Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
Werengani kuti mumve zimene a Mboni za Yehova achita mu 2014 ndiponso mbiri ya Mboni za Yehova ku Dominican Republic.
Lemba la Chaka cha 2015
Lemba la chaka cha 2015 lachokera pa Salimo 106:1 ndipo ndi lakuti: “Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino.”
Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira
Bungwe Lolamulira likuyamikira Akhristu onse padziko lapansi chifukwa cha ntchito zawo zachikondi, kukhulupirika komanso kupirira.
Zinthu Zikuyenda ku Warwick
Onani zinthu zosangalatsa zimene zachitika pamalo amene akumanga likulu la Mboni za Yehova.
Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga Padziko Lonse
Dipatimenti yatsopanoyi iyenera kuonetsetsa kuti ntchito yomanga ikuyenda bwinobwino kumalo oposa 13,000.
Baibulo la Dziko Latsopano Ndi Lolimba Kwambiri
Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso limene linatuluka mu 2013 ndi lokongola komanso lolimba kwambiri.
Msonkhano Waukulu Kwambiri wa Mboni za Yehova
Anthu ambirimbiri kuposa kale anamvetsera msonkhano wapachaka wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania wa nambala 129.
Mwambo Wotsegulira Ofesi ya Nthambi ku Sri Lanka
Anthu m’madera osiyanasiyana anatha kuonera pulogalamuyi m’masikirini.
Lipoti la Milandu
A Mboni za Yehova akuyesetsa kuti akhale ndi ufulu wolambira.
Malipoti Apadera a Zochitika M’mayiko Osiyanasiyana
N’chifukwa chiyani tiatsikana tina tiwiri tinapereka ndalama zogulira foni kuti zithandize pa ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu?
“Taona Zodabwitsa”
Kodi ndi zinthu ziti masiku ano zimene zikufanana ndi zodabwitsa zimene zinkachitika Yesu ali padzikoli?
Africa
Werengani zimene Mboni za Yehova zachita pophunzitsa anthu ku Angola, Congo (Kinshasa), Ghana, Nigeria, ndi South Africa mu 2014.
North ndi South America
Werengani ntchito yathu yophunzitsa Baibulo ku Argentina, Brazil, Haiti, Paraguay, ndi ku Suriname mu 2014.
Ku Asia ndi ku Middle East
Werengani ntchito ya Mboni za Yehova yophunzitsa anthu ku Indonesia, Mongolia, ku Philippines, ndi ku dziko lina la ku Asia mu 2014.
Europe
Werengani ntchito ya Mboni za Yehova yophunzitsa anthu ku Bulgaria, Finland, Germany, Romania, Russia, Spain ndi ku Sweden mu 2014.
Oceania
Werengani ntchito yathu yophunzitsa anthu ku Kiribati, Marshall Islands, Papua New Guinea ndi ku Vanuatu mu 2014.
Mfundo Zachidule Zokhudza Dominican Republic
Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mfundo zachidule zokhudza dzikoli komanso anthu ake.
Ntchito Inayambika
Kodi amishonale oyambirira anayamba liti kuphunzitsa anthu Baibulo ku Dominican Republic?
“Tidzawapeza”
Pablo González anapeza anthu amene ankawafufuza patatha zaka 13.
Anamangidwa Ndipo Ntchito Yolalikira Inaletsedwa
Kodi n’chiyani chinathandiza anthu ena a Mboni za Yehova kuti apirire mavuto oopsa amene ankakumana nawo kundende?
Ntchito Yolalikira Inapitirirabe
Polemba maola ndi maulendo obwereza, ofalitsa ankangolemba zinthu monga kabichi ndi spinachi.
Ufulu Wosayembekezereka Kenako N’kuletsedwanso
Ntchito ya a Mboni za Yehova inaletsedwa kwa zaka 6 kenako mu 1956 anapatsidwa ufulu kwa miyezi 11 yokha.
Ubwenzi wa Trujillo ndi Tchalitchi cha Katolika
Akuluakulu a Katolika ankaikira kumbuyo ulamuliro wa Trujillo kwa nthawi yaitali koma anasintha maganizo n’kupepesa anthu a ku Dominican Republic.
Anazunzidwa Koopsa
A Mboni anaukiridwa koopsa koma sanabwerere m’mbuyo.
Kodi Mutu Ndi Ndani?
Ankagwiritsa ntchito makina opanga fotokope, chitini cha mafuta, saka ndi chinangwa pothandiza kuti abale azilandira magazini pa nthawi ya bani.
Tikanatha Kumangidwa Nthawi Iliyonse
Ngakhale kuti a Mboni za Yehova ku Domincan Republic analetsedwa kusonkhana, sanasiye koma ankasamala kwambiri kuti anthu asadziwe.
