Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

DOMINICAN REPUBLIC

A Mboni za Yehova Amathandizana

A Mboni za Yehova Amathandizana

Sukulu Yatsopano Inathandiza Kwambiri

Yehova anadalitsa kwambiri atumiki ake pa ntchito imene ankagwira ku Dominican Republic. Mu 1994 kunali ofalitsa okwana 16,354 m’mipingo 259. Izi zinachititsa kuti pafunike akulu ndi atumiki othandiza oyenerera. Choncho Bungwe Lolamulira linavomereza kuti m’dzikoli mutsegulidwe Sukulu Yophunzitsa Utumiki imene panopa yalowedwa m’malo ndi Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu.

Pofika mu October 2011 panachitika makalasi 25 ndipo abale oposa 600 anamaliza maphunziro awo. Panopa, hafu ya anthu amene analowa sukuluyi ali mu utumiki wa nthawi zonse. Abale 71 ndi apainiya apadera ndipo 5 ndi oyang’anira madera. Makalasi 10 ankachitikira pa nthambi koma kenako sukuluyi inamangidwa ku Villa González ndipo maphunzirowa akhala akuchitikira kumeneko kuyambira kalasi nambala 11.

“A Mboni za Yehova Amathandizana”

Pa September 22, 1998, m’dziko la Dominican Republic munachitika chimphepo choopsa. Nyumba zambiri zinawonongeka ndipo anthu 300 anaphedwa. Nthawi yomweyo panakonzedwa komiti yopereka chithandizo imene inkagwira ntchito yake pa Nyumba ya Ufumu ya ku La Romana, ndipo komitiyi inkayang’aniridwa ndi komiti ya zomangamanga. Panali Akhristu okwana 300 amene anathandiza pa ntchitoyi ndipo 16 anali ochokera m’mayiko ena.

Abalewa anamanga kapena kukonza Nyumba za Ufumu zokwana 23 komanso nyumba za abale ndi alongo zokwana 800. Mlongo wina dzina lake Carmen anali mmodzi mwa anthu amene nyumba zawo zinawonongeka. Mlongoyu ndi mpainiya wokhazikika wachikulire ndipo anakhala m’nyumba yakeyo kwa zaka 38. Koma anasangalala kwambiri ataona abale 15 atabwera n’kuyamba kumumangira nyumba. Iye anati: “Yehova amatikumbukira nthawi zonse ndipo amatisamalira. Zoona abalewa akundimangira nyumba yokongola chonchi? Mpaka aneba anga anafika ponena kuti: ‘A Mboni za Yehova amathandizana ndipo amakondana kwambiri.’” Mawu ngati amenewa ankanenedwa m’madera osiyanasiyana amene abale ndi alongo anathandizidwa.

N’zoona kuti chimphepochi chinali choopsa koma zimene abale ndi alongo anachita pothandiza anzawo zinali zosaiwalika. Zinathandiza kuti moyo wawo ukhalenso wabwino ndiponso azitumikira Mulungu bwinobwino. Koma chofunika kwambiri n’chakuti zinathandiza anthu kulemekeza kwambiri Yehova amene amatitonthoza kwambiri.

Ntchito Yomanga Nyumba za Ufumu Inawonjezeka

Popeza Akhristu ankawonjezeka, pankafunika Nyumba za Ufumu zambiri. Ndiyeno mu November 2000, abale a ku Dominican Republic anayamba kumanga Nyumba za Ufumu mothandizidwa ndi pulogalamu yomanga nyumbazi m’mayiko osauka. Mipingo inkamaliza kumanga Nyumba ya Ufumu pa miyezi iwiri yokha. Pofika mu September 2011, magulu awiri omanga nyumbazi anamanga kapena kukonza Nyumba za Ufumu zokwana 145.

Ntchito yomangamangayi yathandiza kwambiri kuti anthu alemekeze Mulungu. Mwachitsanzo, m’katauni kena abale anapeza malo abwino kumangapo Nyumba ya Ufumu. Ndiyeno mpainiya wapadera anapita kukakambirana ndi mwini wa malowo kuti agule. Poyankha, munthuyo anati: “Mungotaya nthawi yanutu. Sindingayerekeze kukugulitsani. Bolanso mukananena zina chifukwa ine zatchalitchizo ndiye ayi.”

Atangosiyana naye, munthuyo anapita kukaona mchimwene wake ku Puerto Plata. Mchimwene wakeyo anali wa Mboni za Yehova ndipo atafika anapeza kuti akudwala ndipo akusungidwa m’nyumba ya wa Mboni za Yehova wina kumeneko ndipo akusamaliridwa bwino. Banja limene linkamusungalo linkapita naye kuchipatala, kumisonkhano ndiponso mu utumiki. Ndiyeno munthuyo anafunsa mchimwene wakeyo kuti: “Kodi akutchajani ndalama zingati pa zonse zimene akuchitiranizi?” Mchimwene wakeyo anati: “Sananditchaje kalikonse. Ndi abale angatu amenewa. Angondithandiza basi.”

“Ine sindinaonepo gulu la anthu ogwirizana chonchi.”

Atatero munthuyo anadabwa kwambiri moti anakakumana ndi mpainiya wapadera uja n’kumuuza kuti wasintha maganizo ndipo awalola kugula malowo. Abalewo anaguladi malowo n’kuyamba kumanga Nyumba ya Ufumu. Poyamba, mkazi wa munthuyo ankadananso ndi a Mboni za Yehova koma ataona mgwirizano wawo pomanga nyumbayo ananena kuti: “Ine sindinaonepo gulu la anthu ogwirizana chonchi.”