Kodi Ndingadziteteze Bwanji Kwa Anthu Ogwiririra Anzawo?
Mutu 32
Kodi Ndingadziteteze Bwanji Kwa Anthu Ogwiririra Anzawo?
Chaka chilichonse anthu ambiri amagwiriridwa kapena kuchitiridwa zachipongwe ndipo kafukufuku amasonyeza kuti anthu ambiri amene amachita zimenezi amapezerera kwambiri achinyamata. Mwachitsanzo, ku United States pafupifupi hafu ya anthu amene anagwiriridwa anali osakwanitsa zaka 18. Chifukwa chakuti achinyamata ambiri akugwiriridwa, n’kofunika kuti muwerenge nkhaniyi.
“Ndinangoona kuti munthu wandigwira n’kundigwetsera pansi mwamsangamsanga. Ndinayesetsa kulimbana naye komanso kukuwa mmene ndikanathera koma sizinathandize. Ndinayesa kumukankha, kumumenya ndi miyendo, manja komanso kumukalakala. Kenako ndinangomva kuti wandibaya ndi mpeni. Thupi lonse linangofookeratu.”—Anatero Annette.
MASIKU ano anthu ogwiririra achuluka ndipo akumapezerera kwambiri achinyamata. Achinyamata, ngati Annette, amagwiriridwa ndi anthu oti sakuwadziwa. Koma ena amagwiriridwa ndi anthu oti amakhala nawo pafupi. Mwachitsanzo, Natalie, anagwiriridwa ali ndi zaka 10 ndi mnyamata amene ankakhala pafupi ndi nyumba ya kwawo. Iye anati: “Ndinkachita mantha komanso manyazi moti sindinauze aliyense zitangondichitikira kumene.”
Koma achinyamata ambiri amagwiriridwa ndi achibale. Mzimayi wina, dzina lake Carmen, ananena kuti: “Bambo anga ankandigwiririra kuyambira ndili ndi zaka 5 mpaka pamene ndinakwanitsa
zaka 12. Nditakwanitsa zaka 20 m’pamene ndinalimba mtima kuwafunsa za nkhaniyi komanso kuwafotokozera mmene zimene ankachitazo zinandikhudzira. Anandipepesa koma patangopita miyezi yochepa anandithamangitsa pakhomopo.”N’zomvetsa chisoni kuti masiku ano anthu ambiri akumagwiriridwa ndi anthu oyandikana nawo nyumba, anzawo kapenanso abale awo amene. * Komatu kuchitira nkhanza ana si nkhani yachilendo. Zinthu ngati zimenezi zinkachitikanso kale pa nthawi imene Baibulo linkalembedwa. (Yoweli 3:3; Mateyu 2:16) Panopa tikukhala m’nthawi yovuta kwambiri. Anthu ambiri ‘sakonda achibale awo,’ ndipo kugwiriridwa kwa atsikana (ngakhalenso anyamata) si nkhani yachilendo. (2 Timoteyo 3:1-3) Ngakhale kuti n’zosatheka kupeweratu kuti zimenezi zisakuchitikireni, pali zinthu zingapo zimene mungachite kuti mudziteteze. Mungayese kuchita zotsatirazi:
Muzikhala tcheru. Mukamayenda mumsewu muzidziwa zimene zikuchitika kutsogolo kwanu, kumbuyo kwanu komanso mbali zonse. Malo ena amachita kudziwikiratu kuti ndi oopsa, makamaka usiku. Ngati n’zotheka muzipewa kudutsa malo otero koma ngati n’zosatheka, onetsetsani kuti simukudutsapo nokhanokha.—Miyambo 27:12.
Musamachititse anthu kukhala ndi maganizo olakwika. Muzipewa kukopa anthu kapena kuvala mochititsa anthu kukhala ndi maganizo olakwika. Kuchita zimenezi kukhoza kupangitsa anthu kuganiza kuti mukufuna amuna kapena kuti simungakane munthu atakufunsirani.—1 Timoteyo 2:9, 10.