Sanasiye Kulalikira Ndipo Analandira Ufulu
Kwa zaka zambiri, ntchito ya Mboni za Yehova ku Dominican Republic inali yoletsedwa. Koma munthu amene ankaganiza kuti sangawathandize anachotsa baniyo.
“Ndinkamenya Nkhondo Ngati Mkango”
Luis Eduardo Montás, anayesa kawiri kuti aphe pulezidenti. Pamene ankayesa kachitatu, anapeza mwayi wophunzira Baibulo.
“Ufumu wa Mulungu Si Nkhambakamwa”
Efraín De La Cruz anatsekeredwa m’ndende 7 ndiponso kumenyedwa koopsa chifukwa cholalikira uthenga wabwino. N’chiyani chinamuthandiza kuti azilalikira mwakhama kwa zaka zoposa 60?
“Sindidzasiya Kukhala wa Mboni za Yehova”
Wansembe anauza Mary Glass kuti apenga akawerenga Baibulo. Koma analiwerengabe ndipo anazindikira chifukwa chake wansembe uja sankafuna kuti aliwerenge.
Ufulu Wolalikira
Trujillo ataphedwa, amishonale ambiri anafika ndipo pang’ono ndi pang’ono anthu anasiya kudana ndi Mboni za Yehova.
A Mboni za Yehova Akhazikika
Ntchito yolalikira inkayenda bwino ngakhale panali mavuto azandale. Kodi n’chiyani chinasonyeza kuti a Mboni za Yehova akhazikika ku Dominican Republic?
Panafunika Olalikira Ufumu Ambiri
Nkhani yokhudza Mboni za Yehova ku Dominican Republic singakhale yosangalatsa ngati sitingafotokoze za anthu amene anamvera pempho loti adzalalikire m’dzikoli.
A Mboni za Yehova Amathandizana
Chimphepo chitawononga ku Dominican Republic mu 1998, a Mboni za Yehova anathandizana kwambiri ndipo izi zinalemekeza Yehova Mulungu.
Panafunika Kumanga Malo Ena Olambirira
Kodi a Mboni za Yehova anatani ataona kuti malo ochitira misonkhano akuchepa ndipo pakufunika abale oyenerera kuti azitsogolera?
Gawo la Chikiliyo cha ku Haiti
A Mboni za Yehova akulalikira uthenga wabwino kwa anthu olankhula Chikiliyo cha ku Haiti. Panopa kuli mipingo yambiri ndipo anthu ambiri akuphunzira chilankhulochi.
Ku Haiti Kunachitika Chivomezi
Ku Haiti kutachitika chivomezi mu 2010, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Dominican Republic inapereka chithandizo chambiri. Abale ambiri anapitanso kukathandiza.
Ofalitsa Akuwonjezereka
Ntchito yolalikira ku Dominican Republic inayambika mu 1945. Abale akungoyembekezera kuti zinthu zikhala bwanji mtsogolo.
Yehova Watsegula Mitima ya Anthu Ambiri
Nthawi imene Leonardo Amor anali mumzinda wa La Vega, palibe amene ankafuna kuphunzira Baibulo. Koma kenako mitima ya anthu ambiri inadzasintha.
Anthu 22 Anasiya Tchalitchi Chawo
Anthu ankanena kuti zimene a Mboni za Yehova ankaphunzitsa zinali za jabulosi komanso zosokoneza. Koma a Mboniwo ankagwiritsa ntchito Baibulo poyankha mafunso mofika pa mtima.
Sankakhulupirira Zoti Kuli Mulungu Kenako Anayamba Kumutumikira
Juan Crispín sankakhulupirira zoti kuli Mulungu ndipo ankaona kuti kusintha maboma andale n’kumene kungathetse mavuto m’dzikoli. Kodi n’chiyani chomwe chinamusintha maganizo kuti ayambe kutumikira Mulungu?
Munthu Woyamba wa Chinenero Chamanja Kuphunzira Baibulo
José Pérez anali munthu wa Chinenero Chamanja woyamba kukhala wa Mboni ku Dominican Republic. Kodi ndi nthawi iti imene anayamba kumvetsa bwino mfundo za m’Baibulo?
Ndinazindikira Cholinga cha Moyo
José Estévez ndiponso banja lake anazindikira cholinga cha moyo. Kodi atsimikizira bwanji kuti Yehova amakwaniritsadi mawu ake?
Ndinkafuna Kusiya Kutumikira Mulungu
Ngakhale kuti Martín Paredes ankaphunzira za unsembe anakhumudwa ndipo ankafuna kusiya kutumikira Mulungu. Kodi buku limene anabwereka linamuthandiza bwanji?
Zaka 100 Zapitazo—1915
Kodi a Mboni za Yehova anatani atakumana ndi mayesero chaka cha 1914 chitadutsa?