Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zaka 100 Zapitazo—1915

Zaka 100 Zapitazo—1915

NSANJA YA OLONDA ya March 1, 1915, inanena kuti: “Tili m’nthawi ya mayesero. Kodi tinkachita khama pa utumiki wathu chifukwa tinkayembekezera kupita kumwamba mu 1914? Kapena tinkachita khama ndiponso tinali okhulupirika chifukwa chokonda Ambuye, ntchito yake ndiponso abale athu?” Magaziniyi inanena chonchi chifukwa mu 1915, Ophunzira Baibulo ena anali okhumudwabe ndipo anthu ambiri m’dzikoli analinso pa mavuto ena.

Pa nthawiyi, nkhondo yoyamba ya padziko lonse inali itavuta ku Ulaya. Zida zoopsa zinkagwiritsidwa ntchito zomwe zinachititsa kuti anthu wamba avutike kwambiri. Mwachitsanzo mu 1915, sitima za nkhondo za pansi pa nyanja za dziko la Germany, zinkakonda kudutsa pafupi ndi dziko la Britain. Pa May 7, 1915, sitima yankhondo ya ku Germany, inamiza sitima ina yonyamula anthu ya dziko la Britain ndipo anthu oposa 1,100 anafa.

Sanamenye Nawo Nkhondo

Ophunzira Baibulo sanamenye nawo nkhondoyi. Iwo anachita izi ngakhale kuti sankamvetsa bwinobwino zimene Baibulo limanena pa nkhani ya kusalowerera nkhondo. Iwo sankalowa usilikali koma ena ankavomera akauzidwa kuti akamenye nawo nkhondo. Abalewa ankapempha kuti azipatsidwa ntchito zina m’malo mogwira mfuti. Nthawi zina akakakamizidwa kumenya nawo nkhondoyi, iwo ankangowombera m’mwamba.

Nsanja ya Olonda ya July 15, 1915, inafotokoza za msilikali wina wa ku Hungary. Iye anavulala kunkhondo ndipo anabatizidwa pa nthawi yomwe ankachira. Koma kenako anabwereranso ku nkhondo. Magaziniyo inafotokoza zomwe zinamuchitikira. Ndipo inati: “Asilikali a dziko la Hungary atatsala pang’ono kukumana ndi asilikali a dziko la Russia, analamulidwa kuti agwiritse ntchito zida zobayira. Pa nthawiyi m’bale uja anali chakumapeto kwa gulu la asilikali. Iye atakumana ndi msilikali wa ku Russia anaganiza zongolanda mdani wakeyo chida chake. Koma m’baleyu anadabwa poona kuti msilikali uja amafuna kuchitanso zomwezo. . . Ndipo msilikali wa ku Russia anangotaya chidacho n’kuyamba kulira. Kenako m’bale wathu atamuyang’anitsitsa anaona kuti wavala kabaji kokhala ndi mtanda ndi chisoti chachifumu. Iye anazindikira kuti anali m’bale wake mwa Ambuye.” *

Nsanja ya Olonda ya September 1, 1915, inali ndi nkhani yakuti; “Kodi Akhristu Ayenera Kumenya Nawo Nkhondo?” Magaziniyi inafotokoza bwino kuti Akhristu sayenera kumenya nawo nkhondo. Inanena kuti munthu akalowa usilikali, kaya wangovala unifolomu ya usilikali, zimasonyeza kuti akuvomereza kuchita ntchito zonse zogwirizana ndi usilikaliwo . . . Kodi pamenepa tinganene kuti munthuyo akukwaniritsa udindo wake monga Mkhristu?” Koma patapita nthawi, Ophunzira Baibulo anamvetsa bwino kuti sayenera kumenya nawo nkhondo.

Zinthu Zinasintha Kulikulu

Mu 1915, anthu 70 omwe ankatumikira pa Beteli ku New York, anauzidwa kuti asiye kaye utumikiwo chifukwa cha mavuto azachuma ndipo akapitirize kugwira ntchito yolalikira. Iwo anauzidwa kuti: “Sitikufuna kukhala ndi ngongole kapena kusokoneza ntchitoyi. N’chifukwa chake taganiza zochepetsa ndalama zimene timagwiritsa ntchito.”

M’bale Clayton J. Woodworth ndiponso abale ena awiri, anasaina kalata yomwe abale 70 amene anauzidwa kuchoka pa beteli analemba. Kalatayi inaikidwa m’magazini ya Nsanja ya Olonda ya May 1, 1915. Abale omwe anachokawa anasangalala kwambiri ndiponso anali oyamikira chifukwa cha zinthu zambiri zomwe anaphunzira nthawi yomwe anali pa Beteli.

Ngakhale kuti zinali zovuta kusiya utumikiwu, abalewa anali ndi mwayi wosonyeza kukhulupirika kwawo. Kodi anapitiriza kutumikira Mulungu mokhulupirika kapena anakwiya? M’bale Woodworth anapitirizabe kugwira ntchito yolalikira moti anadzayambiranso kutumikira pabeteli. Mu 1919, iye anali ndi mwayi wokhala mkonzi woyamba wa magazini ya The Golden Age, yomwe masiku ano timati Galamukani! Iye anakhala mkonzi wa maganiziyi mpaka mu 1946.

Mwayi Wothandiza Anthu

Pa zaka zovutazi, magazini a Nsanja ya Olonda analimbikitsa abale kuti apitirize kugwira ntchito yolalikira. Panakonzedwanso zothandiza anthu omwe kale anasonyeza chidwi, moti magazini ya Nsanja ya Olonda ya December 15, 1915, inanena kuti: “Tili ndi mayina a anthu osiyanasiyana omwe anapempha kuti tiziwapatsa mabuku athu. Tikuganiza kuti anthu amenewa tiwayenderenso kuti tione ngati adakali ndi chidwi.” Cholinga cha nkhaniyi chinali “kulimbikitsa anthu amene anasonyeza chidwi kuti azikonda kwambiri Mulungu ndiponso mfundo za m’Baibulo.”

Pa nthawiyi, zinali zoonekeratu kuti Akhristu anafunika kuika maganizo awo onse pa ntchito ya Ufumu. Nsanja ya Olonda ya February 15, 1915, inanena kuti: “Popeza tili maso tiyenera kugwira ntchito yolalikira mwakhama.” Atumiki a Mulungu anafunika kukhala tcheru. Magaziniyi inapitiriza kunena kuti: “N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala tcheru? Tiyenera kuchita zimenezi kuti tipewe misampha ya masiku ano.”

Mpake kuti lemba la chaka cha 1916, linalimbikitsa abale kukhalabe olimba m’chikhulupiriro. Lembali linachokera pa Aroma 4:20 ndipo linathandiza kwambiri abale chifukwa anakumana ndi mayesero m’chaka chotsatira.

^ ndime 4 Kwa zaka zambiri Ophunzira Baibulo ankavala kabaji kokhala ndi mtanda ndiponso chisoti chachifumu. Chizindikirochi chinkaikidwanso pa magazini a Nsanja ya Olonda. Koma pofika m’ma 1930, a Mboni za Yehova anasiya kugwiritsa ntchito chizindikirochi.