Muzikambirana malire osonyezerana chikondi. Ngati muli pa chibwenzi, kambiranani ndi mnzanuyo zinthu zimene mukuona kuti n’zoyenera kapena ayi. * Mukagwirizana malirewo, yesetsani kuwatsatira chifukwa mukapanda kutero mukhoza kuchititsa mnzanuyo kuti akugwiririreni.—Miyambo 13:10.
Muzilankhula zikalakwika. Si kulakwa kumuuza mnzanuyo mwamphamvu kuti, “Zimenezo ayi” kapena “Zogwiranagwiranazo ayi.” Musalephere kulankhula chifukwa choopa kuti akhoza kuthetsa chibwenzicho. Ngati atathetsa chibwenzicho chifukwa cha nkhani yake imeneyi, ndiye kuti sanali munthu woyenera kumanga naye *
banja. Ndipotu muyenera kukwatiwa ndi mwamuna weniweni amene amalemekeza thupi lanu komanso mfundo zimene mumatsatira.Muzisamala mukamagwiritsa ntchito intaneti. Musamalembepo zinthu zosafunika kuuza anthu chisawawa kapena kuikapo zithunzi zanu zimene zingapangitse anthu ena kudziwa kumene angakupezeni. * Ngati mwatumiziridwa uthenga wokhudza zogonana, ndi bwino kusayankha. Kusayankha kumapangitsa anthu amene amafuna kugwirira anzawo kusowa chochita.
Miyambo 22:3) Komabe ndi zoona kuti nthawi zina n’zovuta kudziteteza. Mwachitsanzo, sizingatheke kuti nthawi zonse muziyenda ndi munthu wina komanso nthawi zina n’zosatheka kupewa kudutsa malo oopsa. Mwinanso dera limene mumakhalalo ndi loopsa.
Mfundo zimene tafotokozazi zingakuthandizeni kuti muzikhala otetezeka. (N’kutheka kuti zimene zinakuchitikirani zinakupangitsa kuvomereza kuti nthawi zina munthu umatha kukumana ndi zinthu zoipa ngakhale kuti umayesetsa kuzipewa. Mwina nanunso munangokumana nazo mwadzidzidzi ndipo munalephera kulimbana ndi munthuyo ngati mmene zinachitikira kwa Annette, yemwe tamutchula koyambirira uja. Kapena mwina munkagwiriridwa muli mwana moti simukanatha kuchita chilichonse kapenanso simunkazindikira n’komwe zimene zinkachitika ngati mmene zinakhalira ndi Carmen. Koma kodi mungatani ngati mumangodziimba mlandu chifukwa chakuti winawake anakugwiririrani?
Zimene Mungachite Ngati Mumangodziimba Mlandu
Mpaka pano Annette amadziimbabe mlandu chifukwa cha zimene zinamuchitikira. Iye anati: “Ndimaona kuti wolakwitsa kwambiri ndinali ineyo. Zimene zinandichitikirazo zimandibwererabe mpaka pano. Ndimaona kuti sizikanachitika ndikanakhala kuti ndinayesetsa kwambiri kulimbana naye. Koma zimene zinachitika n’zoti atangondibaya mphamvu zonse zinatheratu chifukwa cha mantha. Ndinalephera kuchita china chilichonse koma
ndimadziimbabe mlandu poganiza kuti pali zinazake zimene ndinkayenera kuchita.”Nayenso Natalie amadziimbabe mlandu. Iye anati: “Vuto linali lakuti ndinkamukhulupirira kwambiri. Makolo athu ankatiuza kuti nthawi zonse tikamasewera panja tizikhala limodzi ndi mng’ono wanga koma sindinkamvera. Choncho ndimaona kuti ineyo ndi amene ndinam’patsa mnyamatayo mpata woti andichite chipongwe. Zimene zinachitikazo zinakhudza banja lathu lonse ndipo ndimaona kuti ineyo ndi amene ndinayambitsa mavuto onsewa. Maganizo amenewa amandisowetsa mtendere kwambiri.”
