DOMINICAN REPUBLIC
Anthu 22 Anasiya Tchalitchi Chawo
GERMAN GOMERA anabadwa m’banja la ana 11 ndipo iye anali wa nambala 10. Bambo ake komanso achemwali ake awiri atamwalira, mayi ake dzina lawo a Luisa, anaganiza zosamukira kutauni ndipo anakalowa tchalichi chinachake.
German anati: “Mu 1962, m’tauniyo munafika banja lina limene linkachita upainiya wapadera ndipo anthu ankanena kuti zimene akaphunzitsa zinali za jabulosi komanso zosokoneza.” Apainiyawo atafika kunyumba yapafupi imene munkakhala banja la a Piña. Banjali linali lalikulu ndipo linawalandira bwino. Linachita chidwi poona kuti apainiyawo anali okoma mtima komanso ochezeka ndipo linamvetsera zonse zimene ananena. Izi zinachititsa kuti banja lonse la a Piña komanso achemwali anga atatu ayambe kuphunzira.
German anati: “Tsiku lina apainiya aja atafika kudzaphunzira ndi banja la a Piña, mayi anga anaitanidwa. Apainiyawo anawerenga malemba onena zoti tidzakhala ndi moyo wosatha padzikoli. Ndiyeno mayi anga anafunsa kuti: ‘Nanga n’chifukwa chiyani kutchalitchi chathu amanena kuti tidzapita kumwamba?’ M’baleyo anagwiritsa ntchito Baibulo
n’kuwayankha bwinobwino. Mayi angawo anasangalala kwambiri ndipo anayamba kuuza ena zimene anaphunzirazo.“Abusa atamva zoti anthu awo ayamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova, anafuna kuwaletsa. Anawakwiyira kwambiri ndiponso kuwaopseza. Ndiyeno mayi Maximina Piña anawayankha abusawo kuti, ‘Abusa! Inetu si mwana. Ndili ndi ufulu wosankha zochita.’
German anati: “Pamapeto pake, anthu 22 anasiya kupita kutchalitchicho n’kuyamba kusonkhana ndi Mboni za Yehova m’nyumba imene ankachita lendi. Mayi anga anabatizidwa mu 1965, ndipo patapita zaka 4 inenso ndinabatizidwa ndili ndi zaka 13.”