Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MUTU 5

Zimene Mungachite Kuti Muzigwirizana ndi Achibale

Zimene Mungachite Kuti Muzigwirizana ndi Achibale

“Valani . . . kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa, ndi kuleza mtima.”—Akolose 3:12

N’zoona kuti mukakwatirana, mumakondabe makolo anu koma munthu wofunika kwambiri tsopano ndi mwamuna kapena mkazi wanu. Achibale ena angavutike kuvomereza zimenezi. Koma mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni kuti mupitirize kugwirizana ndi achibale anu pamene mukulimbitsa banja lanu latsopano.

1 MUZIWALEMEKEZA

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako.” (Aefeso 6:2) Kaya muli ndi zaka zingati, muyenera kulemekezabe makolo anu. Muzikumbukira kuti mwamuna kapena mkazi wanu nayenso ayenera kulemekeza makolo ake. Pajatu “chikondi sichichita nsanje,” choncho simuyenera kuchita nsanje ngati mnzanuyo amagwirizana kwambiri ndi makolo ake.—1 Akorinto 13:4; Agalatiya 5:26.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Muzipewa kunena mawu ngati akuti, “Achibale ako amandiderera nthawi zonse” kapena akuti, “Nthawi zonse, mayi ako sasangalala ndi zimene ndimachita”

  • Yesetsani kumvetsa maganizo a mwamuna kapena mkazi wanu

2 MUZIKHALA NDI MALIRE

ZIMENE BAIBULO LIMANENA: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:24) Mukalowa m’banja, makolo anu angaonebe kuti ayenera kukusamalirani ndipo angayambe kulowerera banja lanu.

Choncho inuyo ndi mwamuna kapena mkazi wanu muyenera kukambirana malire a zimene makolo anu angachite n’kuwafotokozera mokoma mtima. Muziwafotokozera momasuka ndiponso mosabisa mawu koma mwaulemu. (Miyambo 15:1) Makhalidwe monga kudzichepetsa, kufatsa komanso kuleza mtima angakuthandizeni kuti muzigwirizana ndi achibale anu komanso kukhala ololera pochita nawo zinthu.—Aefeso 4:2.

ZIMENE MUNGACHITE:

  • Ngati mukuona kuti achibale akulowerera kwambiri banja lanu, muyenera kupeza nthawi yabwino n’kukambirana ndi mwamuna kapena mkazi wanu

  • Muyenera kugwirizana zimene mungachite pothana ndi vutoli