Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

DOMINICAN REPUBLIC

Ku Haiti Kunachitika Chivomezi

Ku Haiti Kunachitika Chivomezi

Zinthu Zikuyenda M’gawo la Chitchainizi

Mu 2005, ofesi ya nthambi inapempha M’bale Tin Wa Ng, kuti asiye kutumikira pa Beteli n’cholinga choti akachite upainiya wapadera. Izi zinachitika n’cholinga choti akalalikire kwa anthu a Chitchainizi amene anabwera m’dzikolo. M’baleyu anabadwira ku Dominican Republic n’kukulira komweko. Makolo ake anachokera ku China ndipo ankakhala ku Santo Domingo.

Pa January 1, 2008, mpingo wa Chitchainizi unakhazikitsidwa ku Santo Domingo ndipo mu 2011 kagulu kanakhazikitsidwa ku Santiago. M’gawo la Chitchainizi muli ofalitsa 70 ndipo 36 akuchita upaniya wokhazikika pomwe ena akuchita upainiya wothandiza. Pa mwezi, abale ndi alongowa amachititsa maphunziro a Baibulo okwana 76.

Kufufuza Anthu Olankhula Chingelezi

Pofika mu 2007, ku Dominican Republic kunali ofalitsa 27,466 m’mipingo 376 ndipo ankachititsa maphunziro a Baibulo okwana 49,795. Ngakhale kuti m’dzikoli munali anthu olankhula Chingelezi, munalibe mpingo wa chilankhulochi. Ndiyeno mu April 2008, ofesi ya nthambi inapempha M’bale Donald Elwell ndi mkazi wake Jayne kuti apite ku Santo Domingo kukayambitsa kagulu ka Chingelezi. Panali ofalitsa ochepa koma akhama amene anafufuza m’deralo kuti adziwe malo amene anthu olankhula Chingelezi amapezeka. Kenako anapeza gawo loti azilalikira.

Izi zinachititsa kuti anthu aziwonjezeka m’kaguluka moti mu 2009 mpingo wa anthu 39 unakhazikitsidwa. Zoterezi zinachitika m’madera osiyanasiyana a m’dzikoli ndipo pofika mu November 2011, panali mipingo 7 ya Chingelezi ndi kagulu kamodzi.

Mayi wa Chinenero Chamanja Akutsatira Mfundo za Yehova

Mpainiya wapadera akulankhula ndi Lorys Chinenero Chamanja chochita kugwira dzanja lenilenilo

M’dziko la Dominican Republic muli mayi wina dzina lake Lorys. Makolo ake anamwalira iye ali wamng’ono. Iye anabadwa ndi matenda amene anachititsa vuto la kumva ndipo ali ndi zaka 16 anayamba kuvutika kuona. Masana amaona pang’ono koma usiku saona ngakhale pang’ono. Kukada amafunika kugwira dzanja la munthu amene akulankhula kuti adziwe zimene akunena m’Chinenero Chamanja.

Ali ndi zaka 23, banja lina limene linkachita upainiya wapadera linamupeza. Pa nthawiyo anali atatengana ndi bambo wina wa vuto la kumvanso ndipo anali ndi mwana wamkazi wa chaka chimodzi wakumva bwinobwino. Lorys anavomera kupita ku Nyumba ya Ufumu ndipo anasangalala kwambiri ndi zimene anamva kumeneko.

Nthawi yomweyo anayamba kusintha moyo wake. Mwachitsanzo, atamva kuti anthu ayenera kukwatirana mwalamulo, iye anauza mwamuna wake kuti sangapitirize kukhala limodzi popanda kulembetsa ukwati. Ananena kuti sangalole kuchita zinthu zosemphana ndi mfundo za m’Baibulo. Mwamunayo ataona kuti mkazi wake akulankhula motsimikiza anavomera kukalembetsa.

Zitatero, Lorys anakhala wofalitsa wosabatizidwa ndipo pasanapite nthawi yaitali anabatizidwa. Mayiyu anachita mwayi wophunzira Chinenero Chamanja cha ku America ndipo amaphunzitsa mwana wake Baibulo komanso chinenerochi.

