Mawu Oyamba
Mawu Oyamba
Mayankho Othandiza
‘Kodi ndingatani kuti ndizilankhula momasuka ndi makolo anga?’ ‘Kodi ndingapeze bwanji anzanga abwino?’ ‘Kodi kugonana pongofuna kuthandizana kuli ndi vuto?’ ‘N’chifukwa chiyani ndimangokhala wokhumudwa?’
Ngati munadzifunsapo mafunso amenewa, dziwani kuti simuli nokha. N’kutheka kuti mutafunsa anthu ena, zimene anakuyankhani zinali zotsutsana. Pofuna kuthandiza achinyamata kupeza malangizo odalirika, kuyambira mu January 1982, m’magazini a Galamukani! munayamba kutuluka nkhani za mutu wakuti, “Zimene Achinyamata Amadzifunsa.” Anthu ambiri amakondabe kuwerenga nkhanizi mpaka pano ndipo amapindula nazo. Nkhani iliyonse imafufuzidwa mokwanira isanalembedwe. Ndipotu kuti adziwe mmene achinyamata amaganizira komanso mmene amamvera, olemba Galamukani! akhala akulankhula ndi achinyamata ambirimbiri ochokera m’mayiko osiyanasiyana padziko lonse lapansi. Koma chofunika kwambiri n’choti malangizo amene ali mu nkhani zakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa” amachokera m’Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu.
Buku limene mukuwerengali linatuluka koyamba mu 1989. Koma panopa mitu yake yasinthidwa kuti igwirizane ndi mmene moyo ulili masiku ano. Mitu yoposa 30 yachokera mu nkhani zakuti, “Zimene Achinyamata Amadzifunsa” zomwe zinatuluka mu Galamukani! kuyambira mu 2004 kufika mu 2011.
Buku limeneli likuthandizani kuphunzira makhalidwe amene angadzakuthandizeni mukadzakula. Tikukhulupirira kuti mukamayesetsa kutsatira malangizo a m’bukuli, mukhala m’gulu la anthu achikulire komanso achinyamata mamiliyoni ambiri “amene pogwiritsa ntchito mphamvu zawo za kuzindikira, aphunzitsa mphamvuzo kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.”—Aheberi 5:14.
Ofalitsa Bukuli