Ngati inuyo mumavutika ndi maganizo ofanana ndi amene Annette kapena Natalie ali nawo, kodi mungatani? Choyamba, muzikumbukira kuti ngati munagwiriridwa ndiye kuti sikunali kufuna kwanu. Anthu ena amaiona nkhaniyi mopepuka ponena mawu akuti, “anyamatatu ndi choncho,” ndiponso amanena kuti anthu amene agwiriridwa ndiye kuti anaziyamba dala. Komatu palibe munthu amene amayenera kugwiriridwa. Ngati munagwiriridwa, dziwani kuti limeneli si vuto lanu.
N’zoona kuti mawu akuti “si vuto lanu” ndi ophweka powerenga koma ndi ovuta kuwakhulupirira. Anthu ena amabisa zimene zinawachitikira ndipo amavutika chifukwa cha kudziimba mlandu komanso amakhala ndi maganizo ambirimbiri olakwika. Koma kodi ndi ndani amene zimamuyendera bwino mukapanda kuulula nkhaniyi? Inuyo kapena munthu amene anakugwiririraniyo? Kuti zinthu zikuyendereni bwino mukufunika kuuza anthu ena zimene zinachitikazo.
Muzifotokozera Ena
Baibulo limatiuza kuti Yobu atavutika maganizo kwambiri chifukwa cha zimene zinamuchitikira ananena kuti: “Ndilankhula mwamphamvu za nkhawa zanga. Ndilankhula chifukwa cha kuwawa kwa moyo wanga.” (Yobu 10:1) Kuchita zimenezi nanunso kukhoza kukuthandizani. Kufotokozera munthu wina amene mumamukhulupirira kungathandize kuti m’kupita kwa nthawi muiwale zimene zinachitikazo komanso kuti maganizo anu akhazikike.
Ndipo ngati ndinu Mkhristu, ndi bwino kufotokozera akulu kumpingo zimene zinachitikazo. Mawu olimbikitsa a m’busa wachikondi angakuthandizeni kutsimikizira kuti tchimo limene munthu amene anakugwiririraniyo ali nalo silikukhudzanso inuyo. Zimenezi ndi zimene Annette anachita. Iye anati: “Ndinafotokozera mnzanga wapamtima zimene zinachitikazo ndipo anandilimbikitsa kuti ndikafotokozere akulu kumpingo kwathu. Ndimaona kuti ndinachita bwino kuwafotokozera chifukwa anakambirana nane nkhaniyi maulendo angapo ndipo anandiuza zinthu zimene zinandikhazika mtima pansi kwambiri. Anandiuza kuti zimene zinachitikazo silinali vuto langa ngakhale pang’ono.”
Salimo 37:8) Komanso zingakuthandizeni kuti mulandire thandizo loyenera, lomwe mwina mwakhala mukulilakalaka kwa nthawi yaitali. Natalie atafotokozera makolo ake zoti wagwiriridwa anaona kuti mfundo imeneyi ndi yoona. Iye anati: “Makolo anga anandithandiza kwambiri. Anandilimbikitsa kuti ndizimasuka kufotokozera anthu ena zimene zinachitikazo ndipo zimenezi zinandithandiza kuti ndisamakhale wokhumudwa kwambiri.” Chinthu chinanso chimene chinamulimbikitsa Natalie ndi pemphero. Iye anati: “Kupemphera kwa Mulungu kunkandithandiza makamaka ndikakhala kuti sindikumasuka kuuza munthu wina. Ndikamapemphera ndimalankhula momasuka ndipo zimenezi zimandithandiza kuti ndizikhala ndi mtendere wamumtima komanso maganizo anga azikhazikika.” *
Kufotokozera anthu ena zimene zinakuchitikirani komanso mmene mukumvera kungakuthandizeni kuti musakhumudwe kwambiri kapena kukhala ndi maganizo ofuna kubwezera. (M’kupita kwa nthawi mudzaona kuti pali ‘nthawi yochira.’ (Mlaliki 3:3) Muzidalira anzanu amene akhoza kukuthandizani chifukwa ali ngati akulu omwe amayerekezeredwa ndi “malo obisalirapo mphepo ndi malo ousapo mvula yamkuntho.” (Yesaya 32:2) Muzisamalira thanzi lanu komanso muziganizira zinthu zolimbikitsa. Muzigona mokwanira. Koposa zonse, muzidalira Mulungu amene amatitonthoza, yemwe posachedwapa abweretsa dziko latsopano ndipo m’dziko limeneli anthu onse “ochita zoipa adzaphedwa. Koma oyembekezera Yehova ndi amene adzalandire dziko lapansi.”—Salimo 37:9
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 7 Nthawi zina munthu amagwiriridwa ndi chibwenzi chake. Zimene zimachitika ndi zoti mnyamata amakakamiza kapena kunyengerera mtsikana kuti agonane.