Ku Haiti Kunachitika Chivomezi Choopsa

Lachiwiri pa January 12, 2010, ndi tsiku losaiwalika kwa anthu a ku Dominican Republic ndi ku Haiti. Pa tsikuli ku Haiti kunachitika chivomezi choopsa. Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova linapempha nthambi ya ku Dominican Republic kuti itumize ndalama kunthambi ya ku Haiti zokathandizira anthu. Ndalama zake zinali zambiri ndipo abale anatuma m’bale Evan Batista kuti akapereke. M’baleyu ankagwira ntchito ya udokotala panthambipo, ndi wamtali pafupifupi mamita awiri ndipo amalemera makilogalamu 127.

Kunena zoona m’baleyu anali woyenera kupita kumeneku. Tikutero chifukwa chakuti atafika anauzidwa kuti kunkafunika thandizo la dokotala. Anthu ambiri amene anavulala modetsa nkhawa ankabweretsedwa pa Malo a Misonkhano pafupi ndi ofesi ya nthambi. Abale a ku Haiti atamva zoti M’bale Batista ndi dokotala, anapempha zoti akhale m’dzikolo kwa nthawi yaitali kuti azithandiza anthu. Nthambi ya ku Dominican Republic inavomera pempholi ndipo m’baleyu anathandiza Akhristu ambirimbiri amene anavulala. Izi zinachitika patangodutsa maola ochepa kuchokera pamene chivomezicho chinachitika.

Ku Haiti kutachitika chivomezi mu 2010, abale ambiri anapita kukathandiza

Nthawi yomweyo nthambi ya ku Dominican Republic inakonza zoti igule mpunga wokwana makilogalamu 6,800 komanso nyemba ndi zinthu zina n’kutumiza ku Haiti m’bandakucha wa Lachinayi pa January 14. Thandizo limeneli linali yoyamba kufika m’dzikoli kuchokera m’mayiko ena. Tsiku lomweli, madokotala ena atatu ochokera ku Dominican Republic anayenda ulendo wa maola 7 kupita kunthambi ya ku Haiti. Iwo atafika kunthambi sanafikire m’zipinda zawo koma anangopita kumalo amene kunali anthu ovulala n’kuyamba kuwathandiza mpaka pakati pa usiku. Tsiku lotsatira kunabwera madokotala 4 ndi manesi 4 ochokeranso ku Dominican Republic. Anayamba kuchita opaleshoni anthu ngakhale kuti malo ake sanali abwino. Pamene unkatha mlungu wotsatira, anthu 12 amenewa anathandiza anthu 300 ovulala.

Tsiku lililonse matenda akayakaya ankatumizidwa ku Dominican Republic. Nthawi zina galimoto yonyamula katundu wokapatsa anthu inkanyamulanso anthu odwala mwakayakaya kupita nawo kuzipatala zosiyanasiyana za ku Dominican Republic. Nthambi ya ku Dominican Republic inakonza zoti magulu a abale azikazonda odwala n’kumawalimbikitsa komanso kuonetsetsa kuti akulandira chithandizo chokwanira. Abale ndi alongo ankasunga achibale a anthu ovulala amene anabwera m’dzikolo kudzalandira chithandizo.

A Mboni za Yehova anapereka katundu wolemera makilogalamu pafupifupi 500,000 ndipo pa katunduyu panaliso chakudya chambiri

Zinthu zonse zimene anthu a Yehova anachita pothandiza anzawo pa nthawi yovutayi zinatsimikizira mawu a pa Miyambo 17:17, akuti: “Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse, ndipo bwenzilo ndi m’bale amene anabadwira kuti akuthandize pakagwa mavuto.” Kunena zoona pali zinthu zambirimbiri zimene zachitika zotsimikizira kuti Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake komanso atumiki ake pofuna kuthandiza anthu ake okhulupirika amene ali pa mavuto oopsa kwambiri. Abale ndi alongo ankalandira chithandizo mwakathithi kwa miyezi itatu. A Mboni za Yehova anapereka katundu wolemera makilogalamu pafupifupi 500,000 ndipo pa katunduyu panaliso chakudya chambiri. Abale ndi alongo okwana 78 ogwira ntchito zachipatala anafika ku Haiti kuchokera m’mayiko osiyanasiyana kuti athandize anthu ndipo ankagwira ntchito limodzi ndi anthu ena odzipereka. *

^ ndime 1 Kuti mumve zambiri pa nkhaniyi werengani Galamukani! ya December 2010 tsamba 14 mpaka 19.