Uthenga Wopita kwa Makolo
Kodi mphatso yabwino kwambiri imene mungapatse ana anu ndi iti? Ana amafuna zinthu zambiri. Mwachitsanzo, iwo amafuna kuti muziwakonda, kuwauza zoyenera kuchita komanso kuwateteza. Komabe, mphatso yamtengo wapatali kwambiri imene mungapatse ana anuwo ndi kuwathandiza kuti am’dziwe Yehova ndi choonadi chopezeka m’Mawu ake, Baibulo. (Yohane 17:3) Zimenezi zingathandize anawo kuti azikonda Yehova ndi kum’tumikira ndi mtima wonse, kuyambira ali aang’ono.—Mateyu 21:16.
Makolo ambiri akuona kuti ana aang’ono amaphunzira mofulumira ngati akuwaphunzitsa pang’onopang’ono ndi kuwauza zinthu zina zoti azichita. Choncho ndife osangalala kutulutsa kabuku kano kakuti Zimene Ndikuphunzira M’Baibulo. Mutu uliwonse anaupanga m’njira yakuti ukhale wosavuta kuuphunzira. Kabuku kano talembera ana osapitirira zaka zitatu. Taikamo zithunzi ndi mawu ofotokozera zithunzizo komanso zoti ana azichita. Kabukuka si koti anawo aziseweretsa ayi, koma n’koti inuyo makolo muziwawerengera. Zimenezi zidzathandiza kuti muzikhala ndi nthawi yolankhulana ndi anawo.
Tikukhulupirira kuti kabukuka kakuthandizani kwambiri pamene mukuphunzitsa ana anu choonadi cha m’Baibulo ‘kuyambira ali akhanda.’—2 Timoteyo 3:14, 15.
Ndife abale anu,
Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova