MUTU 12
Khalani ndi Makhalidwe Amene Mulungu Amasangalala Nawo
-
Kodi mungatani kuti Mulungu akhale mnzanu?
-
Kodi zimene Satana anachita potsutsa ulamuliro wa Yehova zimakukhudzani bwanji?
-
Kodi Yehova sasangalala ndi makhalidwe ati?
-
Kodi mungatani kuti mukhale ndi makhalidwe amene Mulungu amasangalala nawo?
1, 2. Kodi ndi anthu ati amene Yehova ankawaona ngati anzake apamtima?
KODI ndi munthu wotani amene mungakonde kuti akhale mnzanu? Sitikukayikira kuti mungasankhe munthu amene maganizo ake, zimene amakonda, komanso mfundo zimene amatsatira pa moyo wake n’zofanana ndi zanu. Komanso mungakonde kugwirizana ndi munthu amene ali ndi makhalidwe abwino, monga kuona mtima ndiponso kuganizira ena.
2 Kuyambira kale, Mulungu wakhala akusankha anthu osiyanasiyana kuti akhale anzake apamtima. Mwachitsanzo, Yehova anatchula Abulahamu kuti ndi bwenzi lake. (Werengani Yesaya 41:8; Yakobo 2:23.) Mulungu ananenanso kuti Davide anali “munthu wapamtima” pake. (Machitidwe 13:22) Komanso Yehova ankaona kuti mneneri Danieli anali “munthu wokondedwa kwambiri.”—Danieli 9:23.
3. Kodi ndi anthu otani amene Yehova anasankha kuti akhale anzake?
3 N’chifukwa chiyani Yehova ankaona anthu monga Abulahamu, Davide ndi Danieli ngati anzake apamtima? Nthawi ina iye anauza Abulahamu kuti: “Wamvera mawu anga.” (Genesis 22:18) Izi zikusonyeza kuti Yehova amakonda anthu odzichepetsa amene amachita zimene iyeyo amafuna. N’chifukwa chake anauza Aisiraeli kuti: “Muzimvera mawu anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, inuyo mudzakhala anthu anga.” (Yeremiya 7:23) Choncho nafenso tikhoza kukhala anzake a Yehova ngati timamumvera.
YEHOVA AMALIMBIKITSA ANTHU AMENE ALI NAYE PA UBWENZI
4, 5. Kodi Yehova amasonyeza bwanji mphamvu zake kwa anthu ake?
4 Taganizirani za ubwino wokhala pa ubwenzi ndi Mulungu. Baibulo limanena kuti Yehova amafunafuna mpata woti “aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Kodi Yehova angaonetse bwanji mphamvu zake kwa inu? Njira imodzi imene angachitire zimenezi yafotokozedwa pa Salimo 32:8, pomwe timawerenga kuti: “Ndidzakupatsa nzeru ndi kukulangiza njira yoti uyendemo. Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anira.”
5 Mawu amenewa akusonyeza mmene Yehova amasamalilira anthu ake. Iye adzakupatsani malangizo ndiponso kukuyang’anirani mukamawagwiritsa ntchito. Mulungu akufuna kukuthandizani kuti muthe kupirira mayesero amene mumakumana nawo. (Werengani Salimo 55:22.) Choncho mukamatumikira Yehova ndi mtima wonse, mungalankhule motsimikiza ngati mmene ananenera wamasalimo kuti: “Ndaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse. Popeza kuti ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.” (Salimo 16:8; 63:8) Zimenezi zikutanthauza kuti Yehova angakuthandizeni kuti mukhale ndi makhalidwe amene amasangalala nawo. Koma monga mmene mukudziwira, pali mdani wa Mulungu amene amafuna kukulepheretsani kuchita zimenezi.
