ZAKUMAPETO
Kodi Yesu Anabadwa mu December?
BAIBULO silitchula tsiku limene Yesu anabadwa. Komabe limafotokoza zifukwa zomveka zosonyeza kuti iye sanabadwe mu December.
Taganizirani mmene nyengo inkakhalira m’mwezi wa December, ku Betelehemu, komwe Yesu anabadwira. Mwezi wa Kisilevi pa kalendala ya Ayuda (womwe umayambira pakati pa mwezi wa November mpaka pakati pa mwezi wa December) unkakhala wozizira komanso wamvula. Mwezi wotsatira unali wa Tebeti (womwe umayambira pakati pa mwezi wa December mpaka pakati pa mwezi wa January). Nthawi imeneyi inkakhala yozizira kwambiri kuposa miyezi ina yonse ndipo nthawi zina m’madera okwera madzi ankaundana. Tiyeni tione zimene Baibulo limanena zokhudza nyengo ya m’dera limeneli.
Zimene Ezara analemba zimatitsimikizira kuti mwezi wa Kisilevi unalidi mwezi wozizira kwambiri komanso wamvula. Atafotokoza zoti anthu ambiri anasonkhana ku Yerusalemu “m’mwezi wa 9 [Kisilevi], pa tsiku la 20 la mweziwo,” iye ananena Ezara 10:9, 13; Yeremiya 36:22) N’zodziwikiratu kuti chifukwa cha nyengo imeneyi, abusa a m’derali ankaonetsetsa kuti ziweto zawo zisakhale kunja usiku m’mwezi wa December.
kuti anthuwo anali “akunjenjemera . . . chifukwa kunali kugwa mvula yamvumbi.” Pofotokoza za mmene nyengo inalili pa nthawiyi, anthu amene anasonkhanawo ananena kuti: “Ino ndi nyengo ya mvula yamvumbi, choncho n’zosatheka kuima panja.” (Koma Baibulo limafotokoza kuti usiku womwe Yesu anabadwa, abusa anali kutchire kodyetsa ziweto zawo. Ndipotu zimene Luka analemba zimasonyeza kuti pa nthawi imene Yesu anabadwa, abusa “anali kugonera kubusa akuyang’anira nkhosa zawo usiku wonse” kufupi ndi ku Betelehemu. (Luka 2:8-12) Mavesi amenewa akusonyeza kuti abusawo amagonera kutchire komweko, osati kungopitako masana n’kubwerera madzulo. Ndiye kuti nkhosa zawo amakhala nazo kutchire komweko usiku wonse. Ndiye tikaganizira zoti abusawo amakhala kutchire usiku wonse ndi ziweto zawo, kodi tingati unalidi mwezi wa December womwe unkakhala wozizira komanso wamvula? Ayi, zimenezi n’zosatheka. Choncho zimene zinachitika pa nthawi imene Yesu anabadwa, zimasonyeza kuti iye sanabadwe m’mwezi wa December. *
Mawu a Mulungu amatiuza nthawi yeniyeni imene Yesu anafa, koma sanena za tsiku lenileni limene anabadwa. Zimenezi zikutikumbutsa mawu amene Mfumu Solomo inanena akuti: “Mbiri yabwino imaposa mafuta onunkhira, ndipo tsiku lomwalira limaposa tsiku lobadwa.” (Mlaliki 7:1) Ndiye n’zosadabwitsa kuti Baibulo limafotokoza zambiri zokhudza utumiki wa Yesu ndi imfa yake, koma silinena zambiri za tsiku limene anabadwa.
^ ndime 1 Kuti mumve zambiri pa nkhaniyi, onani tsamba 239-242 m’buku la Kukambitsirana za m’Malemba, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.