Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

2

Kodi Ndiyeneradi Kudandaula Ndi Mmene Ndimaonekera?

Kodi Ndiyeneradi Kudandaula Ndi Mmene Ndimaonekera?

KODI YANKHO LA FUNSOLI LINGAKUTHANDIZENI BWANJI?

Pali zinthu zina zofunika kwambiri kuposa maonekedwe.

KODI MUKANAKHALA INUYO MUKANATANI?

Taganizirani izi: Mtsikana wina dzina lake Julia akadziyang’anira pagalasi, amadziona kuti ndi wonenepa kwambiri. Amaganiza kuti: “Ndikuyenera kuchepetsa thupi.” Iye amachita zimenezi ngakhale kuti makolo ake ndi anzake amamuuza kuti si wonenepa.

Julia wayamba kudzimana chakudya komanso kuchita zinthu zina n’cholinga choti akhale wochepa thupi.

Ngati inunso simusangalala chifukwa choona kuti ndinu wonenepa kwambiri, kodi mungatani?

MFUNDO YOFUNIKA KUIGANIZIRA

Mwina mumadziona molakwika ngati mmene mungaonekere pagalasi limene limasintha maonekedwe a munthu

Si kulakwa kuganizira za mmene mumaonekera. Ndipotu Baibulo limati akazi ndi amuna ena monga Sara, Rakele, Abigayeli, Yosefe ndi Davide anali ooneka bwino. Limatinso mtsikana wina wotchedwa Abisagi anali “chiphadzuwa.”—1 Mafumu 1:4.

Koma achinyamata ambiri amangokhalira kuganizira za maonekedwe awo. Zimenezi zingawabweretsere mavuto. Taganizirani izi:

  • Kafukufuku wina anasonyeza kuti atsikana 58 pa 100 alionse ankadziona kuti ndi onenepa kwambiri. Koma zoona zake zinali zakuti atsikana 17 okha pa 100 alionse, ndi amene analidi onenepa kwambiri.

  • Kafukufuku wina anasonyezanso kuti akazi 45 pa 100 alionse omwe anali ochepa thupi ankadziona kuti ndi onenepa kwambiri.

  • Pofuna kuchepetsa thupi, achinyamata ena amasala zakudya. Zimenezi zimachititsa kuti ayambe kudwala matenda amene amapangitsa kuti azidana ndi kudya.

Ngati mwayamba kudwala matenda amenewa kapena alionse okhudza kudana ndi kudya, muyenera kupeza thandizo. Uzani makolo anu kapena munthu aliyense wamkulu amene mumam’khulupirira. Baibulo limati: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.”—Miyambo 17:17.

KHALIDWE LABWINO LIMAPOSA KUKONGOLA

Khalidwe la munthu ndi limene limachititsa kuti anthu azimukonda kapena ayi. Chitsanzo ndi Abisalomu yemwe anali mwana wa Mfumu Davide. Baibulo limati:

“Mu Isiraeli yense munalibe mwamuna wina wotamandika kwambiri koposa Abisalomu chifukwa cha kukongola kwake. Iye analibe chilema chilichonse.”2 Samueli 14:25.

Koma Abisalomu anali wonyada, wodzikuza komanso wachinyengo. Choncho ngakhale anali wokongola, Baibulo silifotokoza kuti anali munthu wabwino. M’malomwake limasonyeza kuti anali wochititsa manyazi, wosakhulupirika komanso wakupha anthu.

Mpake kuti Baibulo limatilangiza kuti:

“Muvale umunthu watsopano.”Akolose 3:10.

“Kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwakunja . . . koma kukhale kwa munthu wobisika wamumtima.”1 Petulo 3:3, 4.

Si kulakwa kufuna kukhala wooneka bwino. Koma chofunika kwambiri kuposa zimenezi ndi kukhala ndi makhalidwe abwino. Ndipotu pakapita nthawi makhalidwe abwino ndi amene angachititse kuti anthu azikukondani kuposa kuoneka bwino. Mtsikana wina dzina lake Phylicia, anati: “Anthu amakopeka mosavuta ndi munthu wooneka bwino, koma munthu wakhalidwe labwino ndi amene anthu amadzamukumbukira pakapita nthawi.”

KODI MUMAMVA BWANJI MUKADZIYANG’ANIRA PAGALASI?

Kodi nthawi zambiri mumakhumudwa ndi mmene mumaonekera?

Kodi munaganizapo zochititsa opaleshoni inayake kapena kusintha zimene mumadya n’cholinga choti muzioneka bwino?

Kodi ndi zinthu ziti pathupi lanu zimene mukanakonda kuti zisinthe? (Sankhani.)

  • MSINKHU

  • KULEMERA

  • TSITSI

  • THUPI

  • NKHOPE

  • KHUNGU

Mwina mwayankha mafunso awiri oyambirira kuti “inde” komanso mwachonga zinthu ziwiri kapena kuposerapo. Komabe dziwani kuti, n’kutheka kuti anthu ena sakuonani kuti ndinu wosaoneka bwino kwambiri. Nthawi zambiri achinyamata amadera nkhawa ndi mmene amaonekera ndipo amachita zinthu zosiyanasiyana kuti azioneka bwino.—1 Samueli 16:7.