ZIMENE SATANA ANATSUTSA
6. Kodi Satana anakayikira zoti chiyani?
6 Mutu 11 unafotokoza mmene Satana Mdyerekezi anatsutsira ulamuliro wa Mulungu. Satana ananena kuti Mulungu ndi wabodza ndipo sanachite bwino posalola kuti Adamu ndi Hava azisankha okha zochita, kaya zabwino kapena zoipa. Pambuyo poti Adamu ndi Hava achimwa ndipo ana awo ayamba kuchuluka padziko lapansi, Satana anakayikira zoti anthu amatumikira Mulungu chifukwa chomukonda. Iye anati, ‘Anthu satumikira Mulungu chifukwa choti amamukonda. Ingondipatsani mpata ndipo muona, nditha kuchititsa kuti aliyense asiye kutumikira Mulungu.’ Nkhani ya Yobu imasonyeza kuti Satana amakhulupirira zimenezi. Koma kodi Yobu anali ndani, nanga anakhudzidwa bwanji ndi maganizo a Satana oti anthu satumikira Mulungu chifukwa chomukonda?
7, 8. (a) Kodi n’chiyani chinachititsa Yobu kuti akhale wosiyana ndi anthu a m’nthawi yake? (b) Kodi Satana ananena kuti Yobu ankatumikira Mulungu chifukwa cha chiyani?
Yobu 1:8) Izi zikusonyeza kuti Mulungu ankasangalala ndi zochita zake.
7 Yobu anakhala ndi moyo zaka pafupifupi 3,600 zapitazo. Iye anali munthu wabwino moti Yehova ananena kuti: ‘Palibe wina wokhala ngati iyeyo padziko lapansi. Iyetu ndi munthu wopanda cholakwa ndi wowongoka mtima, woopa Mulungu ndi wopewa zoipa.’ (8 Koma Satana ankakayikira zolinga zimene Yobu anali nazo potumikira Mulungu. Mdyerekezi anauza Yehova kuti: “Kodi inuyo simwam’tchinga iyeyo? Mwatchingiranso nyumba yake ndi chilichonse chimene ali nacho. Mwadalitsa ntchito ya manja ake ndipo ziweto zake zachuluka kwambiri padziko lapansi. Koma tsopano tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza zonse zimene ali nazo, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!”—Yobu 1:10, 11.
9. Kodi Yehova anachita chiyani pofuna kuyankha zimene Satana ananena, nanga n’chifukwa chiyani anachita zimenezi?
9 Polankhula mawu amenewa, Satana anasonyeza kuti ankaona kuti Yobu ankatumikira Mulungu chifukwa cha zimene Mulunguyo ankamupatsa. Satana ananenanso kuti Yobu akhoza kusiya kutumikira Mulungu ngati atayesedwa. Kodi Yehova anatani Satana atalankhula zimenezi? Popeza nkhaniyi inkakhudza zolinga za Yobu potumikira Mulungu, Yehova analola kuti Satana amuyese Yobu. Zimenezi zikanathandiza kuti zioneke ngati Yobu amakondadi Mulungu kapena ayi.
MMENE YOBU ANAYESEDWERA
10. Kodi Yobu anakumana ndi mayesero otani, nanga anachita zotani?
10 Satana atangopatsidwa mwayi, anayesa Yobu m’njira zingapo. Ziweto zina za Yobu zinabedwa, pomwe zina zinaphedwa. Antchito ake ambiri anaphedwa. Zimenezi zinachititsa kuti akhale ndi mavuto azachuma. Zinthu zinafika poipa kwambiri pamene ana ake okwana 10 anafa ndi mphepo yamkuntho. Komabe, ngakhale kuti anakumana ndi mavuto onsewa, “Yobu sanachimwe, kapena kunena kuti Mulungu wachita zosayenera.”—Yobu 1:22.
11. (a) Kodi maganizo ena amene Satana anali nawo okhudza Yobu anali otani, nanga Yehova anamuyankha bwanji? (b) Kodi Yobu anatani atadwala kwambiri?