^ ndime 10 Kuti mudziwe zambiri werengani Mutu 4, m’Buku Lachiwiri.
^ ndime 11 Malangizo amenewa angagwirenso ntchito ngati mtsikana atakakamiza mnyamata kuti agone naye.
^ ndime 12 Kuti mudziwe zambiri werengani Mutu 11, m’Buku Lachiwiri.
^ ndime 23 Nthawi zina anthu amene agwiriridwa amayamba kudwala matenda ovutika maganizo. Zimenezi zikachitika ndi bwino kukaonana ndi adokotala. Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya kuvutika maganizo, werengani Mutu 13 ndi 14.
LEMBA
“Masiku otsiriza adzakhala nthawi yapadera komanso yovuta. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, . . . osakonda achibale awo, . . . osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino.”—2 Timoteyo 3:1-3.
MFUNDO YOTHANDIZA
Ngati munagwiriridwapo, lembani malemba angapo omwe angakulimbikitseni. Mukhoza kuphatikizapo malemba awa: Salimo 37:28; 46:1; 118:5-9; Miyambo 17:17 ndi Afilipi 4:6, 7.
KODI MUKUDZIWA . . . ?
Ana 9 pa 10 aliwonse amene anagwiriridwa ku United States, anagwiriridwa ndi munthu woti amamudziwa.
ZOTI NDICHITE
Ndikayamba kudziimba mlandu chifukwa cha zomwe zinachitikazo, ndizichita izi ․․․․․
Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․
KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?
● Kodi kufotokozera ena ngati mwagwiriridwa kuli ndi phindu lotani?
● Kodi n’chiyani chingakuchitikireni inuyo kapena anthu ena ngati mutabisa nkhaniyi?
[Mawu Otsindika patsamba 232]
“Zimakhala zovuta kwambiri kufotokozera munthu wina zimene zinakuchitikira koma n’kothandiza kwambiri. Kumathandiza kuti usamangokhala wokhumudwa, wokwiya komanso kuti zinthu ziyambirenso kukuyenderani bwino.”—Anatero Natalie
[Bokosi patsamba 230]
“Ngati Umandikonda . . . ”
Anthu ena akafuna kugwiririra atsikana sachita kugwiritsa ntchito mphamvu. Amangowasokoneza maganizo. Kodi amachita bwanji zimenezi? Amatha kulankhula mawu ngati akuti, “Aliyensetu amachita zimenezi,” “Palibe amene adziwe,” kapena amanena mawu amene anatchulidwa m’Mutu 24 akuti, “Ngati umandikondadi, ulola.” Musapusitsike ndi mnyamata amene angakuuzeni kuti kugonana ndi umboni woti mumakondana. Mfundo ndi yakuti, aliyense amene amaganiza choncho akungofuna kusangalatsa mtima wake ndipo saganizira za inuyo. Koma mwamuna weniweni angaganizire za zofuna zanu kuposa zake ndipo angasonyeze kuti amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo. (1 Akorinto 10:24) Mwamuna weniweni samaona atsikana ngati ofunika kugona nawo basi. M’malomwake, amaona akazi achitsikana ngati alongo ake, ndipo pochita zimenezi sakhala ndi maganizo alionse oipa.—1 Timoteyo 5:1, 2.
[Chithunzi patsamba 233]
Kusafotokozera anthu ena pambuyo poti mwagwiriridwa kuli ngati kunyamula nokha katundu wolemera. Choncho ndi bwino kufotokozera anthu ena kuti akuthandizeni