Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

8

Kodi Ndiyenera Kudziwa Chiyani Zokhudza Anthu Ogwiririra?

Kodi Ndiyenera Kudziwa Chiyani Zokhudza Anthu Ogwiririra?

KODI YANKHO LA FUNSOLI LINGAKUTHANDIZENI BWANJI?

Chaka chilichonse anthu ambiri amagwiriridwa kapena kuchitiridwa zachipongwe ndipo ambiri mwa ogwiriridwawo amakhala achinyamata.

KODI MUKANAKHALA INUYO MUKANATANI?

Tsiku lina Annette akuyenda, anangoona kuti munthu wina wamugwira n’kumugwetsera pansi. Iye anati: “Ndinayesetsa kulimbana naye komanso kukuwa mmene ndikanathera koma sizinathandize. Ndinayesa kumukankha, kumumenya ndi miyendo, manja komanso kumukanda. Kenako ndinangomva kuti wandibaya ndi mpeni. Thupi lonse linangofookeratu.”

Kodi zimenezi zikanachitikira inuyo mukanatani?

MFUNDO YOFUNIKA KUIGANIZIRA

Ngakhale kuti mungayesetse kukhala osamala nthawi zonse, nthawi zina zoipa zingachitikebe. Baibulo limati: “Anthu othamanga kwambiri sapambana pampikisano . . . odziwa zinthu sakondedwa, chifukwa nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo.”—Mlaliki 9:11.

Achinyamata ena ngati Annette, amagwiriridwa ndi anthu oti sakuwadziwa. Koma ena amagwiriridwa ndi anthu oti amakhala nawo pafupi. Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Natalie anagwiriridwa ali ndi zaka 10 ndi mnyamata amene ankakhala pafupi ndi kwawo. Iye anati: “Ndinkachita mantha komanso manyazi moti zitangondichitikira kumene sindinauze aliyense.”

WOLAKWA SI INU

Annette amadziimbabe mlandu. Iye anati: “Ndimaona kuti wolakwa ndinali ineyo. Ndikakumbukira zimene zinachitika, ndimaganiza kuti ndikanakhala kuti ndinayesetsa kulimbana naye, mwina sakanandigwiririra. Koma atangondibaya mphamvu zonse zinatheratu chifukwa cha mantha. Koma ndimadziimbabe mlandu poganiza kuti pali zinazake zimene ndikanachita.”

Nayenso Natalie amadziimbabe mlandu. Iye anati: “Vuto linali lakuti ndinkamukhulupirira kwambiri mnyamatayo. Makolo anga ankandiuza kuti ndikamasewera panja ndizikhala ndi mchemwali wanga, koma sindinkamvera. Choncho ndimaona kuti ineyo ndi amene ndinam’patsa mpata woti andichite chipongwe. Zimene zinachitikazo zinakhudza banja lathu lonse ndipo ndimaona kuti ineyo ndi amene ndinayambitsa mavuto onsewa. Maganizo amenewa amandisowetsa mtendere.”

Ngati inunso munagwiriridwapo ndipo mumadziimba mlandu, dziwani kuti munthu sachita kufuna kuti agwiriridwe. Anthu ena amaiona nkhaniyi mopepuka ndipo amati, “anyamatatu ndi choncho.” Ena amanena kuti anthu amene agwiriridwa ndiye kuti anaziyamba dala. Komatu palibe munthu amene amayenera kugwiriridwa. Ngati munagwiriridwapo, dziwani kuti vuto si inuyo.

Koma mwina zingakuvutenibe kukhulupirira kuti vuto si inuyo. Anthu ena amabisa zimene zinawachitikira n’kumangodziimba mlandu komanso kukhala ndi maganizo ambirimbiri olakwika. Koma kodi ndi ndani amene zimamuyendera bwino mukabisa nkhaniyo? Inuyo kapena munthu amene anakugwiririraniyo? Choncho ndi bwino kuuza anthu ena zimene zinachitikazo.

MUYENERA KUFOTOKOZERA ENA

Baibulo limatiuza kuti Yobu atavutika maganizo kwambiri chifukwa cha zimene zinamuchitikira, ananena kuti: “Ndilankhula chifukwa cha kuwawa kwa moyo wanga.” (Yobu 10:1) Nanunso mukafotokozera munthu wina amene mumamukhulupirira zingathandize kuti muyambe kuiwala zimene zinachitikazo komanso kuti maganizo anu akhazikike.