11 Satana sanasiyire pomwepo. Iye ayenera kuti ankaganiza zoti Yobu 27:5.
ngakhale kuti Yobu anapirira kuphedwa kwa ana ake ndi antchito ake, ndiponso kubedwa ndi kuwonongeka kwa chuma chake, akhoza kusiya kutumikira Mulungu ngati atadwala kwambiri. Yehova analola kuti Satana achititse Yobu kudwala matenda opweteka kwambiri, omwe ananyansitsa thupi lake lonse. Koma Yobu sanasiyebe kukhulupirira Mulungu. M’malomwake, analankhula molimba mtima kuti: “Mpaka ine kumwalira, sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.”—12. Kodi zochita za Yobu zinasonyeza bwanji kuti zimene Satana ananena ndi zabodza?
12 Yobu sankadziwa kuti Satana ndi amene akuchititsa mavuto akewo. Chifukwa choti sankadziwa zimene Mdyerekezi ananena potsutsa ulamuliro wa Yehova, Yobu ankaona ngati Mulungu ndi amene akuchititsa mavutowo. (Yobu 6:4; 16:11-14) Komabe, anapitirizabe kutumikira Mulungu mokhulupirika. Ndipo kukhulupirika kwa Yobu kunasonyeza kuti zimene Satana ananena zoti iye ankatumikira Mulungu ndi zolinga zadyera n’zabodza.
13. Kodi n’chiyani chinachitika chifukwa cha kukhulupirika kwa Yobu?
13 Kukhulupirika kwa Yobu kunathandizanso kuti Yehova ayankhe ndi mphamvu pa mawu achipongwe amene Satana ananena. Yobu anasonyeza kuti analidi pa ubwenzi wabwino ndi Yehova, ndipo Mulungu anamudalitsa chifukwa cha kukhulupirika kwake.—Yobu 42:12-17.
NKHANI IMENEYI IKUKUKHUDZANI
14, 15. N’chifukwa chiyani tinganene kuti zimene Satana ananena pa nkhani ya Yobu zikukhudza anthu onse?
14 Nkhani yonena za kukhala wokhulupirika kwa Mulungu imene Satana anayambitsa sinkakhudza Yobu yekha. Inunso ikukukhudzani. Zimenezi zikuonekera bwino pa lemba la Miyambo 27:11, pomwe Mawu a Yehova amati: “Mwana wanga, khala wanzeru ndi kukondweretsa mtima wanga, kuti ndimuyankhe amene akunditonza.” Mawu amenewa omwe ananenedwa patadutsa zaka zambirimbiri kuchokera pamene Yobu anamwalira, akusonyeza kuti Satana anali adakanyozabe Mulungu ndiponso kuneneza atumiki ake. Tikakhala ndi makhalidwe amene Yehova amasangalala nawo, timakhala tikumuthandiza kuyankha zinthu zabodza zimene Satana amanena ndiponso timakhala tikusangalatsa mtima wake. Kodi simukuona kuti ndi mwayi waukulu kuthandiza nawo posonyeza kuti zimene Mdyerekezi ananena ndi zabodza? Kuti tichite zimenezi, nthawi zina tingafunikire kusintha zinthu zina pa moyo wathu.
15 Kumbukirani kuti Satana ananena kuti: “Munthu angalolere kupereka chilichonse chimene ali nacho kuti apulumutse moyo wake.” (Yobu 2:4) Pamene ananena kuti “munthu,” Satana anasonyezeratu kuti zimene ananenazo sizikukhudza Yobu yekha, koma anthu onse. Kudziwa mfundo imeneyi n’kofunika kwambiri. Satana amakayikira zolinga zanu potumikira Mulungu mokhulupirika. Iye amafuna kuti musamamvere Mulungu ndiponso kuti musamatsatire malamulo ake pamene mwakumana ndi mavuto. Kuti zimenezi zitheke, kodi Satana angagwiritse ntchito njira zotani?
16. (a) Kodi Satana amagwiritsa ntchito njira zotani akafuna kuti anthu asiye kutumikira Mulungu? (b) Kodi Satana angagwiritse ntchito bwanji njira zimenezi kuti akusocheretseni inuyo?
