “abale a ku Lusitara ndi ku Ikoniyo anamuchitira umboni wabwino.” (Machitidwe 16:2) Paulo ankakhulupirira kuti Timoteyo akhoza kuchita zambiri potumikira Mulungu, ndipo n’zimenedi anachita. M’zaka zotsatira Timoteyo anayenda m’madera ambiri n’kumakhazikitsa mipingo komanso kulimbikitsa abale. Makhalidwe abwino amene Timoteyo anali nawo anapangitsa kuti Paulo azimukonda ndipo patapita zaka 11, Paulo anauza Akhristu a ku Filipi kuti: “Ndilibe wina wamtima ngati iye, amene angasamaledi za inu moona mtima.”—Afilipi 2:20.
Kodi inuyo mukuchita zinthu zosonyeza kuti mukufuna kuti muzigwiritsidwa ntchito? Ngati mukufunitsitsa kutumikira Mulungu, dziwani kuti mudzapeza madalitso ambiri. Yehova amakonda kwambiri achinyamata amene ‘amadzipereka mofunitsitsa.’ (Salimo 110:3) Komanso simuyenera kukayikira zoti Yehova Mulungu “si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu.”—Aheberi 6:10.