Kusafotokozera anthu ena mmene mukumvera, kuli ngati kunyamula nokha katundu wolemera. Choncho ndi bwino kufotokozera anthu ena kuti akuthandizeni

Annette anaona kuti zimenezi n’zoona. Iye anati: “Ndinafotokozera mnzanga wapamtima zimene zinachitikazo ndipo anandiuza kuti ndikafotokozere akulu kumpingo kwathu. Ndimaona kuti ndinachita bwino kuwafotokozera chifukwa anakambirana nane nkhaniyi maulendo angapo ndipo zimene anandiuza zinandithandiza kwambiri. Anandiuza kuti zimene zinachitikazo silinali vuto langa.

Natalie anafotokozera makolo ake zimene zinamuchitikira. Iye anati: “Makolo anga anandithandiza kwambiri. Anandiuza kuti ndizimasuka kufotokozera anthu ena zimene zinachitikazo ndipo izi zinandithandiza kuti ndisamakhale wokhumudwa kwambiri.”

Chinanso chimene chinamulimbikitsa Natalie ndi pemphero. Iye anati: “Kupemphera kwa Mulungu kunkandithandiza makamaka ndikakhala kuti sindikumasuka kuuza munthu wina. Ndikapemphera, ndimalankhula momasuka ndipo zimenezi zimandithandiza kuti ndizikhala ndi mtendere wamumtima komanso maganizo anga azikhazikika.”

Nanunso pakapita nthawi mudzaona kuti pali ‘nthawi yochira.’ (Mlaliki 3:3) Muzisamalira thanzi lanu, muzigona mokwanira komanso muziganizira zinthu zolimbikitsa. Koposa zonse, muzidalira Mulungu amene amatitonthoza.—2 Akorinto 1:3, 4.

NGATI MWAFIKA MSINKHU WOKHALA NDI CHIBWENZI

Ngati ndinu mtsikana ndipo munthu amene muli naye pa chibwenzi akufuna kuti mugone naye, si kulakwa kumuuza mwamphamvu kuti, ‘zimenezo ayi’ kapena ‘zogwiranagwiranazo ayi.’ Musaope kuti akhoza kuthetsa chibwenzicho. Ngati atathetsa chifukwa cha nkhani imeneyi, ndiye kuti sanali munthu woyenera kumanga naye banja. Ndipotu muyenera kukwatiwa ndi mwamuna weniweni amene angalemekeze thupi lanu komanso mfundo zimene mumatsatira.

MAFUNSO

Mtsikana wina, dzina lake Coretta ananena kuti: “Kusukulu kwathu, anyamata ankandikoka khamisolo, n’kumandiuza zinthu zopusa ngati zokhudza mmene ndingasangalalire nditagona nawo.”

Kodi zimene anyamatawo anachitazi mungaziike m’gulu liti?

  1. Kumuvutitsa?

  2. Kumukopa?

  3. Kumuchitira nkhanza zokhudza kugonana?

Mtsikana wina, dzina lake Candice anati: “Tsiku lina tili m’basi, mnyamata wina anayamba kundiuza zinthu zopusa kenako anandigwira. Ndinakankha dzanja lakelo n’kumuuza kuti asandiyandikire. Mnyamatayo anangondiyang’ana modabwa kwambiri.”

Kodi zimene mnyamatayo anachitazi mungaziike m’gulu liti?

  1. Kumuvutitsa?

  2. Kumukopa?

  3. Kumuchitira nkhanza zokhudza kugonana?

Mtsikana wina, dzina lake Bethany anati: “Chaka chatha, mnyamata wina ankangokhalira kundiuza kuti ndimamusangalatsa ndipo anandifunsira. Ngakhale kuti ndinakana, iye ankangopitirizabe kundiuza zimenezi. Tsiku lina anayamba kundisisita pamkono. Ndinamuuza kuti asiye koma sanamve. Tsiku linanso nditawerama n’kumamanga zingwe za nsapato, mnyamatayo anandigwira m’matako.”

Kodi zimene mnyamatayo anachitazi mungaziike m’gulu liti?

  1. Kumuvutitsa?

  2. Kumukopa?

  3. Kumuchitira nkhanza zokhudza kugonana?

Yankho lolondola pa mafunso onsewa ndi C.

Kodi kuchitira munthu nkhanza zokhudza kugonana kumasiyana bwanji ndi kungomuvutitsa kapena kukopana?

Kuchitiridwa nkhanza zokhudza kugonana n’koipa kwambiri ndipo munthu amachita zimenezi ngakhale zitakhala kuti winayo sakufuna.

Nthawi zina nkhanza zokhudza kugonana zimafika poipa kwambiri, moti munthu amene akuchitidwayo akhoza kugwiriridwa.