16 Monga tinaphunzirira m’Mutu 10, Satana amagwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana akafuna kuti atisocheretse ndipo tisiye kutumikira Mulungu. Njira imodzi ndi yoti amatiukira “ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” (1 Petulo 5:8) Pogwiritsa ntchito njira imeneyi, zochita za Satana zimachita kuonekeratu chifukwa angachititse anzathu, achibale athu, kapenanso anthu ena kuti azitsutsa zolinga zathu zofuna kuphunzira Baibulo ndiponso kutsatira zimene tikuphunzirazo. * (Yohane 15:19, 20) Koma nthawi zina “Satana amadzisandutsa mngelo wa kuwala.” (2 Akorinto 11:14) Mdyerekezi akhoza kugwiritsa ntchito njira zovuta kuzizindikira n’cholinga choti akusocheretseni ndiponso kukunyengererani kuti musiye kuchita zimene Mulungu amafuna. Nthawi zinanso akhoza kungokugwetsani ulesi, kapena kukuchititsani kuti muziona ngati simungakwanitse kuchita zimene Mulungu amasangalala nazo. (Miyambo 24:10) Kaya Satana angalimbane nanu pochita zinthu ngati “mkango wobangula,” kapena ngati “mngelo wa kuwala,” komabe maganizo ake sasintha. Amaonabe kuti mungasiye kutumikira Mulungu ngati mutakumana ndi mavuto aakulu kapena mayesero. Kodi mungachite chiyani kuti musonyeze kuti zimene Satana ananena ndi zabodza ndiponso kuti musonyeze kuti ndinu wokhulupirika ngati Yobu?
KUMVERA MALAMULO A YEHOVA
17. Kodi chifukwa chachikulu chimene chimatichititsa kutsatira malamulo a Yehova n’chiyani?
17 Mungasonyeze kuti zimene Satana ananena ndi zabodza ngati mutamachita zinthu zimene Mulungu amasangalala nazo. Koma kodi n’chiyani chingatithandize kuchita zimenezi? Baibulo limayankha kuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse.” (Deuteronomo 6:5) Mukayamba kukonda kwambiri Mulungu, mungamafunitsitse kuchita zimene iye amafuna kuti muzichita. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake.” Ndipo ngati mumakonda Yehova ndi mtima wanu wonse, mudzaona kuti “malamulo akewo ndi osalemetsa.”—1 Yohane 5:3.
18, 19. (a) Kodi ena mwa malamulo a Mulungu ndi ati? (Onani bokosi patsamba 122.) (b) Kodi tikudziwa bwanji kuti Mulungu satiuza kuchita zinthu zimene sitingakwanitse?
18 Kodi ena mwa malamulo a Yehova ndi ati? Ena amanena za makhalidwe amene tiyenera kuwapewa. Mwachitsanzo, onani bokosi lakuti “ Muzipewa Zinthu Zimene Yehova Amadana Nazo,” lomwe lili patsamba 122. M’bokosi limeneli muli malamulo omveka bwino onena za zinthu zimene Baibulo limaletsa. Makhalidwe ena ndi oti ukawawerenga angaoneke ngati si oipa kwenikweni. Koma mukaganizira mofatsa mfundo zimene zili m’malemba amene atchulidwawo, mungaone kuti malamulo a Yehova ndi othandiza kwambiri. Kusintha khalidwe lanu kukhoza kukhala kovuta kwambiri kuposa zinthu zina zonse. Komabe, kuchita zinthu zimene Yehova amasangalala nazo kumapangitsa munthu kuti azikhala ndi moyo wosangalala. (Yesaya 48:17, 18) Ndipotu zimenezi ndi zoti mukhoza kukwanitsa. Kodi n’chiyani chikutipangitsa kuona kuti tikhoza kukwanitsa?
19 Yehova satiuza kuchita zinthu zimene sitingakwanitse. (Werengani Deuteronomo 30:11-14.) Iye amadziwa zinthu zimene tingakwanitse komanso zimene sitingakwanitse kuposa mmene ifeyo timadzidziwira. (Salimo 103:14) Kuwonjezera pamenepa, Yehova akhoza kutipatsa mphamvu zoti zitithandize pochita zimene akufuna. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulungu ndi wokhulupirika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire, koma pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.” (1 Akorinto 10:13) Kuti muthe kupirira zinthu zimene mukukumana nazo, Yehova akhozanso kukupatsani “mphamvu yoposa yachibadwa.” (2 Akorinto 4:7) Paulo atakwanitsa kupirira mayesero ambirimbiri analemba kuti: “Pa zinthu zonse, ndimapeza mphamvu kuchokera kwa iye amene amandipatsa mphamvu.”—Afilipi 4:13.
KHALANI NDI MAKHALIDWE AMENE MULUNGU AMASANGALALA NAWO
20. Kodi ndi makhalidwe ati amene Yehova amasangalala nawo omwe inuyo muyenera kukhala nawo, nanga makhalidwe amenewa ndi ofunika bwanji?
20 Komatu palinso zina zimene mungachite kuti musangalatse Aroma 12:9) Tikukhulupirira kuti inuyo mumagwirizana kwambiri ndi anthu amene maganizo awo, zimene amakonda, ndiponso mfundo zimene amayendera pa moyo wawo n’zofanana ndi zanu. Yehova amachitanso chimodzimodzi. Choncho, muyenera kuphunzira kukonda zinthu zimene Yehova amazikonda. Zina mwa zinthu zimenezi zinatchulidwa mu Salimo 15, momwe timawerenga za anthu amene Yehova amawaona kuti ndi anzake. (Werengani Salimo 15:1-5.) Anthu amene Yehova amawaona kuti ndi anzake amakhala ndi “makhalidwe amene mzimu woyera umatulutsa.” Makhalidwe amenewa akuphatikizapo “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa ndi kudziletsa.”—Agalatiya 5:22, 23.
Yehova. Kuwonjezera pa kupewa zinthu zimene amadana nazo, muyenera kukonda zimene iyeyo amakonda. (21. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kukhala ndi makhalidwe amene Mulungu amasangalala nawo?
21 Kuwerenga ndiponso kuphunzira Baibulo nthawi zonse kudzakuthandizani kuti mukhale ndi makhalidwe amene Mulungu amasangalala nawo. Ndipo kuphunzira zimene Mulungu amafuna kudzakuthandizani kusintha maganizo anu kuti azigwirizana ndi maganizo ake. (Yesaya 30:20, 21) Mukamayesetsa kuti muzikonda kwambiri Yehova, m’pamenenso mudzakhale ndi mtima wofunitsitsa kuchita zinthu zimene amasangalala nazo.
22. Kodi chingachitike n’chiyani mukamachita zinthu zimene Mulungu amasangalala nazo?
22 Kukhala ndi makhalidwe amene Yehova amasangalala nawo kumafuna khama. Baibulo limafotokoza kuti kusintha khalidwe lakale kuli ngati kuvula zovala zakale n’kuvala zatsopano. (Akolose 3:9, 10) Koma wolemba masalimo ananena kuti: “Munthu wosunga zigamulozo [malamulo a Yehova] amapeza mphoto yaikulu.” (Salimo 19:11) Nanunso mudzaona kuti kuchita zinthu zimene Mulungu amasangalala nazo kumabweretsa madalitso ambiri. Mukamachita zimenezi, mudzasonyeza kuti zimene Satana ananena ndi zabodza komanso mudzasangalatsa mtima wa Yehova.
^ ndime 16 Zimenezi sizikusonyeza kuti munthu aliyense amene amakutsutsani akutsogoleredwa ndi Satana. Koma Satana ndi amene ali mulungu wa nthawi inoyo ndipo dziko lonse lapansi lili m’manja mwake. (2 Akorinto 4:4; 1 Yohane 5:19) Choncho, n’zochita kudziwikiratu kuti anthu ambiri sangakonde kutsatira malamulo a Mulungu ndipo ena angamakutsutseni pamene mukutsatira malamulowo.