Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

DOMINICAN REPUBLIC

“Sindidzasiya Kukhala wa Mboni za Yehova”

Ana María (Mary) Glass

“Sindidzasiya Kukhala wa Mboni za Yehova”
  • CHAKA CHOBADWA 1935

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1956

  • MBIRI YAKE Ali mtsikana, anali wakhama kutchalitchi chake cha Katolika. Koma ataphunzira Baibulo, ankazunzidwa ndi achibale ake, anthu a ku tchalitchi komanso boma ndipo ankapirira molimba mtima.

NDINALI wokonda kwambiri zopemphera ndipo ndinkachita zambiri m’tchalitchi changa cha Katolika. Ndinali wakwaya ndipo ndinkayenda ndi ansembe akamachita mwambo wa Misa kumalo osiyanasiyana. Kenako mu 1955, mkulu wanga anandiuza nkhani ya Paradaiso. Iye anandipatsa Baibulo, kabuku kakuti “This Good News of the Kingdom” ndiponso buku lakuti “Mulungu Akhale Woona.” Ndinasangalala kwambiri moti ndinafunsa wansembe ngati ndingawerenge Baibulo. Wansembeyo anandiuza kuti ndipenga nalo, koma ndinasankha kuti ndiliwerengebe.

Kenako ndinasamuka n’kumakakhala ndi agogo anga mumzinda wa Boca Chica. Wansembe wa kumeneko anandifunsa chifukwa chimene sindikupitira kutchalitchi. Ndinamufotokozera kuti zinthu zambiri zimene anthu amaphunzira ku tchalitchichi si za m’Baibulo. Wansembeyo anakwiya kwambiri n’kunena kuti: “Iwe mtsikana, sukudziwa kuti ndiwe nkhosa yanga yosochera?”

Koma ndinayankha kuti: “Ayi bambo. Nkhosatu ndi za Yehova, si za munthu ayi. Inuyo ndi amene mwasochera m’gulu la nkhosa za Yehova.”

Kungoyambira nthawi imeneyo, sindinapitenso kutchalitchi. Kenako ndinasamuka n’kumakakhala ndi mkulu wanga uja. Ndinabatizidwa patangopita miyezi 6 yokha kuchokera pa nthawi yoyamba imene ndinamva za Paradaiso. Nthawi yomweyo ndinayamba upainiya wokhazikika. Patangotha chaka chimodzi, ndinakwatiwa ndi m’bale wina dzina lake Enrique Glass ndipo pa nthawiyo anali woyang’anira dera. Tsiku lina tikulalikira kupaki mumzinda wa La Romana, apolisi anamanga Enrique. Apolisiwo atamutenga, ndinawathamangira n’kuwafunsa kuti: “Nanga ineyo mukundisiyiranji? Inensotu ndi wa Mboni za Yehova ndipo ndikulalikira.” Koma sanandimange.

Enrique anali atamangidwa pa nthawi zinanso m’mbuyomu moti nthawi yonse imene anakhala m’ndende inakwana zaka 7 ndi hafu. Pa nthawiyi anamulamula kuti akhale m’ndende miyezi 20. Ndinkapita kukamuona Lamlungu lililonse. Tsiku lina, woyang’anira ndende anandifunsa kuti: “Ukudzatani kuno?”

Ndinayankha kuti: “Mwamuna wanga ali m’ndende chifukwa choti ndi wa Mboni za Yehova.”

Iye anati: “Iwetu ndiwe mtsikana ndipo ungakhale ndi tsogolo labwino. Bwanji ukudzitayitsa nthawi ndi a Mboni za Yehova?”

Ndinayankha kuti: “Inenso ndi wa Mboni za Yehova. Olo mutandipha n’kundidzutsa, kundipha n’kundidzutsa mpaka maulendo 7, sindidzasiya kukhala wa Mboni za Yehova.” Nditatero anangondiuza kuti ndizipita.

Bani itachotsedwa, ine ndi Enrique tinagwira ntchito yoyang’anira dera ndi chigawo kwa zaka zambiri. Koma Enrique anatisiya pa March 8, 2008. Ineyo ndikupitiriza upainiya wokhazikika.