Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

ZAKUMAPETO

Chakudya Chamadzulo cha Ambuye Ndi Mwambo Umene Umalemekeza Mulungu

Chakudya Chamadzulo cha Ambuye Ndi Mwambo Umene Umalemekeza Mulungu

AKHRISTU analamulidwa kuti azichita mwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Mwambo umenewu umatchulidwanso kuti “Chakudya Chamadzulo cha Ambuye.” (1 Akorinto 11:20) Kodi mwambo umenewu ndi wofunika bwanji? Kodi uyenera kuchitika liti ndipo motani?

Yesu Khristu anayambitsa mwambo umenewu mu 33 C.E., madzulo a tsiku limene Ayuda ankachita mwambo wa Pasika. Mwambo wa Pasika unkachitika kamodzi kokha pa chaka, pa tsiku la 14 la mwezi umene Ayuda ankautchula kuti Nisani. Mwezi wa Nisani unkayamba mwezi ukaoneka pambuyo pa mlungu woyamba wa mwezi wa March. Kenako Ayuda ankachita mwambo wa Pasika pakadutsa masiku 14 kuchokera pa tsiku limene mwezi waonekalo.

Yesu anachita mwambo wa Pasika limodzi ndi ophunzira ake, kenako atachotsa Yudasi Isikariyoti pagulupo, anayambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Mwambo umenewu unalowa m’malo mwa mwambo wa Pasika umene Ayuda ankachita ndipo umayenera kuchitika kamodzi pa chaka.

Uthenga wabwino wa Mateyu umanena kuti: “Yesu anatenga mkate, ndipo atapempha dalitso, anaunyemanyema n’kuupereka kwa ophunzira ake. Iye anati: ‘Eni, idyani. Mkate uwu ukuimira thupi langa.’ Kenako anatenga kapu ndipo atayamika, anaipereka kwa iwo n’kunena kuti: ‘Imwani nonsenu. Vinyoyu akuimira “magazi anga a pangano,” amene adzakhetsedwa chifukwa cha anthu ambiri kuti machimo akhululukidwe.’”—Mateyu 26:26-28.

Anthu ena amakhulupirira kuti Yesu anasandutsa mkatewo kukhala thupi lake lenileni ndiponso vinyo kukhala magazi ake enieni. Komatu pa nthawiyi n’kuti thupi la Yesu lili bwinobwino. Kodi ophunzira a Yesu anadyadi thupi lenileni ndi kumwa magazi ake? Ayi, chifukwa kuchita zimenezo kukanakhala kudya munthu ndipo akanakhala akuphwanya lamulo la Mulungu. (Genesis 9:3, 4; Levitiko 17:10) Malinga ndi Luka 22:20, Yesu anati: “Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano pamaziko a magazi anga, amene adzakhetsedwa chifukwa cha inu.” Kodi kapuyo ndi yomwe inakhala pangano latsopano? Zimenezi n’zosatheka, chifukwa pangano sichinthu choti munthu angachione kapena kuchigwira.

Choncho mkate komanso vinyo ndi zizindikiro basi. Mkate umaimira thupi lopanda uchimo la Khristu. Yesu anagwiritsa ntchito mkate womwe unatsala pa mwambo wa Pasika. Mkate umenewu unapangidwa wopanda yisiti kapena chofufumitsa china chilichonse. (Ekisodo 12:8) Nthawi zambiri Baibulo limagwiritsa ntchito mawu akuti chofufumitsa potanthauza uchimo. Choncho mkate wopanda chofufumitsa umaimira thupi langwiro lomwe Yesu anapereka ngati nsembe. Thupi limeneli linali lopanda uchimo.—Mateyu 16:11, 12; 1 Akorinto 5:6, 7; 1 Petulo 2:22; 1 Yohane 2:1, 2.

Vinyo wofiira amaimira magazi a Yesu. Magazi amenewa ndi amene anachititsa kuti pangano latsopano liyambe kugwira ntchito. Yesu ananena kuti magazi ake anakhetsedwa kuti “machimo akhululukidwe.” Izi zikusonyeza kuti anthu akhoza kuonedwa kukhala oyera m’maso mwa Mulungu ndiponso kulowa m’pangano latsopano ndi Yehova. (Aheberi 9:14; 10:16, 17) Pangano limeneli, kapena kuti mgwirizano, ndi limene limachititsa kuti Akhristu odzozedwa okhulupirika akhale ndi mwayi wopita kumwamba. Akhristu amenewa alipo 144,000 ndipo adzakhala mafumu ndi ansembe omwe azidzatumikira anthu.—Genesis 22:18; Yeremiya 31:31-33; 1 Petulo 2:9; Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1-3.

Kodi ndi ndani amene ali woyenera kudya zizindikiro zimenezi? Anthu amene ayenera kudya mkate ndi kumwa vinyo ndi amene adzapite kumwamba, ndipo zimenezi n’zomveka chifukwa anthu amenewa ndi omwe ali m’pangano latsopano. Mzimu woyera wa Mulungu umawatsimikizira kuti asankhidwa kukakhala mafumu kumwamba. (Aroma 8:16) Anthu amenewa alinso m’pangano la Ufumu ndi Yesu.—Luka 22:29.

Nanga bwanji za anthu amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi? Anthu amenewa amamvera lamulo la Yesu ndipo amapezeka pa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, osati kuti adzadye zizindikiro, koma amangoonerera mwaulemu. Mboni za Yehova zimachita mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye kamodzi pa chaka, pa Nisani 14 dzuwa litalowa. Ngakhale kuti anthu amene amanena kuti akuyembekezera kupita kumwamba alipo masauzande ochepa okha, Akhristu onse amaonabe kuti mwambo umenewu ndi wofunika kwambiri. Imeneyi ndi nthawi imene anthu onse amayenera kuganizira za chikondi chachikulu chimene Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu anatisonyeza.—Yohane 3:16.