Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Ndizigwiritsa Ntchito Nthawi Yanga Mwanzeru?

Kodi Ndingatani Kuti Ndizigwiritsa Ntchito Nthawi Yanga Mwanzeru?

Mutu 21

Kodi Ndingatani Kuti Ndizigwiritsa Ntchito Nthawi Yanga Mwanzeru?

Kodi mumalakalaka mukanakhala ndi maola angati owonjezera pa tsiku? ․․․․․

Kodi maola owonjezerawo mukanawagwiritsa ntchito bwanji?

□ Pocheza ndi anzanga

□ Kugona

□ Kuwerenga

□ Zina ․․․․․

NTHAWI ili ngati hatchi yamphamvu. Kuti muigwiritse ntchito bwino mukufunika kuphunzira kuilamulira. Muzilamulira nthawi yanu ndipo zimenezi zidzakuthandizani kuti musamapanikizike kwambiri, muzikhoza bwino kusukulu, komanso makolo anu akhoza kumakudalirani. Koma mwina mukhoza kunena kuti, “Zitakhalatu choncho, zikhoza kukhala bwino kwambiri. Koma kuchita zimenezi n’kovuta. Zikungooneka zophweka polankhula.” N’zoonadi kuti mukhoza kukumana ndi mavuto pochita zimenezi. Komabe mukhoza kuwagonjetsa. Tiyeni tione zitsanzo zingapo.

Vuto Loyamba: Kukhala Ndi Pulogalamu Yochitira Zinthu

Zimene zingakulepheretseni kukhala ndi pulogalamu. Mukhoza kumaganiza kuti kukhala ndi pulogalamu yochitira zinthu kungapangitse kuti muzipanikizika. Mwina mumakonda kuchita zinthu pa nthawi imene mwafuna osati kuchita kukonzeratu nthawi yochitira zinthuzo.

N’chifukwa chiyani muyenera kukhalabe ndi pulogalamu? Mfumu Solomo inalemba kuti: “Zolinga za munthu wakhama zimam’pindulira.” (Miyambo 21:5) Solomo ankatanganidwa kwambiri chifukwa anali wokwatira, anali ndi ana komanso anali mfumu. Ndipo mwachidziwikire maudindo amenewa ankawonjezereka m’kupita kwa nthawi. Nanunso mumakhala otanganidwa panopa komabe kutanganidwako kuziwonjezereka mukamakula. Choncho ndi bwino kuyambiratu panopa kuchita zinthu mwadongosolo.

Zimene anzanu ananena. “Kwa miyezi 6 yapitayi ndakhala ndikuchita zinthu zanga motsatira pulogalamu. Ndimayesetsa kuti zimene ndikuchitazo zisamaoneke ngati zovuta ndipo ndaona kuti kutsatira pulogalamu kwandithandiza kwambiri.”​—Anatero Joey.

“Kulemba zinthu zonse zimene ndikufuna kuchita kumandithandiza kuti ndikwanitse kuchita zonse zimene ndikufuna. Ngati papezeka zinthu zina zofunika kuti tichite, timazilemba ndipo ndimakambirana ndi mayi anga kuti tione zimene tonse tingachite kuti zinthuzo zitheke.”​—Anatero Mallory.

Zomwe zingakuthandizeni. Tiyerekeze kuti banja lanu lonse lili pa ulendo. Aliyense akungoponya mwachisawawa chikwama chake m’galimoto moti zayamba kuoneka kuti malo sakwana. Kodi mungatani? Mukhoza kutsitsa kaye zikwama zonse n’kuyambiranso kuziika bwinobwino. Mungakweze kaye zikwama zikuluzikulu kenako m’mipata yomwe yatsala, mungaikemo zikwama zing’onozing’ono.

Mungatsatirenso njira imeneyi pamene mukufuna kupeza njira yabwino yogwiritsa ntchito nthawi yanu. Ngati mutayamba kuchita zinthu zing’onozing’ono, mukhoza kupezeka kuti mulibe nthawi yochitira zinthu zofunika. Choncho, pezani kaye nthawi yochitira zinthu zofunika kwambiri, ndipo mudzadabwa kupeza kuti muli ndi nthawi yambiri yochitira zinthu zinazo.—Afilipi 1:10.

Lembani zinthu zofunika kwambiri zimene mukufuna kuchita.

․․․․․

Kenako zipatseni manambala malinga ndi kufunika kwake ndipo chofunika kwambiri chikhale nambala 1. Ngati mutachita kaye zinthu zofunika kwambiri mungadabwe kupeza kuti mwatsala ndi nthawi yambiri yochitira zinthu zina zotsalazo.

Zimene mungachite. Khalani ndi kabuku koti muzilembamo zimene mukufuna kuchita ndipo muzilemba zinthuzo malinga ndi kufunika kwake. Apo ayi mukhoza kugwiritsa ntchito zinthu zotsatirazi:

□ Kalendala ya mu foni

□ Pepala

□ Kalendala ya pa kompyuta

□ Kalendala yeniyeni

Vuto Lachiwiri: Kutsatira Pulogalamu Yanu Nthawi Zonse

Zimene zingakulepheretseni kutsatira pulogalamu yanu. Mwina mukaweruka kusukulu mumangofuna mutakhala pansi n’kumaonera TV. Kapena mukhoza kukhala ndi maganizo oti muziwerenga pokonzekera mayeso, koma n’kulandira meseji yokuitanani kuti mupite kwa mnzanu kukaonera filimu. Mukhoza kukhala ndi maganizo oti ndi bwino kukaonera kaye filimuyo, n’kudzapitiriza kuwerengako usiku. Mwina mungamadziuze kuti, ‘Komansotu ine ndimachita zinthu bwino kukatsala nthawi yochepa.’

N’chifukwa chiyani muyenera kutsatirabe pulogalamu yanu? Mungamakhoze bwino kusukulu ngati mutamawerenga maganizo anu asanasokonezeke ndi zinthu zina. Komanso monga mwana wa sukulu mwachidziwikire mumapanikizika kale ndi zinthu zina. Choncho, si bwino kumawerenga zinthu zambirimbiri komanso usiku kwambiri pokonzekera mayeso chifukwa zingawonjezere kupanikizika komwe muli nako kale. Kuchita zimenezi kungapangitse kuti mudzuke mochedwa, mukhale wotopa, muzichita kuthamanga popita kusukulu komanso mwina mukhoza kuchedwa kusukuluko.​—Miyambo 6:10, 11.

Zimene anzanu ananena. “Ndimakonda kuonera TV, kuimba gitala komanso kucheza ndi anzanga. Pazokha zinthu zimenezi si zolakwika koma nthawi zina zimandichititsa kuti ndinyalanyaze zinthu zofunika kwambiri zomwe zimachititsa kuti zinthu zofunikazo ndidzazichite mwaphuma.”​—Anatero Julian.

Zomwe zingakuthandizeni. Musamangoika ntchito zokhazokha pa pulogalamu yanu, muziikaponso zinthu zosangalatsa. Julian ananena kuti: “Zimandiphwekera kugwira ntchito zimene zili pa pulogalamu yanga chifukwa ndimadziwa kuti ndaika kale nthawi yochitira zinthu zina zosangalatsa.” Mukhozanso kukhala ndi cholinga chachikulu chimene mukufuna kuchikwaniritsa kenako mungakhale ndi zolinga zing’onozing’ono zimene zingakuthandizeni kukwaniritsa cholinga chachikulucho.

Zimene mungachite. Lembani chinthu chimodzi kapena ziwiri zomwe mukhoza kuzikwaniritsa m’miyezi 6 ikubwerayi.

․․․․․

Lembani cholinga chimene mukhoza kuchikwaniritsa m’zaka ziwiri zikubwerazi ndiponso zimene muyenera kuyamba kuchita panopo kuti zimenezi zidzatheke. *

․․․․․

Vuto Lachitatu: Kukhala Waukhondo Ndiponso Kuchita Zinthu Mwadongosolo

Zimene zingakulepheretseni kuchita zimenezi. Mwina simukudziwa kuti kukhala waukhondo komanso kuchita zinthu mwadongosolo kungakuthandizeni kuti muzigwiritsa ntchito nthawi yanu mwanzeru. Komanso kumangosiya zinthu paliponse kungamaoneke ngati kophweka. Mwinanso mungamaone kuti mukhoza kukonza kuchipinda kwanu nthawi ina, kapenanso osakonzako n’komwe. Mwina inuyo mumaona kuti kugona m’chipinda chosakonza kulibe vuto. Koma kodi n’zoona kuti kusakonza kuchipinda kwanu kulibedi vuto?

N’chifukwa chiyani muyenera kuchita zimenezi? Kukhala waukhondo komanso kuchita zinthu mwadongosolo kungakuthandizeni kuti musamatenge nthawi yaitali mukufufuza zinthu zanu. Kungakuthandizeninso kuti musamapanikizike.​—1 Akorinto 14:40.

Zimene anzanu ananena. “Nthawi zina ndikapanda kuika zovala zanga pamalo ake zimachititsa kuti zinthu zina zofunika zizivuta kupeza chifukwa zimaphimbika ndi zovalazo.”​—Anatero Mandy.

“Nthawi ina waleti yanga inasowa kwa wiki yathunthu ndipo sindinkamva bwino. Koma ndinaipeza pamene ndinkakonza kuchipinda kwanga.”​—Anatero Frank.

Zomwe zingakuthandizeni. Muziyesetsa kuika chilichonse pamalo ake mukangomaliza kuchigwiritsa ntchito. Muzichita zimenezi nthawi zonse ndipo musamadikire kuti zinthu zichulukane.

Zimene mungachite. Yesani kukhala ndi chizolowezi choika zinthu zanu mwadongosolo. Ngati mutamasunga zinthu zonse mwadongosolo komanso zili zoyera simungamapanikizike pochita zinthu.

Nthawi imene inuyo mumakhala nayo pa tsiku ndi yofanana ndi nthawi imene anzanu komanso makolo anu amakhala nayo. Mukapanda kuigwiritsa ntchito mwanzeru zidzakuvutani. Koma ngati mutaigwiritsa ntchito mwanzeru, zinthu zidzakuyenderani bwino kwambiri. Choncho, muli ndi ufulu woigwiritsa ntchito mwanzeru kapena ayi.

M’MUTU WOTSATIRA

Kodi mukukhala ndi makolo omwe akugwira ntchito dziko lina? Kodi mumaona kuti mumasiyana ndi anzanu akusukulu komanso kunyumba? Werengani nkhaniyi kuti muone zimene mungachite ngati muli ndi vuto limeneli.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 32 Kuti mudziwe zambiri, werengani Mutu 39.

LEMBA

“Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”​—Afilipi 1:10.

MFUNDO YOTHANDIZA

Musayese kutsatira mfundo zonse za mu nkhaniyi nthawi imodzi. M’malomwake yesani kutsatira mfundo imodzi m’mwezi ukubwerawu. Mukazolowera kutsatira mfundo imeneyo, sankhani ina yoti muyambe kutsatira.

KODI MUKUDZIWA . . . ?

Kufuna kuchita zinthu zambirimbiri tsiku limodzi kungachititse kuti muzipanikizika. Kudziwa zinthu zofunika kwambiri kudzakuthandizani kusankha zimene muyenera kuchita komanso zimene mukhoza kungozisiya.

ZOTI NDICHITE

Zinthu zimene sindikufunika kumazichita kwa nthawi yaitali ndi ․․․․․

Nthawi yotsalayo ndikhoza kumaigwiritsa ntchito pochita izi ․․․․․

Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pa nkhaniyi ․․․․․

KODI INUYO MUKUGANIZA BWANJI?

● Kodi kuphunzira kugwiritsa ntchito bwino nthawi panopa kungadzakuthandizeni bwanji m’tsogolo mukadzakhala ndi khomo lanulanu?

● Kodi mungaphunzire chiyani kwa makolo anu pa nkhani ya mmene amagwiritsira ntchito nthawi yawo?

● Ngati munayamba kale zomalemba pulogalamu ya zimene mukufuna kuchita, kodi mungasinthe zinthu ziti kuti pulogalamuyo izikhala yothandiza kwambiri?

[Mawu Otsindika patsamba 154]

“Tsiku lina ndinamva anthu ena akuuzana moseka kuti ngati akufuna kuti ndikakumane nawo 4 koloko ayenera kundiuza kuti ndipite isanakwane 3 koloko. Nditangomva zimenezi ndinazindikira kuti ndili ndi vuto losachita zinthu pa nthawi yake ndipo ndikufunika kusintha.”​—Anatero Ricky

[Bokosi patsamba 155]

Kodi Nthawi Yanga Imathera pa Zinthu Ziti?

Mlungu uliwonse, ana ambiri a zaka zapakati pa 8 ndi 18 amagwiritsa ntchito nthawi yawo motere:

17

kuchita zinthu zina ndi makolo awo

30

kusukulu

44

kuonera TV, kuchita masewera a pa kompyuta, kutumizirana mameseji komanso kumvera nyimbo

Phatikizani maola onse amene mumawononga pa mlungu

kuonera TV ․․․․․

kuchita masewera a pa kompyuta ․․․․․

kuchita zinthu pa intaneti ․․․․․

kumvera nyimbo ․․․․․

Maola onse ․․․․․

Maola ochitira zinthu zofunika kwambiri amene ndingapeze ngati nditachepetsa nthawi yochitira zinthu zina ․․․․․

[Chithunzi patsamba 153]

Nthawi ili ngati hatchi yamphamvu. Kuti muigwiritse ntchito bwino mukufunika kuphunzira kuilamulira