9
Kodi N’zoona Kuti Zamoyo Zinachokera ku Zinthu Zina?
KODI MUKANAKHALA INUYO MUKANATANI?
Tiyerekeze kuti mnyamata wina dzina lake Alex wakhala akukhulupirira kuti kuli Mulungu ndiponso zinthu zinachita kulengedwa. Koma lero aphunzitsi ake a sayansi aphunzitsa motsimikiza kuti nkhani yakuti zamoyo zinachokera ku zinthu zina ndi yolondola. Aphunzitsiwo akuti asayansi anachita kafukufuku pa nkhaniyi ndipo anapeza umboni wodalirika. Izi zamusokoneza kwambiri Alex koma sakufuna kuoneka ngati wotsalira. Choncho akudzifunsa kuti, ‘Ngati asayansi atsimikizira nkhaniyi, ndiye ine ndine ndani kuti nditsutse?’
Kodi inuyo mukanakhala Alex mukanangokhulupirira zimene mukuphunzirazo chifukwa zili m’mabuku a kusukulu?
MFUNDO YOFUNIKA KUIGANIZIRA
Anthu amene amati zamoyo zinachita kusintha komanso amene amati zinachita kulengedwa, nthawi zambiri amangonena kuti amakhulupirira zimenezi koma sadziwa chifukwa chake amazikhulupirira.
-
Ena amangokhulupirira kuti zinthu zinachita kulengedwa chifukwa chakuti n’zimene amaphunzitsidwa kutchalitchi.
-
Anthu ena amakhulupirira kuti zamoyo zinachokera ku zinthu zina chifukwa n’zimene anaphunzitsidwa kusukulu.
MAFUNSO 6 OFUNIKA KUWAGANIZIRA
Baibulo limati: “Nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu.” (Aheberi 3:4) Kodi zimenezi n’zoona?
ZIMENE ENA AMAKHULUPIRIRA: Zinthu zonse zinangokhalako mwangozi.
1. Ngati ndi choncho, ndani amene kapena ndi chani chimene chinachititsa kuti zinthu zikhaleko mwangozi?
2. Kodi ndi mfundo iti pa ziwirizi imene mukuona kuti ndi yomveka? Yoti zinthu zinangokhalako zokha kapena yakuti pali winawake amene anazilenga?
ZIMENE ENA AMAKHULUPIRIRA: Anthu anachokera ku nyama.
3. Ngati anthu anachokeradi ku nyama monga anyani, n’chifukwa chiyani amakhala anzeru kwambiri kuposa anyaniwo?
4. N’chifukwa chiyani zinthu zamoyo, ngakhale zing’onozing’ono kwambiri, ndi zogometsa kwabasi?
ZIMENE ENA AMAKHULUPIRIRA: Pali umboni wakuti zamoyo zinachokera ku zinthu zina.
5. Kodi munthu amene amanena zimenezi anafufuzadi n’kupeza umboni?
6. Kodi si zoona kuti ambiri amakhulupirira zoti zamoyo zinachokera ku zinthu zina chifukwa chakuti anangomva kwa anthu ophunzira kwambiri?
“Tiyerekeze kuti mukuyenda m’nkhalango ndipo mwaona nyumba yamatabwa yokongola kwambiri. Kodi mungaganize kuti; ‘Palibe amene anaimanga koma mitengo imene inkagwera pamalowa yapanga nyumbayi’? Zimenezi n’zosamveka. Ndiye mukuona kuti ndi nzeru kukhulupirira kuti zinthu zinangokhalako mwangozi?”—Julia.
“Tiyerekeze kuti munthu wina wakuuzani zoti makina pafakitale inayake yosindikiza mabuku anaphulika, inki n’kutayikira m’makoma ndi kudenga ndipo inkiyo komanso mapepala zinapanga dikishonale yabwino zedi. Kodi mungakhulupirire zimenezi?”—Gwen.
N’CHIFUKWA CHIYANI TIYENERA KUKHULUPILIRA KUTI KULI MULUNGU?
Baibulo limati muzigwiritsa ntchito ‘luntha lanu la kuganiza.’ (Aroma 12:1) Izi zikutanthauza kuti musamangokhulupirira kuti kuli Mulungu chifukwa . . .
-
CHONGOTENGEKA (Ndikuona kuti payenera kukhala winawake wamphamvu kwambiri)
-
CHONGOTSANZIRA ENA (Kudera limene ndimakhala anthu ambiri ndi opemphera)
-
CHOKAKAMIZIKA (Ndinakulira m’banja loopa Mulungu ndiye inenso ndimakhulupirira kuti kuli Mulungu. Nditasiya kukhulupirira zimenezi makolo anga angakhumudwe)
Koma inuyo panokha muyenera kupeza zifukwa zomveka zokuchititsani kukhulupirira kuti kuli Mulungu.
“Aphunzitsi athu akamafotokoza mmene matupi athu amagwirira ntchito, sindimakayikira ngakhale pang’ono zoti kuli Mulungu. Chiwalo chilichonse m’thupi lathu chimagwira ntchito yake, ndipo ntchito zina n’zing’onozing’ono kwambiri. Nthawi zambiri ziwalozi zimagwira ntchito yake ife tisakudziwa n’komwe. Kunena zoona thupi la munthu ndi logometsa.”—Teresa.
“Ndikaona nyumba zitalizitali kwambiri, sitima kapena galimoto, ndimadzifunsa kuti, ‘Kodi anapanga zinthu zimenezi ndani?’ Kuti galimoto ipangidwe, pamafunika anthu anzeru. Izi zili choncho chifukwa galimoto ili ndi zinthu zambiri zing’onozing’ono zimene zimagwira ntchito pamodzi mogwirizana. Choncho ngati panafunika winawake kuti apange galimoto, n’zoonekeratu kuti palinso winawake amene anatilenga.”—Richard.
“Ndikamaphunzira kwambiri sayansi, m’pamenenso ndimapeza umboni wamphamvu wosonyeza kuti zamoyo sizinachite kusintha kuchokera ku zinthu zina. . . . Ineyo ndimaona kuti n’zosamveka kukhulupirira kuti zinthu zinangokhalako zokha.”—Anthony.
ZOTI MUGANIZIRE
Ngakhale kuti kwa nthawi yaitali asayansi akhala akuchita kafukufuku wokhudza nkhaniyi, sanapezebe mfundo zimene onse angagwirizane. Ngati asayansi, omwe amati ndi akatswiri, sakugwirizana chimodzi pa nkhaniyi, kodi mukuona kuti n’chinthu chanzeru kumakhulupirira zoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina?