DOMINICAN REPUBLIC
“Tidzawapeza”
“Tsiku Lina Tidzawapeza”
Cha mu 1935, munthu wina dzina lake Pablo González anayamba kuwerenga Baibulo kuchigwa chotchedwa Cibao. Poyamba ankapemphera ku tchalitchi chinachake koma anasiya ataona kuti zochita za anthu ake zinkasemphana ndi zimene iye anawerenga. Koma sanasiye kuphunzira Baibulo ndipo ankauza ena zimene waphunzira. Anayamba kuuza achibale ake ndi anthu ena apafupi kenako anthu a m’midzi yapafupi. Iye anagulitsa famu yake komanso ng’ombe zake kuti apeze ndalama zoyendera pokalalikira.
Pofika mu 1942, Pablo ankaphunzitsa mabanja oposa 200 ndiponso ankachititsa misonkhano. Ankachita zimenezi ngakhale kuti anali asanakumane ndi Mboni za Yehova. Iye ankalimbikitsa anthu kuphunzira Baibulo komanso kutsatira mfundo zake. Ambiri ankatsatira zimene ankaphunzira moti anasiya fodya komanso mitala.
Munthu wina amene anamva uthenga umene Pablo ankalalikira anali Celeste Rosario. Iye anati: “Pamene
ndinali ndi zaka 17, msuweni wa mayi anga, dzina lake Negro Jiménez anali m’gulu limene linkatsogoleredwa ndi Pablo González. Ndiyeno Negro atafika kwathu anatiwerengera mavesi a m’Baibulo. Zomwe anatiwerengerazo zinandichititsa kutuluka mu tchalitchi cha Katolika. Ku tchalitchichi ankatiwerengera mawu m’chilankhulo cha Chilatini ndiye sitinkamva chilichonse. Pasanapite nthawi yaitali, Pablo González anabwera kudzatilimbikitsa. Iye anati: ‘Ife sitili m’chipembedzo chilichonse koma tikudziwa kuti tili ndi abale athu padziko lonse. Panopa sitikuwadziwa ndipo sitikudziwanso dzina lawo. Koma tsiku lina tidzawapeza.’”Pablo anayambitsa magulu ophunzira Baibulo ku Los Cacaos Salcedo, ku Monte Adentro, ku Salcedo ndiponso ku Villa Tenares. Mu 1948, iye anaima ku Santiago kuti akwere basi ina. Ali kumeneku, anaona a Mboni akulalikira mumsewu ndipo anamupatsa Nsanja ya Olonda. Pa ulendo wina, anapatsidwa mabuku awiri ndi mlongo wina. Mlongoyu anamuitaniranso ku
mwambo wokumbukira imfa ya Khristu ku Santiago. Pa mwambowu, Pablo anasangalala kwambiri ndi zimene anamva. Iye anazindikira kuti wapeza abale ake amene ankawafuna kwa nthawi yaitali aja.Amishane ankapita kukaona anthu amene ankaphunzitsidwa ndi Pablo. Atafika kwina anapeza anthu 27 akuwadikira. Anthu ena anali atayenda makilomita 25 wapansi ndipo ena anayenda makilomita 50 pa mahatchi. Pamalo ena anapeza anthu 78 ndipo pena anapeza anthu 69.
Pablo anapereka mayina a anthu 150 kwa amishonalewo kuti aziphunzira nawo. Anthuwo anali atayamba kale kuphunzira Baibulo ndiponso kutsatira mfundo zake. Koma ankangofunika kuwapatsa malangizo komanso kutsogoleredwa ndi gulu. Celeste Rosario anati: “Amishonale atafika tinachita msonkhano ndipo panakonzedwa zoti anthu abatizidwe. Woyamba kubatizidwa ndinali ineyo kenako mayi anga a Fidelia Jiménez, ndi mchemwali wanga dzina lake Carmen.”
Msonkhano wadera woyamba m’dzikoli unachitika pa September 23 mpaka pa 25, 1949, ku Santiago. Msonkhanowu unalimbikitsa kwambiri ntchito yolalikira. Pamsonkhanowu panafika anthu ambiri moti Lamlungu kunabwera anthu 260 kudzamvetsera nkhani ya onse. Anthu 28 anabatizidwa ndipo msonkhanowu unathandiza anthu ambiri kudziwa kuti gulu la Yehova ndi lomweli.