Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

DOMINICAN REPUBLIC

Mfundo Zachidule Zokhudza Dominican Republic

Mfundo Zachidule Zokhudza Dominican Republic

Mmene Dzikoli Lilili: Mbali yaikulu pachilumba cha Hispaniola ili m’dziko la Dominican Republic, ndipo mbali yotsalayo ili m’dziko la Haiti. M’dziko la Dominican Republic muli nkhalango, mapiri ataliatali, madambo komanso zipululu. Phiri lalitali kwambiri m’dzikoli ndi la Pico Duarte, ndipo ndi lalitali mamita 3,175. M’madera ambiri a m’mbali mwa nyanja muli mchenga woyera bwino. M’madera a mkatikati mwa dzikoli muli zigwa zachonde, monga chigwa chotchedwa Cibao.

Anthu: Anthu ambiri m’dzikoli ndi makaladi amene makolo awo anachokera ku Ulaya ndi ku Africa. M’dzikoli mulinso anthu a mitundu ina koma ambiri ndi ochokera ku Haiti.

Chilankhulo: Anthu ambiri m’dzikoli amalankhula Chisipanishi.

Abale ndi alongo akucheza

Ntchito Zawo: Chuma chambiri m’dzikoli chimachokera ku migodi, shuga, khofi ndiponso fodya. Koma chaposachedwapa, ndalama zambiri zikupezeka kuchokera ku ntchito zokopa alendo komanso ku makampani opanga zinthu zosiyanasiyana.

Nyengo: Nyengo ya m’dzikoli imakhala yabwino chifukwa nthawi zambiri kumatentha madigiri pafupifupi 25. Nayonso mvula imagwa bwino kwambiri. Chaka chilichonse, kumadera akumapiri kumagwa mvula yoposa mamilimita 2,032, koma kumadera ena imagwa mamilimita pafupifupi 760. Nthawi zina m’dzikoli mumachitika mphepo ndi mvula yamkuntho.

Chikhalidwe: M’dzikoli anthu amadalira mpunga, nyemba ndiponso ndiwo zamasamba. Anthu a m’dzikoli amakondanso nsomba, zipatso, tsabola ndiponso nthochi zophika. Zina mwa zakudya zimenezi amazisakaniza n’kuphika chakudya chimene anthu ambiri amakonda, chomwe amachitchula kuti La Bandera Dominicana (kutanthauza mbendera ya ku Dominican). Anthu a m’dzikoli amakondanso mpira, nyimbo ndiponso kuvina. Poimba, amakonda kugwiritsa ntchito gitala, ng’oma, zitoliro ndiponso mangolongondo.